MkwasoZa M'dziko Muno

KHANSALA ASOWETSA MALATA

Sindinabe – Cosmas

Akuti amamva zayekha

Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA

Ntchito zachitukuko mu Wodi ya Mlomba, m’boma la Machinga, zayamba zaima kaamba koti khansala wa derali a Alexander Cosmas, anathawa poopa anthu olusa amene akufuna kuti khansalayu abweze malata makumi anayi (40) achitukuko omwe anasowetsa. Malatawo anali othandizira kukonzera nyumba za aphunzitsi pa sukulu ya pulayimale ya Wataka m’bomalo. Anthu a m’derali ati a Cosmas, omwe
anathawa ndipo akukhala kwa Jenda m’boma la Mzimba, akulephera kulongosola komwe anapititsa malatawa. Nyuzipepala ya Mkwaso
yapeza kuti khansalayu anamangidwapo chifukwa cha nkhaniyi ndipo nkhaniyi ili ku khoti ku Machinga. Ngakhale a Cosmas anatsimikizira nyuzipepalayi zakumangidwa kwawo iwo anakana zoti anaba malatawo. Anthu omwe anatsina khutu mtolankhaniyu koma anapempha
kuti asatchulidwe maina awo, anati khansalayu anathawa mu Januwale chaka chino ataona kuti zinthu zafika povuta. “Khansalayu wakhala akuchita utambwali pankhani ya chitukuko zomwe zachititsa kuti anthufe timulusire. Chaka chatha kutachitika ziwonetsero (zokhudza nkhani yovala mahijabu) pa sukulu ya Wataka, zinthu zinawonongeka. Ndipo nyumba za aphunzitsi zikukonzedwa kunapezeka kuti kunasowa malata 40 omwe sitinakayikire kuti khansalayu anatenga. “Ngakhale anatiuza kuti anakasungitsa katundu yense ku parishi ya Nsanama, kafukufuku wathu anasonyeza kuti atakasiyidwa malatawo khansalayu anapita mwanseri kukatengako yekha,” anatero mmodzi
mwa anthu a m’deralo. Zimenezi ati zinachititsa anthu kukamumangitsa khansalayu. Malatawa anagulidwa ndi ndalama zachitukuko za District Development Fund (DDF). “Khansalayu samamva za munthu ndipo ubale wake ndi makomiti achitukuko, mafumu ndi ena siwabwino. Anthu okwiya anamupatsa makofi chifukwa salabadira mavuto omwe tikukumana nawo m’dera lino. “Chimene chikutiwawa kwambiri ndi chotibera katundu wa chitukuko chomwe chikanatipindulira. Munthu wa mtundu wanji wobera anthu omwe amawaimira?”
anadandaula wina. A Cosmas anavomereza kuti anthu a kudera lawo anawamangitsa kaamba kowaganizira kuti anaba malata omwe ankayenera kugwira ntchito ya chitukuko. “Zambiri sindingayankhule chifukwa nkhaniyi ili ku khothi komanso m’manja mwa oweruza
milandu omwe akuyiyendetsa kuti chilungamo chiwoneke,” anatero a Cosmas. Koma a Cosmas anati anachoka ku dera kwaoko pofuna
chitetezo chifukwa ati nthawi zambiri amanyozedwa pagulu ndi mafumu ena a deralo zomwe ati sizimawasangalatsa komanso
akuti pamakhala kukondera pochita zinthu zina ku derali. “Mafumu omwe sindiwatchula maina awo, amawoneka kuti samasangalala kuti ndinapambana chisankho chifukwa yemwe ankamufuna potengera chikhalidwe ndi zikhulupiriro zawo anagonja. “Chifukwa cha chimenechi,
sandipatsa ulemu komanso anawuza madera ena kuti asamabwere ku mikumano yanga. Mwa chitsanzo, komiti yoyendetsa sukulu ya Wataka yakhala isakukumana nane kuti tigwire ntchito limodzi yokonzanso sukuluyi mpaka pano,” anatero a Cosmas. Iwo anati nyumba yawo ili ku derako ndipo amapita ku khonsolo kukakhala zochitika koma akamaliza msonkhano wawo amabwerera ku Mzimba komwe ati akukhala mwaufulu komanso mosalimbana ndi munthu. “Chomwe ndingakuwuzeni, mu 2025 sindidzayimiranso dera limene lija chifukwa kuli anthu okanika, ofuna munthu azichita zomwe iwo akufuna osati khansala kuwawuza zinthu ayi; makamaka mafumu ndi ena,”
anatero a Cosmas. Iwo anati anadziwitsa kale bwanamkubwa wa boma la Machinga komanso a ku Unduna wa Maboma Aang’ono za kusamukako kaamba koti chitetezo chawo ati chinali pa chiopsezo. “Ngakhale Masauko Chipembere anathawa m’dziko muno chifukwa moyo wake unali pa chiopsezo. Nanenso ndangosuntha kuchoka ku Machinga kubwera kwa Jenda kufuna chitetezo komanso kuti moyo wanga usakhale pa chiopsezo,” anapitiriza a Cosmas. Mkulu wa khonsolo ya Machinga, khansala Simple Diwa anati kalata yomwe a Cosmas
analemba siinawapeze koma nkhani yawo ati akuyidziwa chifukwa anawafotokozera. “Nkhani yakuchoka kwawo anandiuza komanso ngati khansala mnzanga yemwe ndikugwira naye ntchito dera limodzi ndinamukhazika pansi ndi kumuwuza kuti asachoke kukakhala kutali.
“Pamakhala zinthu zina zofunikira zadzidzidzi zomwe zimafunika khansala azione mwachangu zomwe zingatheke ngati ali m’dera lomwelo osati kutali ngati kwa Jenda,” anatero a Diwa. Iwo anati kusamvana kwa khansala, mafumu, phungu ndi makomiti achitukuko kunayamba kalekale ndipo zikukhala zovuta kuti zinthu ziyende chifukwa adindowa sakulumikizana pochita zinthu. “Sungapange chitukuko popanda
kudziwitsa mafumu, phungu ndi komiti ya chitukuko chifukwa omwe amadziwa koyenera kupita chitukuko ndi anthu osati khansala yekha ayi,” anatero a Diwa. Iwo anatsimikizanso kuti a Cosmas anamangidwa kaamba ka nkhani ya malata omwe akuwaganizira kuti anasowetsa.
A Diwa anati ndi zosokoneza khansala kumakhala kutali ndi anthu ake chifukwa ati phungu amadalira khansala pantchito ya
chitukuko. Mneneri ku Unduna wa Maboma Ang’ono, a Anjoya Mwanza, anati afufuze ngati kalata ya kuchoka kwa a Cosmas ku dera lawo inafika ku undunawu. Mmene timasindikiza nkhaniyi nkuti asanatsimikizire kuti kalatayo analandira kapena ayi.