Katswiri ayamikira mwana wa Orton Chirwa, MCP

Chirwa (kumanzere) kulankhula pa tsiku losaina mgwirizano wa MCP ndi UTM

Wolemba: Godfrey MAOTCHA

Katswiri woona za ulamuliro wa-bwino wati kupezeka kwa mwana wa namatetule pa ndale malemu Orton Chirwa pa tsikulomwe chipani cha Malawi Congress (MCP) chimasaina mgwirizano ndi UTM ati ndi mwayi ku mbali ziwirizi kuti zionetse kwa Amalawi kuti zakale zinapita.

Banja la a Orton Chirwa lidazunzika kwambiri mu ulamuliro wa chipani cha MCP mu nthawi ya ndale za chipani chimodzi pomwe mtsogoleri wake adali malemu  Hastings Kamuzu Banda.

Mtsogoleri wa chipani cha MCP a Lazarus Chakwera, adaitanitsa Dr Zengani Chirwa mwana wa a Orton Chirwa kuti adzakhale nawo posainira mgwirizano wa zipani ziwirizi ku Lilongwe ndipo adamuitana mkuluyu kuti ayankhule kwa anthu.

A Henry Chingaipe ati kupezeka kwa a Chirwa ndi mwayi kuchipani cha MCP koma anati sanganeretu za maganizo aku banja la malemu Orton pa nkhaniyi.

“Chipani chilichonse chimadziwika ndi atsogoleri omwe alipo pa nthawiyo. MCP yomwe idachitira nkhaza a Orton Chirwa si yomwe ilipo panoyi, komanso nawo a Zengani Chirwa ndi mbewu yatsopano ku banja la a Orton Chirwa mwakuti mbali zonsezi zidaonetsa anthu kuti ndi zotheka kuiwala zakale ndi kuyambanso mwatsopano,” anatero a Chingaipe.

Iwo ati chipani cha MCP chaonetsa kuti chimavomereza kuti kale lake liri ndi mbiri ina yoipa, motero ndi pofunika kukonza.

A Chingaipe anati: “A Chakwera akufuna kuonetsa kuti utsogoleri wao ndi wosiyana ndi atsogoleri a MCP mu nthawi yomwe bambo awo a Chirwa adazuzidwa.”

A Orton Chirwa adali mtsogoleri woyamba wa chipani cha MCP mu nthawi ya atsamunda. Iwo adakhala nduna mu boma la chipani cha MCP asadasemphane ndi Dr Kamuzu Banda ndipo adafera ku ndende atamangidwa pa zifukwa za ndale.

A Chakwera adauza anthu kuti iwo adazutsa a Zengani Chirwa pofuna kupereka ulemu kwa bambo awo omwe anali mtsogoleri woyamba wa chipani chawo.

Mmodzi mwa akhristu  m’dayosiziyo yemwe amapemphera ku Parishi ya Matawale a Lawrence Nkaweya anati ndi zabwino kulimbikitsidwa kuti n’kofunika kumapemphera mosalema.

“Ndikukhulupirira kuti mate-ndawa atha ndithu. Mulungu atithandiza kuti zonse ziyambenso kuyenda bwino. Ndipemphenso Amalawi anzanga kuti titsate zomwe achipatala akutipempha,” anatero a Nkaweya.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *