Kamlepo wati sazidzudzula chisawawa

Kamlepo: Akuti chitukuko chayamba kufika ku dera lake

Wolemba: Bartholomew BOAZ

Phungu wa dera la kumvuma kwa boma la Rumphi a Kamlepo Kalua wati sadzingodzudzula chipani cha Democratic Progressive (DPP) chisawawa koma adzitero pokhapo poyenera kutero.

A Kalua ndi m’modzi mwa andale amene akhala akulidzudzula boma la DPP pankhani zosi-yanasiyana. Koma posachedwapa, iwo adzidzimutsa anthu a-mbiri pamene anena kuti akuyenera kukhala pambuyo pa boma “pobweretsa chitukuko”.

“Ndakhala mbali yotsutsa kwa zaka zambirimbiri. Tsopano tikuyenera kuthandiza boma pa ntchito zimene likugwira pobweretsa chitukuko ku madera athu. Ndikuyenera kukhala nkhope ya dera langa ndipo tsopano nthawi yakwana yoti ndisamangodzudzula wamba,” anatero a Kalua.

Iwo anapitiriza kuti: “Ndikuchita zimenezi chifukwa cha anthu anga kuti apeze zimene akhala akuzisowa kwanthawi yayitali kuti zichitike kuno.”

A Kalua anayamikira mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika chifukwa cha chitukuko chimene ati abweretsa kudera lawo monga magetsi ndi thalansimita yothandiza kuti deralo kuzikhala netiweki ya lamya za m’manja maka ku Tchalo.

“Anthu a ku wodi ya Tchalo samatha kuimba foni chifukwa cha vuto la netiweki. Tsopano thilansimita ya foni yabwera. Posachedwapa kudera kuno kukhala magetsi ndipo chimanga chigawidwa monga momwe adalonjezera a Pulezidenti. Ndili ndi chikhulupiriro kuti msewu wa Chiweta-Mlowe ukonzedwa posachedwapa,” iwo anaonjezera.