Blue Eagles yati tsopano maso ali pa Ligi

Blue Eagles ikuti zikho zina yatopa nazo

Wolemba: Victor SINGANO Junior, Mtolankhani Wapadera

Timu ya Blue Eagles yati iyo siikugonabe tulo ndi kulephera kosatenga chikho cha TNM Supa Ligi mu zaka zammbuyomu kotero iyo yati ulendo uno imenya nkhondo yoopsa kuti inyamule ligi. 

Kaputeni wa timuyi yomwe imathandizidwa ndi nthambi ya apolisi ku likulu lawo ku Area 30 mu mzinda wa Lilongwe, Micium Mhone watsindika kuti ngakhale patenga nthawi mpira usanayambe mdziko muno kamba ka mliri wa Covid-19, timuyi siinasinthebe khumbo lake lomwe inalonjeza kuti ikufunitsitsa itanyamula chi-kho cha TNM Supa Ligi kuyambira chaka chino.

Mhone wati zomwe akuluakulu komanso osewera a timuyi anagwirizana kumapeto a chaka chatha chinali choti amenye nkhondo yonyamula ligi osatinso kulimbana ndi zikho zakapherachoka zomwe anati azipambana kokwana tsopano.

Eagles inamalidza mwapamwamba mu ligi ya 2019 pomwe inathera panambala yachitatu pa mndandanda wa matimu amu Supa Ligi ndipo kuwonjezera apo, timuyi inatenganso chikho cha FISD Challenge Cup komanso chikho cha Airtel Top 8 mu 2018.

Timuyi inakwanitsanso kugonjetsa matimu onse akuluakulu omwe ndi Nyasa Big Bullets, Be Forward Wanderers, Civo Service United komanso Silver Strikers mchaka chathachi.

“Zonse zomwe tinagwirizana zili chimodzimodzi ndipo palibe chomwe tingasinthe. Tikudziwa kuti matimu ambiri akhala atatikonzekera malinga ndi zomwe tinapanga chaka chatha komabe ife tayima pachiganizo choti tinyamule ligi basi.

“Kuchokera chaka chatha, tinali ndi timu yabwino kwambiri ndipo chaka chinonso tikhala ndi timu yoposera pamenepo chifukwa tinalandira osewera enanso aluso kuchokera ku matimu ena zomwe zikutipatsa chilimbikitso kuti pavute pasavute ligi idzakhala mmanja mwathu,” anatero Mhone yemwenso amasewerera timu ya dziko lino ya Flames.

Eagles inaonjezera osewera monga Lazarus ‘Deco’ Nyamera, Mphatso Filimoni, Chifuniro Mpinganjira, mwa ena.