‘Ndikuyamba kuimba sindinkalimbana ndi ndalama’

Lulu: Chomwe ndinkafuna ndi kupeza mwayi woti ndidziwike

Wolemba: Bartholomew BOAZ

Katswiri wokanyanga nsambo Lulu wapempha oimba amene akutumphuka kumene kuti asamaike mtima pa ndalama koma kupititsa patsogolo luso lawo.

Lulu, yemwe dzina lake lenileni ndi Lawrence Khwisa, wati oimbawa akaitanidwa kukaimba limodzi ndi amkhalakale, adzitenga mwayi           umenewu ngati wolimbikitsira luso lawo.

“Ndikungoyamba kumene kui-mba, sindimaika chidwi pa ndalama. Ndinkadziwa kuti ndinali wosatchuka motero chomwe ndimafuna ndichoti ndingopeza mwayi woti ndidziwike,” anatero Lulu pouza Malawi News Agency.

Lulu anaonjezera kuti: “China chimene chimakhala m’mutu mwanga ndichoti sindinkalibweretsa gulu lovinalo ndi ine ayi.

Motero, chomwe ndinkafuna ndikuimba koti ndikope mitima ya anthu kuti mtsogolo adzakhale ndi chidwi chobwera ku madansi anga.”

Oimba ongoyamba kumene akhala akumadandaula kuti sakumapatsidwa ndalama akaitanidwa kukhala akalambulabwalo ndi oimba okhazikika.

Koma Lulu wati kukhala woimba wotumphuka kumene kuli ngati kukhala mwana wa sukulu motero ndi anthu ochepa amalipidwa chifukwa choti akuphunzira.

Iye wati asanatchuke adakhala akuimba kwa zaka zosawerengeka popanda kulandira khobidi.

“Ndikukumbukira panali nthawi yomwe anthu ankandinyoza kuti ndaimba nthawi yayitali koma ndidakayendabe pansi,” anatero.