Ndale zafika pa ali ndi mwana agwiritse

Wolemba: Joseph KAYIRA

Zatsimikizika. Chipani cha Malawi Congress (MCP) ndi UTM Party asainirana mgwirizano. Akuti zipani ziwirizi kuku-bweraku ziuza mtundu wa Amalawi kuti amene adzatsogolere mgwirizano umenewu ndi ndi ndani ndipo womutsatira adzakhala yani. Ndi uthenga womwe anthu amene anasonkhana pa bwalo Kamuzu Institute for Sports Lachinayi pa 19 Malichi chaka chino ankafuna kumva. Koma mwina a MCP ndi UTM asunga dala mainawo pofuna kuti amve manong’onong’o ochokera kwa anthu.

Monga m’mene anthu amaye-mbekezera akatswiri pa ndale ndi ulamuliro wabwino ayamba kale kuthirirapo ndemanga pa mgwirizanowu. Ena akuti uwu ndi mgwirizano umene uli ndi kuthekera kotenga boma chifukwa ndi umene uli ndi owatsatira ambiri. Ena akuti mgwirizano wa chipani cha Democratic Progessive (DPP) ndi United Democratic Front (UDF) ndiwo unga-tenge boma pokhala kuti enawo ali m’boma kale ndipo mwina kampeni siingawavute. Awa ndi maganizo a akatswiri omwe akuunika za momwe ndalke zikuyendera pakali pano.

Pa chisankho chapita chija – cha mu Meyi chaka chatha – a Peter Mutharika a DPP ndiwo bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidalengeza kuti apambana. Wowatsatira anali a Dr Lazarus Chakwera a MCP ndipo a Saulos Chilima a UTM Party adali a chitatu.

Ponenapo za mphamvu za mgwi-rizano wawo, a Chilima anati ngakhale sadagwirizane ndi zotsatira za chisankho cha pulezidenti, kungo-phatikiza mavoti omwe a Chakwera ndi iwo adapeza pa chisankhocho, ndi umboni wokwanira kuti MCP ndi UTM Party akhoza kupeza mavoti ochuluka kuposa a wina aliyense pa chisankho chikudzachi.

“Mukachita masamu ophatikiza mavoti omwe ine ndi Dr Chakwera tinapeza muona kuti ndi ambiri kuposa a enawo. Mgwirizano wathuwu ndi wamphamvu ndipo cholinga chake sikupeza maudindo koma kukonza Malawi,” anatero a Chilima polankhulapo za mgwirizano wa MCP ndi UTM Party.

Iwo akuti pali zambiri zofuna kukonza – umphawi wayanga ndele, katangale wachuluka, ntchito kwa achinyamata zikusowa – mwachidule iwo akuti dziko lasokonekera. Kusokonekera kumeneku kukusowa atsogoleri wokonda dziko lawo ndipo amenewa akuti ali mu mgwirizano wa MCP ndi UTM Party.

Koma sikukhala kwapafupi kusuntha chipani chimene chakhala chili m’boma kuyambira chaka cha 2005 nkudzapuma zaka ziwiri (2012-2014) nkudzalowanso m’boma 2014 mpaka lero. Chipani cha DPP nacho chili ndi ochitsatira ochuluka makamaka mchigawo cha kum’mwera ndi kum’mawa. Chipanichi chimathanso kutola mavoti m’maboma a m’mbali mwa nyanja monga Mangochi, Salima, Nkhotakota ndi Nkhatabay.

Mayi Ansah: Ayendetsabe chisankhochi?

Nthawi ya malemu Bingu wa Mutharika, maka pa chisankho cha mu 2009, chipani cha DPP chinasesa mavoti ochuluka kuphatikizapo m’maboma omwe pa nthawiyo anthu ankati ndi kuchipinda kwa MCP. Chipanichi chinakalowerera m’ma-boma monga Lilongwe, Mchinji, Ntchisi komanso Kasungu.

Bingu naye anapeza mavoti ochuluka kwambiri poyerekeza ndi omwe adapeza pa chisankho cha 2004. Ambiri anamukonda mtsogoleriyu ati kaamba ka chidwi chake chofuna kuthana ndi katangale yemwe panthawiyo anali atavuta kwambiri m’boma la UDF.

Komanso ambiri anakhutira ndi momwe Bingu anachitira pa nkhani ya ulimi. Kwa nthawi yoyamba mzaka zambiri, boma la Malawi linakhazikitsa ndondomeko yotha-ndiza alimi kupeza zipangizo zaulimi zotchipa monga mbewu ndi fetereza. Izi zinapangitsa kuti dziko la Malawi likolole chakudya chochuluka. Uku kunali ngati kuchepetsa njala m’mabanja ambiri.

Koma zinthu zinayamba kukhota pomwe Bingu anayamba mtima wosamva chidzudzulo. Ulendo wina anthu ataona kuti boma la DPP layamba kuphwanya maufulu awo, anthuwa motsogozedwa ndi mabungwe omwe siaboma anachititsa zisankho za dziko lonse. Ku Mzuzu ndi ku        Lilongwe apolisi anaombera anthu ndipo chiwe-rengero cha ophedwa chinafika pa 20.

Komanso boma la DPP pa nthawiyo linasintha malamulo ena ndi kuika atsopano monga loti nduna izitha kutseka nyumba zosindikiza ndi kuulutsa mawu ndunayo ikaona kuti nyumbazo siziyendetsa bwino ntchito zake. Komanso lamulo lina pa nthawiyo linali loti apolisi azitha kuchita chipikisheni wopanda zipepala zowaloleza kutero.

Sizinatenge nthawi. Boma la Bingu linapirikitsa Kazembe wa ku Britain ati kaamba koti kazembeyo anauza dziko lake kuti Bingu anafika poti sakumvanso chidzudzulo ndipo ulamuliro wake ukulowera ku ulamuliro wa mphamvu. Izi sizinasangalatse a Bingu ndi boma lawo. Kazembeyo a Cochrane Dyet anauzidwa kuti azipita kwawo. Mavuto a boma la Bingu anayambira pamenepo.

Mafuta a galimoto anayamba kusowa. Dziko la Britain linaimitsa lina mwa thandizo lomwe limapereka kuno ku Malawi kuphatikizapo thandizo la ndalama zomwe zimapita ku ndondomeko ya chuma cha dziko lino (bajeti). Mwachidule, chuma cha Malawi chinasokonekera. Izi zina-tsatizana ndi imfa ya a Bingu pa 5 April 2012.

DPP kutuluka nkudzalowanso m’boma

Imfa ya Bingu inapereka mpata kwa mayi Joyce Banda, omwe pa nthawiyo anali wachiwiri wa pulezidenti kulowa m’boma ngati pulezidenti. Mayi Banda anali atawachotsa mchipani cha DPP ndipo pa nthawiyo anali ndi chipani chawo cha Peoples (PP). 

Mayi Banda anakhala pa mpando waupulezidenti kwa zaka ziwiri. Umu nkuti chipani cha DPP chikudzitolera pansi pa utsogoleri wa a Peter Mutharika. Pa chisankho cha mu 2014, a DPP anabwereranso m’boma. A MCP sanagwirizane ndi zotsatira za chisankho cha pulezidenti. Wakhala uli ulendo wapendapenda mpaka chaka chatha pomwe chisankho china chinachitika.

Monga mchaka cha 2014, a MEC analengeza kuti a Mutharika ndiwo adapambana koma ulendo uno ‘wolephera’ anathamangira ku khoti komwe akhoti anagamula kuti chisankhochi chichitikenso.

Chigamulocho chadza ndi za-mbiri. Malamulo oyendetsera chisankho cha pulezidenti atanthauziridwa mwatsopano. Akuti tsopano wopambana pa chisankho cha pulezidenti akuyenera kupeza theka la mavoti omwe aponyendwa – chidule chake akuti 50%+1. M’mbu-yomu yemwe watsogola amatha kupeza mpando waupulezidenti.

Kusintha kwa lamuloli ndi komwe kwadzetsa mpungwepungwe pakati pa zipani. Zikuonekeratu kuti yemwe angaime payekha mwina sangakwanitse kupeza 50%+1 monga mmene malamulo akunenera. Kupanda kupeza 50%+1 kukuta-nthauza kuti opikisana awiri oya-mbirira adzapikisananso m’ndime yachiwiri.

