NICE iphunzitsa amkupamame pa nkhondo ya Covid-19

Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA

Bungwe lophunzitsa anthu nkhani zosiyanasiyana la National Initiative for Civic Education (NICE) Trust laphunzitsa amkupamame (mavolontiya) omwe amagwira ntchito ndi bungweli za mmene angafalitsire mmene nthenda ya Coronavirus imafalikira komanso kapewedwe kake.

Mkulu wa bungweli m’boma la Balaka a Henry Zekeriya anati cho-linga cha maphunzirowo mkufuna kuwapatsa amkupamame upangiri ndi mphamvu za mmene angawawuzire anthu akumudzi mmene angavalire ka nsalu kodzitchingira ku maso (mask) moyenerera ndi kupewa matendawa kuti asafalikire pakati pawo.

Zekeria: M’madera a m’midzi ntchito idakalipo

“Anthu ambiri sakuvala masiki moyenerera chifukwa chosadziwa enanso akumangotaya paliponse zomwe ana ndi anthu ena akumatola kumagwiritsanso ntchito. Izinso ndi zina zomwe zingachititse matendawa kumangofalikira pakati pa anthu chifukwa chakusadziwa kasamalidwe kake,” anatero a Zekeriya.

Iwo anati anthu akumudzi alinso ndi zikhulupiliro zoti nthendayi ndi ya anthu olemera komanso azungu zomwe zili zolakwika. Chifukwa wina aliyense ali pa chiopsezo chotenga matendawa posatengera mtundu ka-pena chuma chomwe ali nacho.

“Kotero pofuna kuthana ndi zikhulupiliro zomwe anthu ambiri ali nazo, bungwe lathu laphunzitsa amkupamame, achipatala, mafumu ndi adindo kuti azitenga nawo mbali yozindikilitsa anthu madera omwe akuchokera ndipo ntchitoyi tikuyitchula kuti ‘Ntchembere zandonda’ pa Chichewa chifukwa adziyenda khomo ndi khomo kuphunzitsa anthu,” anatero a Zekeriya.

Iwo anati anthu ambiri makamaka akumudzi ngakhale mmizinda imene sakudziwa kuti Covid-19 ndi chani  ena akumati ndi chifuwa wamba ndipo anthu akuda sangadwale koma azungu.

“Nthendayi sichifuwa wamba ndipo anthu achotse zikhulupiliro zomati nthendayi inabwerera azungu ndi anthu ochita bwino okha. Anthu adziyesesa kumavala masiki molondola ngakhale kuti nthawi zina imabanikitsa,” iwo anatero.

Mmodzi mwa a mkupamame ochokera wodi ya Rivirivi a Willy Tambala anati maphunzirowa awa-thandiza kudziwa za kapewedwe ka Covid-19 komanso upangiri womwe alandira uthandiza kagwiridwe kawo ka ntchito kuti iyende bwino.

“Kumudziku nkhani yovala masiki, kusamba mmanja ndi sopo mowilikiza, kukhala motalikirana ndi zina, anthu ambiri sakutsatira kaamba ka zikhulupiliro zomwe ali nazo. A mkupamame ndi ntchito yathu kutengapo mbali yozindikilitsa anthuwa za izi kuti kufalikira kwa matendawa kuchepe,” anatero a Tambala.

Bungweli linaphunzitsa amkupamame 163 ochokera ma wodi a Liwawadzi ndi Rivirivi komanso alangizi azaumoyo 32.