Ken-C wakumana ndi Macelba mu ‘Mpata’

Wolemba: Bartholomew BOAZ

Mnyamata amene wangotumphuka pa nkhani zoimba Ken-C wati adzakhala wokondwa kwambiri ngati nyimbo za oimba a m’dziko muno zitamakondedwa ku maiko ambiri.

Ken-C, yemwe dzina lake lenileni ndi Kenneth Chikwangwala ndipo amakhala ku Zomba, watulutsa nyimbo yake yachisanu yotchedwa ‘Mpata’ imene waimba ndi woimba wodziwika, Macelba.

Ken-C: Nyimbo zathu zidzikondedwa kunja

“Ndikufuna kuti nyimbo zathu zidzikondedwa ndi anthu ngakhale a ku maiko ena n’chifukwa chake kwambiri ndikufuna ndiziimba nyimbo mu chamba chachikhalidwe chathu,” anatero Ken-C.

Iye anati ‘Mpata’ ndi nyimbo ya chikondi yomwe ikukamba zoti zingavute motani samusiya mkaziyo mpaka atamupatsa mpata woti amukonde. Iyi ndi nyimbo yachisanu chiyambireni kuimba chifukwa watulutsapo nyimbo zina monga ‘Mwananga Samala’, ‘Chonde Usapite (Nagama)’, ‘Mudzatipeza’ ndi ‘Chiphadzuwa’.

Nyimbo ya ‘Mpata’ yajambulidwa ndi DJ Sley. Ndipo zina mwa nyimbo zomwe adajambulazi zikuonetsedwa kale mu wailesi za kanema komanso kuimba mu wailesi zambiri za m’dziko muno.

Komai ye wati zamudyera ndalama zambiri kuti atulutse nyimboyi “koma ndine wokondwa kuti zatheka. Ndikuganiza zotulutsa chimbale changa choyamba chaka cha mawa,” watero Ken-C.