MkwasoNkhani Zina

Montfort Media ikhazikitsa buku la malemu Nga Mtafu

Wolemba
Joseph KAYIRA

Dzina la Dr. Andrew George Nga Mtafu silachilendo kwa Amalawi ambiri. Mkuluyu anali dotolo woyamba wowona matenda amu ubongo m’dziko muno atachita maphunziro ake m’dziko la Germany. Komanso ambiri akulikumbukira dzina la Andrew George Nga Mtafu ngati phungu wa Nyumba ya Malamulo woyamba wa pazilumba za Chizumulu ndi Likoma. Mkuluyu anakhalaponso nduna ya boma ndikugwiranso ntchito zosiyanasiyana mu boma.

Mkulu yemwe amatchuka kuti Nga Mtafu anamwalira atachita ngozi ya galimoto mchaka cha 2015 mu mzinda wa Blantyre ndipo m’mene ngoziyi inkachitika nkuti iwowa atalemba buku ndipo anali akukambirana ndi kampani yosindikiza mabuku ya Monftort Media ku Balaka kuti awasindikizire buku lawo lomwe likusimba za umoyo wawo ndipo mutu wake ndi Notes and Life Sketches.

Patapita zaka, loto lawo lapherezera bukuli litasindikizidwa ndi a Montfort Media. Pa mwambo womwe unachitika Lachitatu pa 29 Disembala 2021, pa hotela ya Malawi Sun mu mzinda wa Blantyre anthu anayamikira malemu Mtafu chifukwa cholemba buku la moyo wawo kaamba koti anthu ambiri aphunzirapo kanthu pa zomwe atulutsa mu bukuli pa umunthu, chikhalidwe cha Amalawi maka a mtundu wa Chitonga, maphunziro, ndale ndi zina.

Sikawirikawiri kuona akuluakulu omwe anakhalapo nduna, phungu wa Nyumba ya Malamulo kapena maudindo ena akulaukulu m’boma kulemba buku lofotokoza mbiri yawo. Mwina amakhala ndi zifukwa zawo. Pakali pano pali maganizo oti aliyense yemwe wakhalapo pa udindo waukulu m’boma monga pulezidenti, nduna ya boma ndi ena, ayambe kulemba mabuku kufotokoza mbiri yawo komanso zokhuza ntchito yomwe anapatsidwa m’boma. Akuti izi zikhoza kuthandiza kuti obwera m’mbuyo mwawo akwaniritse kugwira ntchito yonga yomweyi mosavuta komanso mwaukadaulo. Mbiri ya dziko, malo antchito kapena munthu akuti ndiyofunika kwambiri pa chitukuko.

A Maureen Masamba, omwe ndi pulezidenti wa Book Publishers Association of Malawi (BPAM) akuti nkofunika kukhala ndi lamulo lokakamiza akuluakulu ogwira ntchito za boma kulemba ndi kusindikiza mabuku.

“Izi zizathandiza kuti akuluakuluwa azitha kugawana nkhani ndi anthu omwe amawatumikira. Nkofunika kuti, ngati dziko, tikhale ndi mfundo ndi ndondomeko zoyenerera kuchokera ku mabuku omwe angasindikizidwe ndi akuluakulu omwe agwirapo ntchito zotumikira anthu. Izi zingazathandize kuti mtsogolo muno tisamabwereze zolakwika zomwe zinachitikapo m’mbuyomu,” akutero a Masamba.

Iwo anayamikira malemu Mtafu polemba buku lomwe akuti muli maphunziro ochuluka opita kwa Amalawi.

“Kwa anthu olembafe, palibe chinthu chonyaditsa monga kukhazikitsa buku lomwe unalemba. Kwakukulu tithokoze makampani monga Montfort Media amene amakhala patsogolo kugwira ntchito ndi anthu olemba monga m’mene anachitira ndi malemu Mtafu. Montfort Media siinatsogoze ndalama koma chidwi pofuna kudzamitsa mbiri ya dziko lino. Pa ichi tikuti zikomo kwambiri,” akutero a Masamba.

Pamene a Montfort Media akangalika kuthandiza alembi pofuna kuti mbiri ya dziko lino isafe, ngakhale kampaniyi nayo ikudutsa mu nyengo zovuta pachuma, Dr Edge Kanyongolo, yemwe anali mlendo wolemekezeka ku mwambo wokhazikitsa buku la a Mtafu, akuphera mphongo kufunika kolemba ndi kusindikiza mabuku a mbiri ya dziko lino.

“Poyamba tivomereze kuti sichinthu chapafupi kusindikiza mabuku. Tikudziwanso kuti tikasindikiza msika wake ndiovutirapo koma a Monftort Media sanakhumudwe chifukwa kwa zaka zambiri akhala akugwira ntchito imeneyi kuthandiza alembic ochuluka. Lero ndi awa asindikiza buku la malemu Mtafu lomwe ndi lofunika kwambiri. Ife tikuti zikomo kwambiri posafooka pa ntchito yanu,” akufotokoza a Kanyongolo.

Iwo akuti ndi cholinga chawo kuona Amalawi akulemba kwambiri mbiri ya dziko lawo kaamba koti akapanda kutero “adzabwera anthu ena akunja omwe adzalembe mbiri ya Malawi koma moti iwakomere olembawo.”

A Kanyongolo akuti olemba oterewa kawirikawiwiri salemba mwa chilungamo nchifukwa chake kuli kofunika kutenga mwayi umene a Montfort Media apereka nkusindi-kiza mabuku a mbiri ya Malawi moona mtima komanso mu njira yopindulira Amalawi.

Pokambapo za buku la a Mtafu, iwo anati mkuluyu anaonetsa kukonda dziko lake, kupilira komanso kulimba mtima pa nthawi yomwe ndale za mdziko muno za chipani chimodzi zinali zovuta kwambiri. A Mtafu anamangidwapo ndikukakhala ku ndende zaka zambiri.

“Tangoganizani kuti anapita ku Germany kukaphunzira zachipatala mchilankhulo cha kumeneko ndikuchita bwino. Iwo anabwerera kwawo ku Malawi kuzatumikira dziko lawo koma monga tikudziwa anamangidwa ndi boma la nthawi imeneyo nkuponyedwa mu ndende. Izi zinali zowawa kwambiri kwai wo ndi banja lawo.

“Tikawerenga buku lawo tiona kuti a Mtafu anali munthu woganiza mofatsa mosaopa kanthu. Analemba buku lawo ndi kulongosola zonse zimene anakumana nazo pa moyo wawo osabisa kanthu. Komanso mbiri yawo ikuonetsa kuti iwo anali munthu wokonda dziko lawo. Amalawi akusowa mabuku monga limene analemba a Mtafu,” akutero a Kanyongolo.

Zinayamba bwanji?
A Viva Nyimba, omwe ndi majisitiliti wamkulu wa makhoti, mu mzinda wa Blantyre komanso yemwe ndi bwenzi la banja la a Mtafu, akuti anawadziwa a Mtafu ali wachiche-pere. Iwo akuti amawatenga a Mtafu ngati munthu yemwe ankamusirira ali pa sukulu ya pulaimale.

“Ndinawasankha a Mtafu kuti akhale munthu yemwe azindilimbikitsa pa maphunziro. M’menemo nkuti ndili ku pulaimale sukulu. Zaka zimenezo maphunziro timawatenga ngati chinthu chapamwamba kwambiri mwina kuposa m’mene zikukhalira masiku ano. Choncho kuchita bwino pa maphunziro kwa a Mtafu kunandilimbikitsa kwambiri,” akutero a Nyimba.

Mkuluyu akuti aatdzakumana ndi Mtafu nthawi ina yake ndipo akucheza ndi pomwe iye anawalimbikitsa kuti alembe buku. A Nyimba akuti a Mtafu sanavute koma kugwirizana nawo pa zakufunika kosindikiza buku ya mbiri yawo.

Iwo anati ndi wokondwa kuti mbiri ya malemu Mtafu tsopano ili mu buku lomwe lipindulire Amalawi ambiri chifukwa muli maphunziro ambiri.

Dr Levi Zeleza Manda, omwe ndi mkonzi wa bukuli akuti atakumana koyamba ndi a Mtafu mu mzinda wa Blantyre pa zosindikiza bukuli, iwo anali ndi chidwi kuti awone mbiri ya mkuluyu.

Iwo atapatsidwa zomwe a Mtafu analemba koyamba, anali odabwa kuti zomwe ankadziwa za Mtafu zinali zosiyana kwambiri ndi zomwe mwini buku anazitulutsa poyera. Mwachitsanzo, anthu ambiri amawadziwa a Mtafu ngati munthu yemwe analankhula mawu mu Nyumba ya Malamulo oti “agalu inu” kukhala ngati kunyoza akumbali ya boma mu Nyumbayo. Koma chilungamo chake chinali choti wolembawo anangosankha pokhapo, chonsecho mawuwa anatuluka chifukwa phungu wina mu Nyumbayo anawanena a Mtafu kuti aphedwa kaamba ka mkangano womwe unabuka pakati pa otsutsa ndi a mbali ya boma.

A Manda akuti buku la a Mtafu latulutsa zoona pa nkhani zomwe Amalawi anali ndi maganizo opotoka. Mwa zina, a Manda akuti atawerenga bukuli koyamba, anaphunzira zinthu zambiri zomwe poyamba sankazidziwa konse.

“Nditawerenga bukuli ndinawauza malemu Mtafu kuti sindikusowa kuti andilipire chifukwa zomwe ndinawerenga m’bukuli anali malipiro kale,” anatero a Manda.
Atalikonza bukuli ndi kulipereka kwa a Mtafu kuti alikonze ndi pomwe mkuluyu ankachita ngozi ya galimoto. Patatha zaka ndipo ganizo la bukuli litayambikanso ndi pomwe a Manda anapatsidwanso bukuli kuti alikonzenso. Apa ndi pomwe iwo anazindikira kuti zomwe anakonza poyamba zija sizinasinthidwe; choncho anagwiranso ntchitoyi kawiri.

“Nanenso ndikufuna ndigwirizane ndi amene akunena kuti akuluakulu ayambe kulemba mabuku. Lembani, lembani, lembani. Buku la a Mtafu litipatse mtima wofuna kugawana ndi ena mbiri ya dziko lathu komanso zomwe ife takumana nazo zomwe zingathandize kusintha dziko lathu kuti likhale lokomera tonse pa ndale kapena pa chitukuko,” akutero a Manda.

Montfort abweretsa chiyembekezo
Bambo Blaise Jailosi, omwe ndi mkulu woyendetsa ntchito za Montfort Media akuti ndi wokondwa kuti ntchito yomwe inayamba m’mbuyomu, nkuima kaamba ka imfa ya a Mtafu, tsopano yatheka. Iwo akuti buku la a Mtafu liri ndi mbiri yabwino yomwe ikhoza kuthandiza pomanga Malawi watsopano yemwe takhala tikumufuna chitengereni ufulu wodzilamulira.

“Malemu Mtafu atatipeza ku Montfort Media pa nkhani yosindikiza buku lawo ife tinali ndi chisangalalo. Tili kale ndi dongosolo ndi ndondomeko yosindikiza mabuku andale ndi ena ndipo buku la a Mtafu ndi limodzi mwa ambiri omwe tasindikiza kale,” akutero Bambo Jailosi.

Bambo Jailosi akuti nkhani yomwe ili mu buku la a Mtafu ndiyochititsa chidwi ndipo ndiyofunika kuti Amalawi ambiri ayiwerenge pogula bukuli limene likupezeka m’mabukushopu a Montfort Media m’maboma ambiri.

Iwo akuti a Montfort Media ndiokonzeka kutukulana ndi alembi osiyanasiyana ndipo apempha boma, makampani, mabungwe omwe siaboma ndi ena amene ali ndi chidwi pa nkhani yonsindikiza mabuku kuti agwirane manja ndi a Montfort Media posindikiza mabuku ophunzitsa mtundu wa Malawi.

Mabuku ena omwe a Montfort Media asindikiza mu ndondomeko yomwe akuitcha kuti Malawi Political History Series (Lest We Forget) ndi monga: Political Prisoner 3/75 lolembedwa ndi malemu Sam Mpasu; Justified by Faith lolembedwa ndi Angela Hanley; Living Dangerously [A memoir of Political Change in Malawi] lolembedwa ndi Padraig O Maille; Suffering in Silence lolembedwa ndi Emily Mkamanga; Malawi a Turning Point lolembedwa ndi Trevor Cullen; Malawi’s Lost Decade lolembedwa ndi Adamson Muula ndi Emmie Chanika; Malawi’s Presidents lolembedwa ndi Okomaatani SL Aipira komanso Nankumba Peninsula lolembedwa ndi Okomaatani SL Aipira.

A Montfort Media amasindikizanso mabuku osiyanasiyana pa maphunziro, zaumoyo, zaulimi, zipembedzo, chikhalidwe ndi zina zambiri. Iwo amasindikizanso nyuzipepala, magazini ndi zina.