Coronavirus yasakaza miyoyo ndi chuma cha maiko

Kusamba m’manja ndi sopo nkofunikira pothana ndi Coronavirus

Wolemba: Joseph KAYIRA

M’mene nkhani yoti matenda a Coronavirus agwa mdera la Wuhan m’dziko la China kumayambiriro a mwezi wa December chaka chatha, ambiri ankangoganiza kuti ndi matenda monga ena aliwonse. Koma patatha miyezi ingapo zawonetsa kuti matendawa simatenda wamba chifukwa tikunena pano Coronavirus yemwe amayamba ndi kachirombo kotchedwa COVID-19, apha anthu oposa 14,000 pa dziko lonse. Anthu oposa 340,000 ndi amene apezeka ndi Coronavirus ndipo matendawa akhuza kale maiko oposa 177.

Izi zachititsa bungwe la zaumoyo pa dziko lonse la World Health Organisation (WHO) kuti lilengeze kuti matendawa tsopano ndi mliri. Pakali pano dziko la China lalengeza kuti lachita chotheka kuchepetsa mliriwu. Koma funso nkumati kachiromboka kachokera kuti? Monga tanena kale ndi mu mwezi wa Disembala chaka chatha pomwe akuluakulu azaumoyo mu mzinda wa Wuhan ku China anadabwa ndi matenda achilendowa.

Kafukufuku wawo kumeneko anaonetsa kuti matendawa ndi Coronavirus ndipo amawanda modabwitsa ndi mwachangu mu deralo. Patadutsa zaka zaonetsa kuti tiziromboti tikusautsa ndipo mchaka cha 2002 kunagwanso matenda ena otchedwa SARS – a chimfine cha mbalame – omwenso anapulula miyoyo ya anthu ku China ndi maiko ena. Mchaka cha 2012 matenda enanso ofananirako ndi awa a MERS anasausanso anthu mchaka cha 2012.

Matendawa asefukira mmaiko ambiri koma mpaka pano kuno ku Malawi kulibe yemwe wapezeka ndi matendawa. Ku Ulaya, ku America komanso muno mu Africa matendawa akusautsa. Muno mu Africa chiwerengero cha omwe apezeka ndi matendawa ndi chochepa tikafanizira ndi maiko aku Ulaya ndi Asia.

Ku China komwe kunayambira matendawa ndi anthu 3,245 omwe amwalira ndi matendawa. Koma ena akuti ndi povuta kukhulupirira chiwerengerochi kaamba koti kumeneko kumavuta kuti nkhani zenizeni zituluke. M’mene timalemba nkhaniyi nkuti ku Italy kutamwalira anthu 3,405 ndi mate-ndawa – chiwerengero chomwe ndichokwera kuposa kwina kulikonse. Maiko ena amene matendawa avuta ndi ku Spain, ku Germany, ku United Kingdom ndi United States.

Anthu ali ndi nkhawa kuti matendawa akalowerera kwambiri kuno ku Africa, kukhala kovuta kuthana nawo potengera kuti maiko ambiri ndi osauka ndipo sangakwanitse kusunga anthu amene ali ndi kachiromboka mmalo apadera osati mzipatala zomwe zilipo kalezi. Izi zidzasowa ndalama zambiri.

Boma la Malawi lalamula kuti sukulu zitsekedwe ngati njira imodzi yothandiza kuti matendawa atati afika m’dziko asafale. Anthu apemphedwanso kuti asamakhale m’misonkhano yoposa chiwerengero cha 100. Mipingo ina nayo yasintha nthawi zopempherera ndipo akungolola anthu ochepa pa nthawi yamapemphero.

Mipingo yaika nthawi yosiyanasiyana kuti chiwerengero cha opemphera chisamachuluke. Mipingo ina yachita chiganizo chopempherera panja ndipo kuti anthu akuyenera kukhala motalikirana. Nkhani imene ikulimbiki-tsidwa ndi ukhondo. Anthu akuyenera kusamba mmanja ndi sopo pafupipafupi popewa kachiromboka.

Mmaiko ena monga ku UK, ku Italy ndi ku Spain anthu akupemphedwa kukhala ku nyumba kwa masiku mpaka pomwe boma lilamulenso kuti abwerere ku ntchito ndi ku bizinesi zawo. Malo omwera mowa ndi odyera ambiri atsekedwa. Ku Italy anthu anauzidwa kuti akhale kunyumba mpaka pa 25 Malichi koma malipoti akuonetsa kuti tchuthichi chipitirira mpaka zinthu zitasintha.

Ku South Korea, Singapore ndi maiko ena mderalo, zinthu kumeneko zafika povuta chifukwa matendawa asakaza kwambiri. Kumenekonso maboma ali tcheru kulimbana ndi mliriwu kachiwiri atathana ndi matendawa kaamba koti anthu obwerera kumudzi akumatenganso matendawa.

Chuma chatekeseka

Chuma cha maiko chimayenda ngati malonda akuchitika pakati pawo. Mwa chitsanzo, ndege zikamayenda pakati pa maiko ndiye kuti chuma chikuyenda. Ndegezi zimanyamula katundu ndi anthu amene amabweretsa ndalama pakati pa maiko.

Mwa chitsanzo ndege za ka-mpani ya South African Airways zomwe zimatela pa mabwalo a Chileka ndi Kamuzu mu mizinda ya Blantyre ndi Lilongwe zimabwe-retsa alendo ndi anthu abizinesi omwe amadzagona mmahotela ndikumasiya ndalama m’meneno. Kuimitsa ndegezi kubwera ku Malawi kaamba ka matenda a Coronavirus kwasokoneza malonda ambiri.

Mmaiko ena kuphatikizapo la Malawi kwaikidwa malamulo oti anthu asayende kupita ku maiko kumene kuli mliri wa Coronavirus. Timadziwa kuti anthu ambiri abizinesi amapita ku China, South Africa ndi Tanzania kukatenga malonda awo nkumadzagulitsa kuno. Chiletso chopita kumeneko chaimitsa malondawa. Ena mwa anthuwa ali ndi antchito amene amawalipira kaamba ka bizinesizi. Nanga akapanda kulowera kume-neko antchito awo adzawalipira chani?

Mmaiko ena anthu ayamba kale kuchotsedwa ntchito kaamba ka Coronavirus. Makampani akuononga ndalama zambiri chifukwa sakupanganso ndalama. Ku Ulaya ndi kumene izi zachulukira chifukwa malo monga odyera kapena ogona sakupindulanso chifukwa anthu asiya kuyenda. Eni malowa akuyenera kutseka kaye mpaka Coronavirus atatha.

Kampani za ndege zikuluzikulu monga Emirates zalengeza kuti ziyamba zayimitsa maulendo a    m’maiko ena mpaka matendawa atazizira. Kampani ya Emirates yaimitsa ndege zopita m’mizinda 100. Ndege za kampaniyi zimapita mmalo 159 pa dziko lonse.

Ndege monga za Emirates zaimitsa maulendo wopita m’mizinda yambiri

Makampani ena ambiri andege akuti aluza ndalama zambiri chiyambireni Coronavirus. Ka-mpani ya ndege yaku Abu Dhabi ya Etihad nayo inalengeza kuti iyimitsa maulendo a ndege zake opita mmizinda 40 mmaiko a China, India, Saudi Arabia, Spain ndi Italy.

Maboma amaiko aku Ulaya ndi ku America aika thumba lapadera lothandiza makampani ndi anthu amene akhuzidwa ndi kuchotsedwa ntchito kwa anthu kaamba ka Coronavirus. Kuno ku Africa ndi maiko ochepa amene angakwanitse kuchita zoterezi. Ambiri amene akhuzidwe ndi matendawa adzayenera kutseka kampani zawo kapena kupeza ngongole kuti ayambirenso kawiri.

Nthendayi imafala pamene anthu ayandikana maka wina akayethyemula kapena kusokomola. Timadzi kaya malovu amene akagwera pa thupi pa wina ndi amene amayambitsa matendawa mwa winayo.

Zina mwa zizindikiro za matendawa ndi kutsokomola, chibayo, kumva kuzizira ndi zina. Maiko, kuphatikizapo la Malawi akuyesa chilichonse – ukhondo, mapemphero komanso kuletsa maulendo aku maiko omwe kuli Coronavirus – kuti mwina nkupulumutsa anthu ku mliri woopsawu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *