MkwasoUncategorized

FISCHER WATSOPANO

Wolemba: Precious MSOSA

Mnyamata wosewera mu timu ya Nyasa Big Bullets, yemwenso ndi mmodzi mwa anthu omwe akufuna kudzapikisana nawo pa mpando wa phungu wa Nyumba ya Malamulo m’dera la ku- mmawa kwa mzinda wa Blantyre, Fis- cher Kondowe wati ndiwokonzeka kudzameta zingongo zake akadzapam- bana pa chisankho cha chaka cha mawa.

Fischer, yemwe ndi wa chipe- mbedzo cha chi Rasta amayankhapo mtolankhaniyu atamufunsa maganizo ake ngati iye ndiwokonzeka kudzameta tsitsi lake akadzapambana potengera kuti Nyumba ya Malamulo siimalola phungu wammwamuna kusungira zi- ngongo.

Iye anati pachipembedzo sizimatengera kavalidwe kapena maone- kedwe aliwonse koma mtima wa munthu.

“Chipembedzo ndi mtima wa munthu kotero nditadzameta sindi- kukhulupirira kuti zitha kudza- ndisintha chilichonse. Pandekha ndizidzazidziwa pomwe ndikuyima,” anatero Fischer.

Anthu ambiri a chipembedzochi amakhulupirira kusunga madiredi ngakhale kuti malamulo ake saletsa munthu kusakhala ndi tsitsi la mtunduwu.

Katswiriyu, yemwe ndi mkhalakale mmodzi yemwe akukankhabe chikopa, ankafunanso kuyimira pa mpandowu mu chisankho chapatatu m’chaka cha 2014 m’dera lomweli koma adakanika chifukwa choti anali asadalembetse mu kaundula wa mavoti.

Poyankhapo pa za makonze- keredwe ake, Fischer yemwe wakhala akusunga madirediwa kwa zaka pa- fupifupi makumi awiri, anati chili- chonse chili m’chimake koma sanayambe kutakata chifukwa bungwe loyang’anira chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) silina- tsegulire zipata za misonkhano yokopa anthu.

Popitilira kuyankhulapo pa za chisankho chikubwerachi, iye anati adakali ndi malingaliro odzayimira payekha popanda chipani. Koma Fi- scher anati ngati pali chipani chomwe chidzafune kuti adzachiyimire, iye ndi- wokonzeka kudzatero.

“Koma ndidzaonesetsa kuti chipanicho chilidi ndi khumbo lofuna kutukula dera lathu chifukwa tanamizidwa nthawi yayitali,” iye anatero.

Koma malipoti a manyuzipepala ati katswiriyu akufuna kudzaima pa tikiti ya chipani cha Malawi Congress (MCP).

Kupatula a chambakale pa nkhani ya ndale omwe akudzalimbirana u- phungu wa derali, Fischer akuyembekezeka kudzalimbirana mpandowu ndi namandwa komanso kaputeni wa kale wa timu ya Flames Peter Mponda.

6 thoughts on “FISCHER WATSOPANO

  • Thank you for sharing this article with me. It helped me a lot and I love it.

  • I enjoyed reading your piece and it provided me with a lot of value.

  • I really appreciate your help

  • Thank you for your articles. They are very helpful to me. May I ask you a question?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *