Mkwaso

NYAMILANDU WATIPINDULIRANJI KU FIFA

PALIBE TAPINDULAPO-KANJERE

Wolemba: Bartholomew BOAZ


Mkulu wa bungwe loyendetsa mpira wa miyendo m’dziko muno la Football Association of Malaw (Fam), Walter Nyamilandu adakapukusabe
mutu wopanda nyanga kusakhaulupirira kuti wagonja. Akuzifunsabe mafunso kuti chinavuta ndi chiyani kuti agwe pa mpando wa umembala ku khonsolo ya bungwe la FIFA, lomwe limayendetsa mpirawu padziko lonse. Nyamilandu, yemwe wakhala membala wa FIFA kwa zaka zitatu, wagwetsedwa pa mpandowu posachedwapa ndi Pinnick Amaju wa ku Nigeria. Pa chisankho chomwe chinachitikira ku Rabat m’dziko
la Morocco pa 12 Malichi, Nyamilandu anagonja ndi mavoti 43 kwa 8. Iye amapikisana ndi Pinnick anthu ena anayi atalengeza tsiku la chisankholo kuti sayima nawo. Katswiri wolankhulapo pa zamasewero George Kaudza-Masina anati dzanja linali litalemba khoma kuti Nyamilandu saphula kanthu. “Zinaonetseratu kuti mamembala anzake a Cosafa anapanga chiganizo chokavotera munthu wa ku Nigeria zomwe zinamusiya Nyamilandu payekha,” anatero Kaudza-Masina. Kugwa kwa Nyamilandu kukutanthauza kuti wasemphana ndi ndalama
zokwana K16 miliyoni zimene amalandira pakutha pamwezi uliwonse. Wasemphananso ndi mwayi wogona m’mahotela apamwamba akapita ku misonkhano komanso maalawansi ankhaninkhani pansi pa FIFA.

Koma kupatula kuti Nyamilandu wasemphana ndi zonsezi, dziko la Malawi lataya chiyani? Atangosankhidwa m’chaka cha 2018 kukhala membala wa FIFA, James Mwenda amene nthawiyo anali wotsatira
wake ku FAM anati kusankhidwa kwa Nyamilandu chinali chinthu chopambana ku mpira wa dziko lino. “Tipindula kwambiri osati ngati FAM yokha komanso ngati dziko lonse,” anatero Mwenda. Ndipo chiyembekezo cha anthu okonda mpira m’dzikomuno chinalidi chambiri podziwa
kuti udindowu ndiwaukulu. Membala wa FIFA amapanga nao ziganizo zokhudza mpira pa dziko lonse. Nyamilandu wati kugonja kwake kwapangitsa kuti dziko lino litaye mwayi waukulu kumbali ya masewero a mpira. “Tinali ndi zaka zitatu zimene Amalawi tadyerera. Kugonja kwanga ndiye kuti Amalawi taluza. Pamene ndinali membala wa FIFA zambiri tinachita muno m’Malawi,” anatero Nyamilandu. “Ndinayambitsa Nyamilandu Football Academy, ndalama za Covid-19 zinabwera ndipo tinazigawa bwinobwino. Mapulojekiti a Chiwembe anamalizika, zambiri tinachita,” anapitiriza Nyamilandu. Ndipo mtolankhani wa masewero pa wailesi ya kanema ya TV
Islam, Yasin Limu, wagwirizana ndi Nyamilandu kuti mwayi umene umabwera ku Malawi chifukwa choti kunali Nyamilandu sumabweranso.
“Nyamilandu atasankhidwa ku FIFA timu ya Flames siimavutika ndalama ngati m’mene zimachitikira m’mbuyomu ndiye tivutika
kwambiri. Zangovuta kuti zatero koma zimenezi zibwenzeretsa m’mbuyo mwayi wambiri,” anatero Limu. Koma Limu wadzudzula Nyamilandu posafuna kugwiritsa ntchito boma pamene amakonzekerachisankhocho kuti limuthandize kuchita kampeni.

Naye mkonzi wa zamasewero pa wailesi ya MIJ FM, Deitrich Friedrich, anati dziko lino lapindula kwambiri kumbali ya mapulojekiti osiyanasiyana omwe achitika. “Mapulojekiti ena timakhala oyambirira kulandira ndi ife kuno ku Africa chifukwa choti Nyamilandu anali membala wa khonsolo motero amamuganizira asanapititse pulojekitiyo kwina,” anatero Friedrich. Koma mkhalakale pankhani za masewero Peter Kanjere wati
Nyamilandu anangokwanitsa kukweza mbiri yake pokhala pa mpando wa umembalawo. “Sindikukhulupirira kuti pali chinthu ch ooneka chimene tinganene kuti Malawi yapindula pokhala ndi m’Malawi ku FIFA. Tikakamba ndalama za Covid-19 zimaperekedwa ku dziko lirilonse
osati ku Malawi kokha,” anatero Kanjere. Naye Joy Khakona wa Yoneco FM wati palibe phindu limene laoneka ku dziko lino kupatula
kuti “wapindula ndi mwini wakeyo”. “Phindu lomwe tinaliona ndiloti dziko lathu lidayikidwa pa mapu chifukwa cha umembala wa Walter ku FIFA. Koma timayembekezera kuti tigwiritsa ntchito mwayiwu kuti mpira wathu utukuke zomwe sizinachitike. “Akanagwiritsa ntchito mwayi
wokhala ku FIFA kuthandizira kupeza njira zolimbikitsira maphunziro aaphunzitsi, oimbira, kuugulitsa mpira wathu ndi zina zambiri koma sizinatero. Ngati pali phindu lenileni linali lake, motero tingati sitinapindule ndi umembala wake,” watero Khakona. Kukhala membala wa FIFA unali mwayi woti Nyamilandu akanathandiza dziko la Malawi kuchita maubale ndi maiko ena pankhani ya mpira. Koma mpakapano Flames ikulepherabe kupeza matimu abwino oti asewere nao masewero apaubale. Nyamilandu adasankhidwa pa mpandowu m’chaka cha 2018 atagwetsa namandwa pankhani za mpira wa ku South Africa Dr Danny Jordaan ndi mavoti 37 kwa 18.