OSEWERA ALI PA CHIOPSEZO

Akuti timu yake siinamitse mapulakatesi – Mzava (kumanzere)

Wolemba: Bartholomew BOAZ

Anyamata ena osewera mu timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino amene padakali pano akusewera m’matimu a ku South Africa ali pa chiopsezo chachikulu chotenga matenda a Covid-19 pamene zamveka kuti akupitirira kuchita mapulakatesi m’dzikolo.

Ena mwa osewera amene ali pa chiopsezo ndi Gabadinho Mhango (Orlando Pirates), Robert Ng’ambi (Black Leopards) ndi Limbikani Mzava (Highlands Park).

Bungwe loyendetsa ligi ya dzikolo idaimitsa masewero a ligi ya chaka chino, monga momwe maiko ena onse pa dziko lapansi achitira ndi cholinga chofuna kupewa mliri wa coronavirus.

Koma malinga ndi zomwe yalemba nyuzipepala ina ya dzikolo ya KickOff.com pafupifupi matimu asanu ndi awiri osewera mu ligi ya Absa Premiership akupitirizabe kuchita mapulakatesi posatengera anthu adaletsedwa kumasonkhano m’magulu ndi kumachita masewero.

Ena mwa matimuwa ndi monga Orlando Pirates, Black Leopards, Bloemfontein Celtic, Cape Town City, Golden Arrows, Highlands Park ndi Stellenbosch FC.

Ganizo la matimuwa lomachita mapulakatesi lapangitsa anthu osiyanasiyana kupereka maganizo awo. Pamene akuti palibe chovuta kutero pokhapokha ngati aku-dziteteza, ena akuti osewerawa saku-yenera kumachita mapulakatesi.

“Ndikuganiza kuti ndi kuika moyo pa chiswe kumapitiriza kumachita mapulakatesi potengera kuopsa kwa matendawa,” Malum Bison anauza kickoff.com.

Pamene timatsindikiza nyu-zipepalayi, anthu oposa 400 nkuti atamwalira ndi nthenda ya Covid-19 m’dziko la South Africa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *