Dayosizi ya Mangochi yakhazikitsa maparishi ang’onoang’ono

Ambuye Stima: M’menemo muzichitika Misa zikuluzikulu

Wolemba: Thokozani CHAPOLA, Mtolankhani Wapadera

Episkopi wa dayosizi ya Mangochi Ambuye Montfort Stima, akhazikitsa tchalitchi zisanu ndi chimodzi za mu dayosiziyi kukhala maparishi ang’onoang’ono.

Ambuye Stima adalengeza izi posachedwapa ku parishi ya St. Louis Montfort ku Balaka pamwambo wa Chibalalitso cha Mpingo.

Matchalitchiwa ndi a Kanono imene ndi nthambi ya parishi ya Phalula, Chiyendausiku (Balaka parishi), Phimbi (Utale 1 parishi), Mpilisi (Utale 2 parishi), Mase (Mangochi parishi) komanso tchalitchi la Mkwepere (Mpiri parishi).

Ambuye Stima ati zimenezi zachitika kutsatira kukula kwa mpingo mu dayosiziyi ndipo ati apereka ndondo-meko zoti tchalitchizi zikakwaniritsa zikwezedwe kukhala maparishi akuluakulu.

“Adzipikisana okhaokha ndipo potengera yomwe ikuchita bwino, imeneyo idzikwezedwa kukhala parishi choncho akuyenera alimbikire koposa. Ndidzilandira malipoti a momwe akuchitira pa kaperekedwe ka cham’mbale ndi masika, mmene akuperekera mtulo komanso mmene akulandilira masakramenti osiyanasiyana,” anatero Ambuye Stima.

Ambuye Stima anapitiriza kuti: “M’menemu mudzichitika Misa zikuluzikulu monga za Kanjedza, Lachisanu Loyera, Pasaka, Khirisimasi ndi miyambo ina ikuluikulu. Akhristu azithanso kumangirako maukwati, Ulimbitso ndi masakramenti ena onse.”

Bambomfumu a parishi ya Balaka, Bambo Louis Mkukumira anati zimenezi zithandiza kuti anthu a mu parishiyo maka ozungulira tchalitchi la Chiyendausiku adzilandira masakramenti mosavuta.

“Ntchito yopereka masakramenti ipepuka chifukwa zambiri zidzichitikira ku parishi yaying’ono ya Chiyendausiku kusiyana ndi kuti onse azidzadzana kuno monga amachitira kale,” anatero Bambo Mkukumira.