Wapampando wa mabungwe ku Balaka alonjeza zakupsa

Wolemba: Precious MSOSA

Wapampando watsopano wa mabungwe omwe siaboma ku Balaka a John Bamusi ati iwo achita chotheka kuwonetsetsa kuti nzika za m’bomali zikulandira zitukuko zowapindulira monga kukhala ndi madzi komanso misewu yabwino.

A Bamusi omwe anasankhidwa pa tikiti ya bungwe lomwe amagwirako ntchito la Foundation for Civic Education and Social Empowerment (FOCESE) anati kwa nthawi yayitali adindo makamaka akulu akulu aku khonsolo akhala akutayirira pa udindo wawo wowonetsetsa kuti anthu a m’bomali akulandira zinthu zowakomera.

Mwachitsanzo iwo anatchula nkhani ya misewu komanso madzi ngati zina mwa zinthu zomwe adindo sakumazilabadira.

Bamusi: Adindo asamatayilire pa chitukuko

“Kuti Balaka akhale ndi zitukuko zolozeka, pakuyenera kukhala mgwirizano wamphamvu wa mabungwe omwe siaboma. Mgwirizano wa mabungwe womwe utha kumaphunzitsa anthu akumudzi momwe angamalondolozere zitukuko. Mabungwe omwe angamathe kumawunika momwe khonsolo ikugwirira ntchito zake. Ndizomvetsa chisoni kuti misewu ya m’boma lino inasanduka maenje chifukwa chakulekereredwa,” anatero a Bamusi.

Iwo anati mu zaka ziwiri zomwe akhale pa mpandowu, awonesetsa kuti anthu akhale ndi mphamvu zomafikira adindo ngati akulephera kukwaniritsa zitukuko zina ndi zina. Iwo anati iyi ndi njira yokhayo yomwe adindo angamachilimike potumikira anthu.

A Bamusi anafotokozanso kuti utsogoleri wawo uwonesetsa kuti nkhani za ziphuphu ndi katangale zisapeze gawo pa ntchito ya zitukuko.

Koma iwo anati mgwirizano wawo wa mabungwe kuti ukhale wa mphamvu, anthu akuyenera  kugwira nawo ntchito.

Pamenepa iwo anawunikiranso kuti a khonsolo asamawatenge iwo ngati adani awo koma kuti ngati abwenzi ofuna kupititsa patsogolo chitukuko m’bomali. A Gama atenga utsogoleriwu kuchokera kwa a Charles Sinetre omwe malingana ndi malamulo samayenera kuyimanso.