Akubwezeretsa ulimi wa mthirira m’chimake

Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA

Pofuna kuthana ndi njala m’dziko muno, boma ndi mabungwe omwe siaboma amalimbikitsa anthu akakolola zokolola ku munda – maka omwe akukhala m’mbali mwa mitsinje kutengerapo mwayi wochita ulimi wa nthirira omwe amalima mbewu zosiyanasiyana nkumagulitsa kuti galu wakuda achepe m’makomo.

Anthu a m’mudzi mwa gulupu Chambuluka, mfumu yayikulu Nkaya, m’boma la Balaka atamva za mmene angathanirane ndi njala mdelari kudzera mu ulimi wa nthilira, anapereka malo awo omwe ali m’mbali mwa mtsinje wa Shire kuti adzilima mbewu zosiyanasiyana.  Malowa ndi okwana mahekitala makumi awiri ndipo amapindulira midzi yoposa isanu.

Sikimu yomwe ipindule ndi ulimi wa mphamvu ya m’bwereza

Malingana ndi a Paul Mtendere, womwe ndi mkulu woyang’anira sikimu ya Nakatale, kaamba ka mavuto akusintha kwa nyengo omwe anakumana nawo mchaka cha 2008, midziyi munali njala yadzaoneni ndipo anthu analibe pogwira chifukwa amadalira zokolola zaku munda.  Panalibe yemwe akanathandiza mzake kumbali ya chakudya ndi ndalama chifukwa sankadziwa kuchita ulimi wa nthirira ngati bizinesi. Iwo ankadalira ulimi wa pa chaka.

“Tinakhala pansi nkukambirana za mmene tingathanirane ndi vutoli ndipo mchaka cha 2010 tinapeza malo kufupi ndi mtsinje kuti tidzichita ulimi wa nthirira. Ndipo tinapempha ala-ngizi a zamalimidwe kuti adzatipatse upangiri wa mmene tingamagwiritsire ntchito sikimu yathu,” anatero a Mtendere.

Iwo anati mu zaka zapakati pa 2010 ndi 2012 galu wakuda mdelari kunalibe chifukwa mabungwe monga Blantyre Synod ndi ena anabwera kudzawathandiza ndi upangiri wa malimidwe amakono ndi zina.

“Koma zinthu zinayamba kusintha mchaka cha 2013 pomwe mtsinjewu unayamba kuphwera ndipo ambiri mbewu zomwe analima sizinachite bwino kaamba ka vutoli,” anatero a Mtendere.

Kuphwera kwa madzi mu mtsinjewu kunabweretsanso mavuto a umphawi komanso njala m’makomo ambiri omwe amadalira sikimuyi.

“Zinthu sizinali bwino. Tinafika pomakatunga madzi m’zitsime kumathirira mbewu zathu  kuti zipulumuke koma chifukwa chotalika mtunda womwe timakatunga madzi ambiri anabwerera m’mbuyo. Pena tinkagula mafuta othira mu pampu yome timagwiritsa ntchito kupopa madzi zomwe ambiri samakwanitsa chifukwa cha mavuto a zachuma,” anatero a Mtendere.

Ngakhale anthuwa anakumana ndi mavutowa chidwi chochita ulimi wa nthirira kuti athane ndi njala anali nacho koma kaamba kakusintha kwa nyengo maloto awo anafera m’mazira chifukwa kwa zaka zinayi, palibe yemwe amapindula ndi sikumuyi.

Ulimi uphweka ndi mphamvu ya m’bwereza ya dzuwa?

Malingana ndi a gulupu a  Chambuluka ati pulojekiti ya tsopano yomwe bungwe la Community Energy Malawi yomwe ikugwira ntchito zolimbikitsa ulimi kudzera ku mphamvu ya  magetsi a m’bwereza, zinthu zisintha ndipo anthu ake avuwuka mu umphawi.

“Kaamba ka kusowa kwa madzi malingana ndi kusintha kwa nyengo komwe kunalipo zaka zapitazi anthu kuno amagona osadya. Sikimuyi imathandiza kwambiri chifukwa mbewu zikacha alimiwa amakagulitsa ndipo ndalamazo zimakathandiza pakhomo monga kulipirira ana sukulu fizi ndi zina,” anatero gulupu Chambuluka.

Yona: Mavuto anjala achepa

A gulupuwa anati sikimuyi ikayamba kugwira ntchito kudzera ku zipangizo zomwe bungweli litayike zithandiza kuchepetse mavuto anjala komanso kuchepetsa kuyenda mtunda wautali womwe amayenda kukasaka madzi kuti athirire mbewu zawo.

“Makina omwe atiyikire kuno sikuti ipundule ndi sikumu yokhayi. Tamvanso kuti anthu omwe amachita mabizinesi ang’onoang’ono monga kumeta ndi zina apindula nawo zomwe zithandize anthu kusayenda mtunda wautali kukameta kapena kukatchaja mafoni,” anatero a          Chambuluka.

Iwo anati migelo yomwe anakumba kupatutsa madzi mu mtsinje wa Shire inakwera m’mwamba zomwe zinachititsa anthuwa kusachitanso ulimi chifukwa madzi amayenda m’migeloyi osapita m’minda yawo.

“Kuyikidwa zinthu zamakono zomwe madziwa aziyenda mosavutika ndipo anthu ambiri omwe amachita ulimi wawo mbali imeneyi adzapindula nawo ngati kale,” anatero a Chambuluka.

Mayi Enifa Phiri omwe akhala akuchita ulimi ku sikimuyi nawo anati njira yogwiritsa mphamvu ya magetsi a m’bwereza ichepetsa ntchito yomwe amagwira yopopa madzi mu mtsinjewu komanso ndalama zomwe amalipira zogulira mafuta kuti jeniseti yomwe amagwiritsa ntchito kupopa madzi idzigwira ntchito yake.

“Pano ulimi uphweka ndipo sizikhala mwa kale pomwe tinkagwiritsa ntchito zipangizo zamakolo pochita ulimi. Ambiri timadandaula kuphwanya thupi ndi zina chifukwa zipangizozo zimalira mphamvu,” anatero a Phiri.

Iwo anati ntchitoyi ikayambika ulimi uphweka ngati kale ndipo galu wakuda ndi umphawi ikhala mbiri yakale chifukwa anthu a mderali amakonda ulimi.

Mlangizi wa bungwe la Community Energy Malawi, a Loius Yona anati bungwe lawo, kudzera pulojekiti ya Rural Energy Access through           Social Enterprise and Desentralization (EASE), cholinga chake ndi kulimbikitsa anthu akumidzi kugwiritsa ntchito magetsi a m’bwereza ocho-kera ku mphamvu ya dzuwa pochita ulimi ndi zina.

“Bungwe lathu titachita kafukufuku yemwe anatenga nthawi anawonetsa kuti ntchito yomwe tikugwira kuno ku sikimu ya Nakatale ndi yomwe ikuyenera kupindula ndipo tikhazikitsa malo otchedwa Hub pa chingerezi omwe tiyikepo zipangizo zomwe zizikagwiritsidwa ntchito ku sikimu komanso omwe akufuna bizinesi monga yometa, yotchaja ma foni ndi zina pa malowa,” anatero a Yona.

A Yona anati ntchitoyi ikatha anthuwa akuyenera kutengapo umwini osamalira zipangizo osati kuwononga kuti mavuto anjala omwe ali mderalo achepe chifukwa azidzachita ulimi kwa chaka chonse ndi kumapha makwacha. Komanso mbewu zomwe amalima monga tomato yemwe amaonongeka chifukwa amalima ochuluka amasowa msika adzawapezera njira zomwe angamadzapangire tomato sosi komanso kupeza misika yabwino osati mmene amagulitsira kale.

Mtendere: Anthu timavutika ndi njala

Bungweli likugwira ntchito m’maboma khumi asanu ndi anayi a m’dziko muno ndipo m’boma la Balaka masikimu awiri ndi omwe apindule ndi ntchitoyi yomwe ndi ya zaka zinayi. Community Energy Malawi ikugwira ntchitoyi ndi thandizo lochokera m’dziko la Scotland ndi ndalama zoposa 30 miliyoni zomwe zigwiritsidwe ntchito pokonza malo a sikimu ya Nakatale.

Kumeneko anthu amalima mbewu za zamasamba, chimanga ndi zina zomwe zimadyetsa anthu a m’maboma ambiri mdziko muno kuphatikizapo bomali komwe anthu amadalira mbewu zolimidwa kumpoto kwa mtsinje wa Shire. Sukulu yapulayimale ya Mzepa idzapindula nawo ndi ntchitoyi ku mbali yowunikira kuti ophzunzira azikatha kuwerenga madzulo.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *