ASACHOKE: Ochemerera Wanderers akufuna Mkandawire

Analengeza kuti sakufuna kuimanso – Mkandawire

Wolemba: Victor SINGANO Junior, Mtolankhani Wapadera

Komiti ya ochemerera timu ya Be Forward Wanderers yabwera poyera kutsindika kuti siikufuna nkhope yatsopano pa udindo wa wapampando woyendetsa timuyi ndipo yati ikufunitsitsa yemwe alipo kale pa udindowu Gift Mkandawire apitirizebe.

Timu ya Wanderers, yomwe inamaliza osapeza chikho chilichonse chaka chatha ikuyembeke-zereka kuchititsa chisankho cha komiti yake yaikulu komanso ya ochemerera posachedwapa.

Sabata zingapo zapitazo wapampando wamkulu wa timuyi, Mkandawire, analengeza kuti alibe chidwi choimanso pachisankhochi. Mmalo mwake, iye anapempha kuti pabwere anthu ena kuti atsogolere timuyi.

Koma nkhaniyi siinakondwe-retse akuluakulu akomiti ya ochemerera timu ya Wanderers ndipo anati ndi nkhani yosayenera kuimva potengera ntchito yayikulu yomwe ati wapampandoyu wakhala akuigwira ku timuyi.

Poyankhula ndi Mkwaso wapampando wa komiti ya ochemerera, Mervin Nkunika, anati a Mkandawire ndi munthu yekhayo yemwe anachilimika ku timuyi kuyerekeza ndi wina aliyense ndipo ati ndi yekhayonso amene akuyenera kutsalira osati anthu ena omwe amagwira nawo ntchito ayi.

“Panopa a Mkandawire sanatipeze ndi kutipatsa chikalata chotsimikiza zakusiya kwawo. Zambiri tikumangozimvera m’mawayilesi ndi nyuzipepala koma ngati gulu la ochemerera tatemetsa nkhwangwa pamwala kuti akatifikira tiwapempha kuti asachoke chifukwa iwo si olephera ndipo ndi munthu yekhayo amene ali ndi mtima wa mpira.

Be Forward Wanderers: Otsatira timuyi akuti pasakhale kusintha pa maudindo ena

“Panopa akuoneka ngati olephera koma si choncho ayi. Mavuto onse omwe timu yakhala ikukumana nawo anabwera chifukwa amnzawo omwe anali nawo m’maudindo amalephera kugwirana nawo manja ndipo mmalo mwake maso awo amayika pofuna kubera timuyi,” anatero Nkunika.

Anapitiriza kuti: “Nditsindike pano kuti onse amene anali mu komiti yayikulu sitikuwafunanso ndipo amene tikhale nawo ndi a Mkandawire ndipo tiwabweretsera anthu omwe akhale odzipereka ngati mmene amachitira.”

Pakadalipano Nkunika wati salola munthu aliyense yemwe alibe mbiri ya mpira kudzasankhindwa pampando uliwonse koma okhawo omwe ndi achidwi chenicheni ndi chikondi cha timuyi.

“Sitikufuna munthu amene sangabweretse kusintha kulikonse koma weniweni wofunira zabwino timu ya Wanderers chifukwa tatopa ndi anthu ongofuna mpando kuti adziwike chabe ku mtundu wa Malawi,” anafotokoza Nkunika.

Mkandawire anakhala wapa-mpando wa timu ya Wanderers kutsatira imfa ya George Chamangwana yemwe anali wapampando wa timuyi.