MkwasoZa Masewero

FLAMES NDINYAMULE!

Wolemba: Bartholomew BOAZ

Akatswiri ati ntchito idakalipo

Ntchito imene imaoneka yosatheka yatheka. Mtunda womwe umaoneka wosakwereka wakwereka. Mwambi woti awonenji adapha mvuwu ndi mono unapherezera pa 29 Malichi pamene timu ya Flames inakwanitsa kutola tikiti yopitira ku mpikisano wa Africa Cup of Nations (Afcon). Flames inagonjetsa timu ya Uganda ndi chigoli chimodzi kwa duu pabwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre. Richard Mbulu, amene akusewera mu timu ya Baroka FC ku South Africa, adalumpha m’malere ngati wanyamulidwa ndi angelo mu mphindi khumi ndi
zisanu zam’chigawo choyamba ndikusumba mpira umene adausema Stanley Sanudi chakumanja. Goloboyi wa Uganda, Dennis
Onyango anangozindikira akukatola mpira mu ukonde. Komweko kunali kuzigulira malo ku Afcon 2022 ku Cameroon, kupangitsanso
Amalawi ambiri kudzazidwa ndi chimwemwe chopanda woleletsa. Flames inachita nawo mpikisanowu komaliza zaka 11 zapitazo
ku Angola.

Flames ikanagonja awa analinso masewero omaliza a Meck Mwase amene kontirakiti yake inatha kale mu Januwale ngati mphunzitsi wa timuyi. Flames imangoyenera kupambana masewerowa mwa njira iliyonse koma sizinali zophweka. Papepala
Uganda ndi imene inali timu yabwino. Mu mpikisanowu Flames inali itagonjetsedwa 2-0 pamasewero omwe anakachitikira ku
Kampala. Ndipo m’mikumano 31 ya matimu awiriwa, Uganda inali itapambana ka 15 ndipo Flames inali itagonjetsapo Uganda kasanu
ndi katatu basi. “Palibe amene anaipatsa mwayi Flames potengera mavuto amene yakhala ikudutsamo,” anatero katswiri pankhani zamasewero Higger Mkandawire. M’masewerowa timuyi, yomwe inachuluka ndi anyamata achisodzera imaoneka yodzikhulupirira
m’maseweredwe ake komabe malo ena amaperewera. Vuto lalikulu limaoneka pakati pomwe pakuoneka kuti pakuyenera kukonzedwa bwino komanso kumbuyo chakumanzere ndi kutsogolo. Potengera mbiri, Flames yakhala chithumba chongokutumulidwa. Yakhala ikungosinthasintha aphunzitsi ndi osewera posadziwa choyenera kuchita.

Chichokereni ku Afcon ya 2010 ku Angola, Flames yakhala ikulemba ntchito azungu ngati aphunzitsi ndicholinga choti ikafike ku Afcon, koma sizinaphule kanthu. Mkonzi wankhani zamaseweroku Times Group, Pilirani Kachinziri anati timuyi isatambalale chifukwa ati ulendo wangoyamba. “Ntchito idakalipo yayikulu. Ku Afcon kumapita matimu amene ndi abwino okhaokha ndipo tikuyenera kupeza osewera amene angaigwire ntchito kumeneko,” anatero Kachinziri.


“Tikuyenera kukonzekera mokwanira. Ndipo tisamve wina akuti akufuna kulemba ntchito mphunzitsi wakunja ayi. Timusiye Meck yemweyu aipitirize timuyi ndipo angopatsidwa zinthu zomuyenereza kugwira bwino ntchitoyi,” anatero Kachinziri pa pologalamu ya Times 360.
Aka ndi kachitatu kuti Flames ifike ku mpikisano wa Afcon. Idachita zimenezi m’chaka cha 1984 mphunzitsi ali malemu Henry Moyo, m’chaka cha 2010 timuyi ikuphunzitsidwa ndi Kinnah Phiri. Ndipo pano ndi timu imodzi mwa matimu atatu kuno kummwera kwa Africa amene
akwanitsa kudzigulira malo. Ena awiri ndi Comoros Islands komanso Zimbabwe pamene matimu omwe amafikafika ku chikhochi monga Zambia ndi South Africa agwa nayo. Flames yamaliza pa nambala yachiwiri itapeza mapointi asanu.