Media Council iyambanso mwatsopano

Wolemba: Joseph KAYIRA

Bungwe la atolankhani la Media Council of Malawi (MCM), mwa zina, limaonetsetsa kuti atolankhani akugwira ntchito mosafinyika. Bungweli limaonesetsanso kuti atolankhani akugwira ntchito yawo mwaukadaulo ndi motsata malamulo amene anakhazikitsidwa mogwirizana ndi ulamuliro wa demokalase. Kwa kanthawi bungweli linakhala ngati laima kaamba ka zifukwa zina, koma pano layambanso ntchito zake.

A Moses Kaufa ndi omwe ale-mbedwa ngati mkulu woyendetsa ntchito za bungweli. Mkwaso unacheza ndi a Kaufa kuti alongosole masomphenya awo pa momwe ayendetsere bungweli.

Mkulku wa MCM a Kaufa

Poyamba ndikufunireni zabwino chifukwa cholembedwa ntchito ngati mkulu wa bungwe la Media Council.

Zikomo kwambiri.

Fotokozani za mbiri yanu.

Kwa zaka khumi, zisanu ndi zitatu ndakhala ndikugwira ntchito ya utolankhani. Ndagwirako ku nyumba zosindikiza nkhani komanso zoulutsa mawu komanso ku wailesi ya kanema. Ndagwirakonso ku mabungwe omwe si aboma. Mwachidule, ndakhala ndikutumikira m’malo osiyanasiyana.

Ku nkhani ya maphunziro ndili ndi mapepala okhudza zautolankhani angapo kuphatikizapo digiri ya Mass Communications komanso pakali pano ndikumalizitsa maphunziro a Masters Degree in Strategic Planning.

Ukadaulo wanu ndi wotani pa nkhani yoyang’anira atolankhani?

Ndagwira ntchito ku mabungwe ndi makampani ambiri amene amasindikiza ndi kufalitsa nkhani. Konseko ndinali ndi mwayi wogwira ntchito m’mipando ikuluikulu. Cho-ncho nkhani yoyang’anira atolankhani kapena anthu ena si yachilendo. Kwa ine kukhala mkulu wa bungwe la Media Council ndikungopitiriza ntchito yomwe ndakhala ndikugwira ku mabungwe ndi makampani ena aja. Ndili ndi chikhulupiriro kuti kuyamba mwatsopano kumene kukuchitika ku Media Council kupindulira ntchito ya utolankhani kuno ku Malawi.

Mukuona kwanu, mungalongosole bwanji za ufulu wa atolankhani kuno ku Malawi?

Ufulu wa ntchito ya utolankhani ulipo m’dziko muno. Komanso tinene mosabisa kuti atolankhani akuyesetsa kugwira ntchito yawo mwaukadaulo. Ambiri ali ndi maphunziro abwino okhudza nkhani ya utolankhani ndipo amatsatira bwino malamulo a ntchito yawo.

Vuto limene lilipo ndi loti pena ndi pena atolankhani amatha kuopsezedwa mkatikati mogwira ntchito yawo. Pena eni wake a manyuzipepala, wailesi ndi mabungwe ena ofalitsa nkhani amatha kuopseza atolankhani kuti asalembe nkhani mwachilungamo kaamba koti nkhaniyo mwina ikukhudza munthu wina wamkulu kapena wodziwana naye.

Choncho atolankhani amatha kukakamizidwa kusalemba nkhani chifukwa mwini nyuzipepala waona kuti iwonongetsa ubale ndi ena ake. Kukakhala ku nyumba zosindikiza ndi kuulutsa nkhani koma za boma – kumenekonso atolankhani ama-kakamizidwa kulemba nkhani zoko-mera okhawo amene akulamula pa nthawiyo. Andale amakhala ndi mphamvu zouza atolankhani zoyenera kulemba zomwe ndi zosemphana ndi malamulo a utolankhani.

Lamulo la Access To Information (ATI), lomwe likupereka mwai kwa Amalawi kufunsa kapena kupeza mayankho pa zinthu zomwe akufuna kudziwa lakakamira m’maofesi ena ku bomaku. Mutani kuti izi ziyende msanga pokhala kuti zatenga nthawi?

Mukakumbuka bwino a Media Council of Malawi, mogwirizana ndi mabungwe ena, anagwira ntchito yaikulu yokhazikitsa lamuloli. Malamulo a dziko lino akunena momveka bwino kufunika kokhala ndi lamulo lotereli. Ena amaganiza kuti ndi lamulo lothandiza atolankhani okha koma si choncho. Lamuloli ndi lothandiza aliyense. Amalawi ali ndi ufulu wofunsa ku boma ndi kwina kulikonse pa zomwe akufuna kudziwa.

Choncho ife talumikizana kale ndi a mbali ya boma – makamaka unduna wofalitsa nkhani kuti ndondomeko zimene zaikidwa zitsatidwe mwamsanga kuti lamuloli liyambe kugwira ntchito. Pali ena amene tikugwira nawo ntchito kuti izi ziyende mwachangu monga a Media Institute of Southern Africa (MISA) Malawi, Malawi Communications Regulatory Authortiy (MACRA) komanso komiti ya Nyumba ya Malaulo yowona zofalitsa nkhani.

Media Council yakhala isakugwira ntchito kwa nthawi. Mutani kuti anthu alidziwe bungweli ndi kulumikizana nalo?

Ndi zoona kuti bungweli linakhala ngati laima kwa kanthawi. Panali zovuta zina zimene linakumana nazo monga mavuto azachuma. Kudzera mukufuna kwabwino kwa eni nyumba zoulutsa ndi kusindikiza nkhani, Media Council yadzutsidwanso. Mavuto azachuma adakalipo. Pakali pano Media Council ikukhazikitsa ndondomeko zoyendetsera bungweli. Zinthu zingapo zikuyenera kusintha kuti bungweli lipite patsogolo.       Malamulo ena adzayenera kukonzedwa. Tikuyeneranso ku-khazikitsa ndondomeko zopezera ndalama zoyendetsera bungweli.

Tayenderako kale nyumba zina zoulutsa ndi kusindikiza nkhani. Media Council ikufuna kuti ubale wake ndi nyumbazi komanso atolankhani ukhale wabwino; wopi-ndulira tonse. Tikhala tikufikira nyumba zonse komanso kulengezetsa ntchito zathu. Tikufuna aliyense adziwe kufunika kwa bungweli. Bungweli ndi limene liri ndi udindo wowonesetsa kuti ntchito zautolankhani zikuyenda motsata malamulo. Bungweli ndi limene limapereka ziphaso zogwirira ntchito ya utolankhani kuno ku Malawi.

M’maiko ena ntchitoyi imakhala m’manja mwa boma koma kuno tinagwirizana kuti Media Council ndi imene ikuyenera kuonesetsa kuti utolankhani ukuchitika motsata malamulo. Ubwino wokhala ndi bungwe lomwe si laboma kutsata zomwe atolankhani akuchita ndi woti kumakhala kosavuta kudzudzula zolakwika.

Akakhala aboma kuti ndi amene apatsidwa ntchitoyi, taona m’maiko ambiri akutseka nyumba zoulutsa ndi kusindikiza nkhani. Tikulimbikitsa ndondomeko yoti Media Council ikhale ndi mphamvu zopereka chilango, kapena kuweruza milandu imene imabwera anthu akakhala ndi dandaulo ndi nyumba zoulutsa kapena kusindikiza nkhani.

Bungweli ndi lofunika bwanji kuno ku Malawi?

Ndi bungwe limene limaonetsetsa kuti amene ali m’boma kapena kuti ali ndi mphamvu asamasokoneze ntchito zautolankhani. M’maiko ambiri m’mene boma linatenga udindo woyang’anira ntchito yautolankhani, zinthu sizikuyenda bwino chifukwa boma limatha kupanikiza ndi kufinya atolankhani. Boma limatha kutseka nyumba zosindikiza ndi kuulutsa nkhani. Atolankhani amatha kumangidwa ndi kuponyedwa m’ndende chifukwa chokwanitsa kugwira ntchito yawo. Kuno tikuti zimenezi ayi. Media Council ikhale ndi udindo woonesetsa kuti atolankhani akugwira bwino ntchito yawo.

Media Council iwonesetsa kuti pamene palakwika anthu akhale pansi nkukambirana. Zikavutitsitsa ndi pamene anthu angapite ku khoti.

Tikufuna pakhale ubale wabwino pakati pa atolankhani ndi anthu komanso pakati pa atolankhani ndi boma. Kwakukulu, tikufuna ulamuliro wa demokalase udziyenda bwino ndipo nyumba zosindikiza ndi kuulutsa nkhani zithandize kudzamitsa ulamulirowu.

Zikuoneka ngati Media Council ilibe chikoka pakati pa atolankhani?

Ndi bungwe lomwe langodzutsidwa kumene ndipo nkofunika kuti tigwirane manja kuti likhazikike. Chikokacho chingabwere pokhapokha tonse tikadziwa komanso kulimbikitsa zolinga za Media Council. Ndikudziwa kuti pali ambiri omwe akufunsa mafunso monga: ndingapindulenji ngati membala? Media Council ndiyofunika bwanji?

Kaufa: Tiyeni tiyendere limodzi

Ndinene kuti Media Council ndi bungwe lofunika kwambiri chifukwa limathandiza kuti utolankhani upite patsogolo. M’dziko limene ato-lankhani amaponderezedwa demokalase ndi chitukuko siziyenda bwino. Choncho atolankhani akuye-nera kukhala patsogolo kuwonesetsa kuti bungweli lilipo nthawi zonse. Madotolo ali ndi bungwe lawo monga lomweli; maloya ali ndi bungwe lawonso. Mabungwewa amaonesetsa kuti ndondomeko ndi malamulo a ntchitozi akutsatidwa.

Atolankhaninso amayenera ku-khala ndi chiphaso chochokera ku Media Council kuti agwire ntchito yawo. M’mbuyomu tinachitapo zimenezi ndipo tichitanso ulendo uno. Atolankhani ayenera kuchitapo kanthu kuti lisafe.

Mwakonzanji kuti Media Council idzame?

Pali zambiri. Tikhala ndi maphu-nziro pa ntchito yautolakhani. Tilumi-kizana ndi mabungwe osiyanasiyana kuti atolankhani apeze mwai wamaphunziro mommuno komanso kunja. Tithandiza nyumba zoulutsa ndi kusindikiza nkhani pophunzitsa atolankhani ndi anthu ogwira ntchito m’nyumbazi pa ukadaulo wosi-yanasiyana monga kulemba nkhani za demokalase, bizinesi ndi chuma, chisankho, zaumoyo, zamaphunziro ndi zina zambiri.

Tikhazikitsa nthambi yomwe ikhale ikusakasaka ndalama kuti bungweli lisafe. Tikukonza zokhala ndi mapulojekiti osiyanasiyana ndi mabungwe omwe si aboma kuti Media Council ikhale yodziimira payokha. Kukwaniritsa izi kutengera ubale wabwino pakati pa Media Council, nyumba zosindikiza ndi kuulutsa nkhani komanso atolankhani eni ake.

Kodi atolankhani m’dziko muno akugwira ntchito motsata malamulo?

Akuyesera ndithu. Chimene chimadzasokoneza ndi malamulo antchito mu nyumba zosiyanasiyana zoulutsa ndi kusindikiza nkhani. Malamulo ena m’nyumbazi amafinya atolankhani ndipo amalephera kugwira bwino ntchito yawo.

Mwa chitsanzo, atolankhani amapezeka kuti sakupatsidwa zipangizo zokwanira pa ntchito yawo. Penanso amalandira ndalama zochepa zomwe zimapereka mpata kwa anthu ena nkumawapatsa ziphuphu kuti mwina asalembe zolakwika zomwe zikuchitika monga nkhani zokhudza katangale. Ulemba bwanji nkhani utapatsidwa ndalama ndi anthu omwe umafuna kuti uwabweretse pa mbalambanda kuti akuchita zolakwika?

Ku nyumba zoulutsa mawu za boma, kumakhala kovuta kuti alembe zoipa zimene zikuchitika m’boma kapena zomwe akuluakulu a m’boma akuchita. Andalewa amatha kuopseza atolankhani kuti asalembe chilichonse chokhudza boma kapena chipani cholamula.

Atolankhani ophwanya malamulo mudzachita nawo chiyani?

Tili ndi malamulo amene atolankhani akuyenera kutsata pa ntchito yawo. Tili nako kabukhu kamene kamalongosola bwino za malamulowa komwe pa chingerezi timati Code of Conduct and Ethics. Nyumba zosindikiza ndi kuulutsa mawu zilinso ndi malamulo awo amene atolankhani amatsatira.

Tikamanena kuti atolankhani akuyenera kukhala ndi ziphaso zochokera ku Media Council timafuna kuti tidzitha kutsatira bwino m’mene akugwirira ntchito komanso m’mene akuonetsera khalidwe lawo akamakafufuza nkhani. Kumakhala kosavuta kufikira amene akuonetsa khalidwe losemphana ndi malamulo a utolankhani.

Onse opezeka kuti akuphwanya malamulo autolankhani amaitanidwa ndi kulangizidwa ndi komiti imene imamva madandaulo komanso kuli-mbikitsa kagwiridwe kabwino ka ntchito yautolankhani.

Mukuwona bwanji ubale wa atolankhani ndi boma?

Ubale wathu uli bwino. Boma limaitana atolankhani ku misonkhano yosiyanasiyana zomwe zikuonetsa kuti liri ndi chikhulupiriro kuti uthenga umene limapereka ukafikira anthu. Pena zinthu zimakhala ngati zikukhota koma tikuyamika kuti kwakukulu zinthu zakhala zikuyenda bwino.

Chofunika ndi kungolimbikitsa kuti ubalewu uzame ndipo pasamakhale kukayikirana pakati pa boma ndi atolankhani. Si ife adani. Tikuyenera kuyendera limodzi kuti titukule Malawi komanso kuti demokalase izamitsitse.

Mukutha kuona nyumba zoulutsa ndi kusindikiza nkhani zikuima pa zokha pa nkhani ya chuma?

Izi ndizotheka ngati boma lingamapereke malonda ku nyumba zonse zoulutsa ndi kusindikiza nkhani mosaona nkhope. Monga mukudziwa bizinesi yosindikiza nyuzipepala kapena kuyendetsa wailesi zimafunika kupeza malonda okwanira. Kuno ku Malawi boma ndi limene limapereka kwambiri malo-nda. Kusemphana ndi boma kumatanthauza kuti malondawa mumanidwa.

Kaufa: Tikufuna atolankhani asamafinyike

Tipemphe boma ndi kampani zosiyanasiyana kuti zizitha kupereka malonda awo ku nyumbazi mosakaikirana. Izi ndi zomwe zingathandize kuti ntchito yautolankhani ipite patsogolo. Komanso nyumba zosindikiza ndi kuulutsa mawu zipeze njira zina zoonetsetsa kuti zikupeza ndalama monga kuchita maubale ndi mabungwe pogwirira limodzi ntchito monga mapulojekiti osiyanasiyana.

Mawu omaliza?

Atolankhani ndi nyumba zonse zosindikiza ndi kuulutsa nkhani, Media Council ndi bungwe lanu. Lithandizeni kuti limere mizu kuti ligwire bwino ntchito yake. Litetezeni polithandiza pa chuma ndi ntchito zina. Ndi bungwe lofunikira kwambiri ngati tikufuna kuti utolankhani udziyenda bwino.

Tikhala tikuyenda dziko lonse kudziwitsa anthu za ndondomeko zomwe takhazikitsa kuti atolankhani komanso mabungwe amene timagwira nawo ntchito azidziwe. Tikukhulupirira kuti ulendo uno zinthu ziyenda bwino ndipo utolankhaninso upita patsogolo.