Popewa kulowa m’ndime yachiwiri, zipani zapangana zoyendera limodzi kuti mwina nkupeza theka la mavoti pakamodzinkamodzi. Ndi ntchito yaikulu. Ndi ntchito yomwe ikusowa mgwirizano wamphamvu komanso kampeni ya usana ndi usiku. Nchifukwa chake mgwirizano uliwonse pa nthawi ino ukuyenera kuunikira kufunika kwa umodzi ndi chilungamo.

Kawirikawiri dyera la atsogoleri limachititsa kuti anthu asakavote. Anthu amati atsogoleri amangogawana mipando ndi kudzilemeretsa iwo eni osalabadira za awo amene anawaika m’mipando.

A Chilima ndi a Chakwera agwirizana kuyendera limodzi pa chisankhochi

Mwa chitsanzo, mgwirizano wa DPP ndi UDF womwe unalipo m’mbu-yomu akuti siunapindulire ambiri. Kuchokera ku UDF ndi a Atupele Muluzi omwe amaoneka kuti zawo zinayenda. Iwo anali nduna m’boma la a Mutharika kufikira pomwe chisankho china chinafika. Ena mu UDF anali ongowonera zochitika. Mwina ndi ochepanso omwe anapatsidwa mpata wolowa nawo mmabodi oyendetsa kampani za boma.

Ulendo uno, kuchokera ku UDF, Pulezidenti Mutharika wasankhanso a Muluzi ndi ena angapo mu maunduna a boma. Uku ndikulimbitsa      mgwirizano wa zipanizi. Koma mgwirizanowu upereka chikoka mzigawo zonse? UDF mphamvu zake zili mchigawo cha kum’mawa – Mangochi, Machinga, Zomba, Balaka ndi Ntcheu. DPP ilinso ndi mphamvu m’mabomawa kuphatikizapo ku Blantyre, Mulanje, Thyolo, Phalombe, Mwanza ndi Neno.

Mgwirizano wa DPP ndi UDF ukuyenera kupeza mavoti ena owo-njezera ku Chikwawa ndi Nsanje. Sipokhapo. Zipanizi zikuyeneranso kulowerera maka mchigawo chapakati ndi kumpoto, komwe pakali pano a MCP ndi UTM Paty akudalira kwambiri. Ndimavoti owonjezerawa omwe angathandize kuti DPP ikhalebe m’boma.

Kumabli inayi, a MCP amadalira kwambiri chigawo chapakati. Kulephera kwawo kulowa m’boma nchifukwa choti amalephera kubooleza mchigawo chakum’mwera. Mgwirizano wawo ndi a UTM Party unga-wathandize kuti adzapateko mavoti owonjezera kum’mwera ndi kumpoto. Koma kuti izi zitheke pakuyenera kukhala kampeni yamphamvu.

Choncho ndi kovuta kuneneratu kuti uyu ndi amene akupita ku nyumba yachifumu. Mgwirizano wa MCP ndi UTM Party uli ndi chikoka pakati pa achinyamata pamene wa DPP ndi UDF ukutsamira kwambiri pa mavoti ochokera m’madera akumidzi.

Chidule chake ndi choti amene achite kampeni yamphamvu nkukopa anthu ambiri amene analembetsa kapena amene alembetse kutsogoloku ali ndi mwayi wopeza theka la mavoti monga m’mene malamulo akunenera.

Nkhani ina imene ikuvuta ndi ya makomishona a MEC ndi wapampando wake mayi Jane Ansah. Kodi apitirira kuyendetsa zisankhozi pamene zipani zina ndi mabungwe ena omwe siaboma akuti anataya nawo chikhulupiriro?

Pulezidenti Mutharika anakana kuchotsa  anthuwa pamaudindo awo. Kodi akayendetsa chisankho anthu omwewa ndipo pulezidenti Mutharika nkupambana zotsatirazo adzadzivomereza? Nanga anthu omwewa akayendetsa chisankhochi ndipo wambali yo-tsutsa nkupambana zidzatha bwanji?

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *