Piksy wakodola Nepman, Saint

Wolemba: Bartholomew BOAZ

Atatulutsa nyimbo yoyamba m’chaka chino yotchedwa ‘Chonchobe’, mnyamata woimba nyi-mbo za achinyamata Piksy waulula kuti akuphika chimbale chake chotchedwa ‘Mtunda’.

Piksy waululanso kuti akukazinga nyimbo imodzi imene ikhale mu chimbalechi ndipo wati aimba nyimbo ina ndi oimba ena otchuka a m’dziko muno.

Piksy: Ndakhala nthawi osatulutsa
nyimbo yowonera

“Ndikukonza zotulutsa nyimbo imene nditaimbe ndi Nepman komanso Saint,” watero Piksy, yemwe dzina lake lenileni ndi Evance Zangazanga.

Patha zaka zingapo mnyamatayu asanatulutse chimbale. Koma iye waulula kuti chaka chino ali ndi ntchito yambiri yotulutsa nyimbo zosiyanasiyana kuphatikizapo nyimbo zowonera.

“Patenga nthawi ndisanatulutse nyimbo yoonera koma pano ndikuwauza anthu ondikonda kuti ayembekezere kuti nditulutsa,” watero Piksy.

Iye wati wayamba kale kujambula nyimbo yoonera ya ‘Cho-nchobe’ ndipo imeneyi ikhala yoyamba m’chaka chino.