MkwasoUncategorized

Cadecom ipempha kampani zidzitenga mbali pakusintha kwa nyengo

Marin (kumanzere): Makampani omwe siaboma ali ndi udindo otengapo mbali

Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA

Bungwe la Mpingo wa Katolika loona zachitukuko la Catholic Development Commission of Malawi (Cadecom) lapempha kampani kuti zidzitenga nawo mbali kuzindikiritsa anthu omwe ama-gwira nawo ntchito mmene angathanirane ndi mavuto odza kaamba kakusintha kwanyengo.

Mmodzi mwa akuluakulu a bungweli a Mercy Chirambo anayankhula izi m’boma la Balaka pa mkumano womwe bungweli linachititsa ndi kampani za Limbe Leaf, Central East African Railways ndi Malawi Cotton.

Iwo anati kampanizi zilipo zambiri ndipo zili ndi kuthekera kote-ngapo mbali pa nkhani yakusintha kwanyengo pobwezeretsa chilengedwe.

A Chirambo anati kampanizi zitha kulimbikitsa madera omwe zikugwirako ntchito kufalitsa uthenga wamomwe anthu angapewere mavuto odza kaamba kakusintha kwanyengo komanso zomwe angachite kuti apulumuke ku zipsinjo zomwe zilipo kaamba ka vutoli.

“Kampanizi zili ndikuthekera kolimbikitsa ntchito yodzala mitengo komwe zikugwira ntchito komanso pakhale mgwirizano wa mmene angathanirane ndi mavutowa,” anatero a Chirambo.

A Chirambo anati zawonetsa kuti ngakhale kampanizi zikulimbikitsa mmene anthu angathanirane ndi mavuto akusintha kwa nyengo, madera ena komwe ziku-gwirako ntchito zikulephera kukwa-niritsa udindo wawo wobwezeretsa chilengedwe.

Mkulu woona ntchito ku ka-mpani yogaya thonje ya Malawi Cotton, a Martin Zhu, anati mkumanowu wawathandiza kudziwa zomwe akuyenera kuchita kumbali ya mmene angapewere zinthu zomwe zingawononge chilengedwe komanso mmene angathandizire madera omwe akugwirako ntchito polimbikitsa kubwezeretsa chile-ngedwe ndi zina.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *