Mussa Chikoti: M’misiri wodabwitsa

Mussa: Ndimathokoza Mulungu kaamba ka luso langa

Wolemba: Joseph KAYIRA

Sitonse amene tinganene kuti tili ndi luso pa chilichonse. Ambiri luso lathu limakhala pa chinthu chimodzi chifukwa mwina tinaphu-nzira kuchita zimenezo – kaya kusukulu ya ukachenjede kapenanso pansi pa mtengo. Ena amatha kukhala ndi luso lingapo – mwinanso kuchita kukakamiza kuti lusolo litheke. Koma Mussa Chikoti ndi wodabwitsa. Iye amachita zinthu zambiri – umekaniki, kuimba nyimbo mu bandi ndi kusewerea zida zosiyanasiyana, umisiri wokonza zipangizo monga firiji, ma air conditioner, makina odinda nyuzipepala ndi makina ena opezeka mmaofesi, kuyendetsa thiraki, kuotcherera zitsulo nkumapanga mawindo ndi zitseko, kukonza matoileti amadzi akaonongeka ndi zina zambiri. Komatu Mussa sanangofikira pamenepa. Ali ndi mbiri yochititsa chidwi. Joseph Kayira wa nyuzipepala ya Mkwaso anacheza ndi Mussa kuti amve za mbiri ya mnyamatayu. Kucheza kwawo kunali motere

Kodi tikamati Mussa Chikoti, ameneyu ndi munthu wotani?

Ndinganene kuti Mussa Chikoti ndi mnyamata amene wakula movutika kwambiri. Ndimamva kuti bambo anga enieni anali a Mussa James. Koma amene andilera ndi a Samson Chikoti, woimba wakalekale mu Alleluya Band ku Balaka. Ndakulanso ndi agogo anga omwe pantha-wiyo nawonso anali wovutika kwambiri ndipo umoyo unali wovuta kuti tidye pakhomo.

Mwangokambapo za bambo anu; nanga mayi?

Akulu, nkhani yanga ndi yovuta kuimvetsa. Ndinauzidwanso kuti mayi anga anandibereka ali pa sukulu. Choncho anakanditaya pafupi ndi mtsinje wa Lirangwi ku Blantyre, iwo nkuthawa. Ananditola ndi abusa aziweto. Iwo atanditola ndipo ataona nsalu imene anandikutamo anazindikira nsaluyo kuti ankavala ndi msungwana wina wake, yemwe anali mayi angawo. Ana-nditengera kukhomo kumene kunkakhala msungwanayo. Koma iye anali atathawa. Choncho ndinakulira pakhomo pa mayi angapo koma chisamaliro panalibe kwenikweni.

Moti zinanditengera zaka 25 kuti ndidzawadziwe mayi angawo. Nthawi yonseyi anali ali kunja kwa dziko lino. Ndinawafunsa kuti ndi chifukwa chani munanditaya mutangondibereka kumene? Kwa ine zakale zilibe ntchito ndipo ndinakambirana nawo mayiwo. Pano ndimalemu koma kwa ine ndimayamika kuti ndinakwanitsa kukumana nawo ndikuwafunsa funso limeneli.

Tsopano kuti mudzidziwika ndi dzina la Chikoti?

Mwafunsa bwino. a Chikoti ndi womwe ananditola ndikuvutika nthawi imene ndinasamukira ku Balaka. Kuyambira pamenepo basi ndinakhala ngati ndine mwana wa banja la a Chikoti. Ndiantenga dzina la Chikoti mpaka lero. Iwowa ankadutsa pakhomo pa agogo anga ndipo amaona mmene ndinkavutikira. Anaganiza zonditenga kuti umoyo wanga usinthike.

Nthawi imeneyo ndinali ndimabala ndipo ndinali mwana uja woti analibe wocheza naye.

Achibale amandikana chifukwa amati ine simwana wawo. Palibe amene ankandithandiza. Apa ndi pomwe a Chikoti anangoti mwanayu ndimutenga. Choncho ndakula ngati mwana wawo ndipo anandiphunzitsa zambiri, monga zokonza zinthu za magetsi komanso kuimba gitala.

Moti pano ndimaimba zida zosiyanasiyana komanso ndimajambula nyimbo mu studio ngati wojambula nyimbo (producer).

Kufikira lero ndakhala ndikuimba ndi magulu komanso oimba osi-yanasiyana. Amatha kundiitana kuti ndikawathandize akakhala ndi mwambo wazoimbaimba. Alipo a-mbiri omwe ndikugwira nawo ntchito zomwe zapangitsa kuti ndidziwe madera ambiri kuno ku Malawi komanso kunja kwa dziko lino.

Za sukulu nde munafika nazo pati?

Monga ndanena kuti ubwana changa chinali chovuta, sukulunso inavuta kuti ndipitirize. Koma mwachisomo ansembe ena a Mpingo wa Katolika anachita chotheka kuti ndi-pitirize maphunziro. Komatu panali matatalazi chifukwa nthawi ina ndimathawa ku Balaka kupita ku Blantyre kukafuna maganyu. Ndinakafikira ku Lirangwi ndipo umoyo unali wovuta chifukwa ndinalibe pogona. Tikagwiragwira maganyu athu timakamagona pansi pa mlatho. Kuchoka pa Lirangwi nde ndinakapezeka ku Bangwe ku Blantyre konko.

Kumenekonso nkhani yake inali ya maganyu komanso kulanda anthu katundu zikatidzera. Tinali ana ovuta mtauni ya Blantyre. Ena mwa amene amatituma anali akamuna wovuta mtauni yonse ija ya Blantyre. Nthawi imeneyo timakulira limodzi ndi achina Njati Njedede ndi Joe Gwaladi.

Taona zovuta chifukwa tima-thanso kugona pansi pa mlatho kapena m’migelo yodutsa madzi. Pena muli pansi pa mlatho mumangoona madzi akuchulukirachulukira mvula ikagwa ku mtunda. Zikatero magonedwe amasokonera. Penanso timakumana ndi apolisi a vakabu. Umoyo unali wovuta kwambiri.

Mwamwayi, munthu wina wake wochokera ku Balaka atandiona anandiuza kuti ndikampeze ku Chirimba chifukwa amafuna kundigayira zovala. Atandipatsa zovalazo anandipatsanso ndalama kuti ndipite ku Ba-laka chifukwa ati ansembe ankandifuna kuti andithandize. Munthuyu ndi amene anathandiziranso kusintha moyo wanga. Nditabwerera ku Balaka ndinabwereranso ku sukulu. Ndinakafika mpaka ku Namandanje m’boma la Machinga komwe ndinakapitiriza maphunziro a sekondale. Ndili kumeneko ndinaphunziranso zaumekaniki. Ndinka-imbanso mu bandi ina yake kumeneko.

Maphunziro anga ndinafika mpaka foromu 4 ndikukhoza mapointi abwino maka mukaganizira kuti ndinakhala nthawi yaitali ndisali ku sukulu. Ndapangakonso maphunziro a zamanja ku TEVET. Choncho ndikhoza kunena kuti mkalasi ndidalowamo ndithu. Luso la ntchito zamanja liripo kwabasi.

Kuti mudziwike kwambiri chidachititsa ndi chani?

Ambiri adandidziwa chifukwa choimba – ndimakonda kuimba chamba cha jazz. Ndimatha kukaimba mmalo osiyanasiyana monga m’mahotela ndi malo ena achisangalalo. Komanso ntchito zanga zamanja monga kukonza ma makanema (television sets), ma firiji, galimoto komanso makina osiyanasiyana zathandiza kwambiri kuti dzina langa lipite patali.

Mussa: Kukonza makina osindikizira nyuzipepala ku Montfort Media ku Balaka

Mwa chitsanzo, kuti ndikadziwe kunja kwa dziko lino ndi chifukwa cha luso langa lokonza makina oziziritsa mu chipinda, ma air conditioner. Ndikukonza makinawa pa chipatala cha Balaka anthu adayamba kundidziwa nkumandipatsa ntchito. Ndinapezeka kuti ulendo wina ndikukonza makina oziziritsa ku nyumba yachisoni pa chipatala cha Machinga ku Liwonde ndinalandira foni yoti ndikakonze makina odzidziritsa chipinda chosungiramo zinthu kuti zisaonongoke, chija pachingerezi amati cold room ku malo a asilikali a Kamuzu Barracks ku Lilongwe. Uku ndikumene kunatsegula mwayi wanga wokaona m’maiko ena muno mu Africa monga ku DRC, Burundi, Kenya, Tanzania, Rwanda, Namibia ndi Nigeria.

Kunalinji ku maikowa?

Oho, chimene chinachitika ndi choti ndinayamba kugwira ntchito ku malo a asilikali kukonza zinthu zosiyanasiyana. Choncho ndinachita mwayi wopita ku Congo (DRC) komwe kuli asilikali athu othandiza kubweretsa mtendere kumeneko.   Ndinapemphedwa kupita nawo kumeneko osati ngati msilikali koma wothandizira kugwira ntchito zina ndi zina.

Apa ndi pomwe ndinachita mwayi woyendanso mmaiko nda-tchula aja. Kumenekonso nda-gwira ntchito zogwirizana ndi luso langa ndipo anthu amanditayira kamtengo.

Nde mumakwanitsa bwanji kuchita zonse mwanena zija? Nokha kukonza galimoto, makina, kuimbanso mbali inayi?

Choyamba ndimathokoza Mulungu chifukwa chondipatsa maluso ochuluka chotere. Chachiwiri ndi choti ukakhala ndi mwayi wotere umayenera kugawa bwino nthawi yako. Ukuyeneranso kugwira ntchito yako mwachilungamo, mosanamiza anthu. Umisiri woterewu umafuna kugwira ntchito mwaukadaulo. Sidzifunika kukhumudwitsa makasitomala. Izi ndi zomwe ine ndimachita.

Ikakhala nthawi ya zoimbaimba ndi chimodzimodzinso. Umayenera kugawa nthawi moyenerera. Kaya ndikufunika ku studio kuti ndikajambule nyimbo, ndiyenera kufika mu nthawi yake ndi kuthandiza kasitomala. Pa zonse chofunika ndi kuthokoza Mulungu zinthu zikamatheka chonchi.

Pali ambiri amene akukhalabe m’misewu nkumapempha, nkumachita maganyu monga munkachitira inu. Muwapatse uthenga wanji?

Anawa asamataye mtima. Chachikulu ndi kudziwa chimene ukufuna pa umoyo wako. Amene angakwanitse kupita ku sukulu atero ndithu. Alipo ambiri misewumu amene akupempha komanso kusowa pogona koma amachita izi chifukwa akusowa mtengo wogwira. Patakhala anthu akufuna kwabwino awatole anawa nkuwapititsa kusukulu. Ena mwa ana aja ndi anzeru ndithu ndipo akhoza kuthandiza pa ntchito yotukula Malawi ataphunzira.

Ine amene ndi umboni wo-kwanira kuti mwana wovutika ata-peza mpata wophunzitsidwa bwino akhoza kukhala munthu wosinthika waphindu. Lero ndikupanga zinthu zambiri zodabwitsa kwa ena chifukwa ansembe a Mpingo wa Katolika aja ndawatchula aja adachita chotheka kuti ndiphunzire. Anthu ena akufuna kwabwino achitenso izi kwa ana amene angoyendayendawa. In e ndikukwanitsa kupanga ntchito zoti mwina bwenzi kukubwera anthu akujakuzagwira ndikanapanda kuphunzitsidwa zimenezi.

Mawu omaliza.

Kwa amene akundidziwa m’me-ne ndinalili kale akuyenera kudziwa tsopano kuti ndine munthu wosinthika. Siinenso uja ankamudziwa kale akusowa zochita mu m’misewumu. Pano ndine mmisiri wogwira ntchito zosiyanasiyana ndi wodziyimira payekha. Asama-ndiderere chifukwa nyengo zanga zinasintha. Kwa anzanga achinyamata amene aka-khala mmavuto amaona dziko latha ndikufuna kuwauza kuti asamataye mtima. Ndizotheka kusinthika ndi kukukhala munthu wodalilika pa mudzi kaya pa banja.

Ine chikhale chitsanzo chosintha ena kuti kuchokera pa mwana wotoledwa nkudzafika pa mmisiri wokonza galimoto, woimba, kukonza mashini osiyanasiyana komanso kukhala munthu wodalilika pa mudzi ndi zinthu zotheka komanso zochitika.