Mkwaso

AMANGITSA BANJA ATAKHALIRA LIMODZI ZAKA 66

Wolemba: Batholomew Boaz

A Raphael Kabango ndi a Sellina Elia ankaimbira limodzi kwayala. M’chaka cha 1954 awiriwa adapatsana pathupi ndipo adakwatirana. Akhala mu banja losadalitsidwa kwa zaka 66. A Raphael ali ndi zaka 90 zakubadwa pomwe a Sellina sakudziwa zaka zao.

Pamene Bambo John Matiki, wansembe wa ku Parishi ya Utale 1 mu dayosizi ya Mangochi ya Mpingo wa Katolika amayendera akhristu odwala ndi okalamba, adapeza banjali ndi kumva nkhani yao. Bambo Matiki adawalimbikitsa awiriwa kuti amangitse ukwati wao ndipo adavomera.

Pa 14 Febuluwale 2021, pamene anthu amakumbukira tsiku la chikondi ndipomwe Bambo Matiki adamanga banja la a Raphael ndi a Sellina.