KULI NJALA YA ZAONENI …Ana 426 akhoza kumamwalira tsiku lirilonse – Save the Children

Chimanga chipezeka?

By Joseph KAYIRA

Pamene kwamveka kale ma-lipoti oti anthu 2.6 miliyoni akhuzidwa ndi njala m’dziko muno, bungwe la Save the Children nalo latulutsa lipoti loti maiko ambiri kunsi kwa chipululu cha Sahara akhala pa mavuto a zaoneni a njala ndipo kuti ana oposa 67,000 akhoza kumwalira kaamba kosowa chakudya komanso mavuto omwe akolezera matenda a Coronavirus (COVID-19).

Lipoti lomwe bungwe la Save the Children latulutsa pa 1 Sepitembala, lati pali nkhawa yoti izi zikapitirira ana ambiri akhoza kumwalira pomafika kumapeto a chaka chino.

Mwa zina, lipotili lomwe lapeza kafukufuku wina kuchokera ku nyuzipepala ya The Lancet yaku Ulaya, lanenetsa kuti ndi ana 426 amene akhoza kumwalira pa tsiku, pokhapokha patachitika dongosolo loti chakudya chipezeke msanga ndi kutumizidwa mmaiko okhuzidwawa.

A Save the Children ati vuto la kusowa kwa chakudya muno mu Africa lakula kwambiri chaka chino kaamba ka mavuto ena monga kusefukira kwa madzi, dzombe lomwe linagwa mmaiko ena monga Kenya komanso kukwera mtengo kwa chakudya.

Mavenda amakweza mtengo wa chimanga zinthu zikafika povuta

“Mliri wa COVID-19 nawo wakolezera mavuto omwe analipo kale pa nkhani ya kusowa kwa chakudya kaamba koti ntchito za chuma zasokonera ndipo mabanja ambiri akusowa mtengo wogwira. Mabanja ambiri akulephera kugula chakudya komanso alibe kuthekera kopita ku chipatala chabwino kuti akathandizidwe akadwala kaamba koti ndalama zikusowa”, letero lipotilo.

Kumayambiriro a chaka chino akatswiri ena pa chuma adachenjeza kuti mliri wa COVID-19 ukankhira anthu ambiri ku umphawi – kutanthauza kuti pa anthu 100 aliwonse, anthu 23 avutika kwambiri ndi umphawi.

A Save the Children ati pofika m’chaka cha 2030 anthu 433 miliyoni adzakhala a matupi opinimbira, osowa chakudya chopatsa thanzi.

Mayi wina waku Puntland ku Somalia, yemwe a Save the Children   angomutchula kuti Ubah yemwenso ali ndi ana asanu ndi m’modzi wati: “Umoyo unali wovuta ndi wowawa kwa ine ndi banja langa koma ndinalimbikira ntchito ndipo tinapulumuka. Koma matenda a Coronavirus atipatsa umphawi. Pakali pano ntchito zikusowa. Tisanalandire thandizo [kuchokera ku Save the Children] timadya kamodzi pa tsiku ndipo uku kumakhala kum’mawa. Ndaona ana anga akugona ndi njala zomwe zili zopweteka kwa mayi. Ndizowawa kuti mayi azilephera kudyetsa ana ake.”

Lipotilo lati pamene chakudya chikusowa m’maiko ambiri, ana ambirinso ali pa chiopsezo cho-tupikana. Mliri wa COVID-19 usanafike, ana oposa 26 miliyoni kum’mawa ndi kum’mwera kwa Africa anali opinimbira ndipo 2.6 miliyoni anali onyentchera. Pamene kuzambwe ndi pakati pa Africa, 15.4 miliyoni a zaka zosaposa zisanu azasowa chakudya chaka chino. Chiwe-rengerochi chakwera ndi ana 20 pa 100 iliyonse potengera m’mene vutoli linalili m’mbuyomu.

“Tayamba kale kuona ululu wa COVID-19 pakati pa anthu omwe amavutika ndi njala chaka ndi chaka. Ndondomeko zopewera Coronavirus zasokoneza miyoyo ya anthu ndikusokonezanso ntchito za ulimi. Ntchito zaumapo, anthu sakulembedwanso ndipo mtengo wa chakudya ukukwera kwambiri – ngati chakudyacho chikupezeka. Chidule chake ndi choti makolo ambiri akukanika kupeza chakudya kuti adyetse ana awo,” anatero a Ian Vale omwe ndi mkulu wa Save the Children kum’mawa ndi kum’mwera kwa Africa.

A Vale anati: “Tikulandira ana   ambiri omwe akufika mzipatala zathu ali onyentchera. Tikudziwa kuti ichi ndi chiyambi chabe. Kusowa kwa chakudya kukhoza kuphetsa mazana manaza a ana. Nkofunika kuwafikira msanga ndi chakudya Sitingadikirenso.”

Mliri wa COVID-19 usanafike, kunsi kwa chipululu cha Sahara kunali kale vuto la kusowa kwa chakudya. Vutoli likapitirira, derali likhala limodzi mwa madera omwe ali ndi anthu ochuluka osowa chakudya pa dziko lonse.

Bungwe la Save the Children likuthandiza anthu powapatsa chakudya ndi ndalama maka mabanja ovutikitsitsa. Bungweli likuonetsetsanso kuti anthuwa akukwanitsa kupeza madzi aukhondo. Ilo lati likufuna mabungwe ndi maiko agwirane manja pothana ndi vuto la njalali.

Zinthu zili chonchi, pamvekanso malipoti oti a Malawi Vulnerability Assessment Committee (MVAC) apeza kuti Amalawi osachepera 2.6 miliyoni asowa chakudya.