Young Generation siyiteranso

Wolemba: Victor SINGANO Junior, Mtolankhani Wapadera

Gulu loimba nyimbo za chamba cha Reggae la Young Generation lati lamereranso nthenga ndipo mmene lawulukiramu ilo siliteranso chifukwa liwonetsetsa kuti nthengazi zisasosokenso.

Gululi lomwe langotulutsa kumene chimbale chatsopano cho-mwe mutu wake ndi ‘Africa Rise’ lauza Mkwaso kuti liri ndi chikhumbokhumbo choonetsetsa kuti labwenzeretsa chikoka chomwe anthu analinacho mu zaka zammbuyomu. Chimbale chatsopanochi mukupezeka nyimbo zokwana khumi ndi zitatu (13).

Amene amayang’anira gululi Felix Mzilahowa wati pali chikonzero choti zochitika za gululi monga kutulutsa zimbale pafupifupi, kukonza madansi, kutsegulanso magulu omwe anthu okonda gululi amatha kumatsatira zochitika zake mmasamba a mchezo monga Facebook, Website komanso WhatsApp.

Young Generation: Tibweretsa chikoka chakale

“Ngati mungakumbukire bwino, gululi linayamba zaka za mma 1980  ndi a Salim Khan koma patapita ka-nthawi linayima ndipo linadzukanso mu zaka za mma 2000 momwe tina-tulutsanso chimbale chotchedwa “Afiti Opemphera”.

Pakatipa tatulutsapo zimbale monga ‘Chikondi Chanu’, ‘Chenjezo’, ‘Mudzalira’, ndi china chomaliza Cha ‘Sweet Love’ chomwe chinatuluka mu 2017 koma mu zaka zina sitimakonza zochitika zosiyanasiyana koma panopa tikufuna tiyambeno mwachilendo,” anatero Mzilahowa.

Chimbale cha Africa Rise chikulimbikitsa umodzi, kukweza amayi komanso kulimbikitsa kukhala mmoyo wauzimu.

Pali chiyembekezo choti chifika pamsika miyezi yoyambilira ya chaka chino cha 2021.

Gululi lomwe mmbuyomu linali ndi mamembala osachepera asanu ndi awiri tsopano linasala ndi mamembala atatu omwe ndi Jangis Khan, Zion Khan, ndi Chris ‘Littoh’ Saka.