Uncategorized

Ku ndende sikothera

Wolemba
Precious MSOSA


Anthu ambiri m’bale wawo akagamulidwa kuti akagwire ukaidi ku ndende amakhala ndi nkhawa ndinso okhumudwa kwambiri. Izi ndizomveka makamaka poganizira momwe moyo wa ku ndende za mdziko muno umakhalira.

Ambiri akakhala kuti akukayamba moyo wa ku malo amenewa sakhalanso ndi chiyembekezo choti atha kudzakhalanso anthu ofunikira ku dziko, kwa iwo amangowona ngati zawo zada ndipo palibenso chiyembekezo chilichonse. Mwachidule titha kunena kuti amangoti ‘kwanga kwatha.’

Koma zonsezi zitha kukhala mbiri yakale ngati pologalamu yomwe bungwe la DVV International linayambitsa ku ndende yayikulu ya Zomba itafalikira mu ndende zambiri. Bungweli mothandizana ndi bungwe la Centre for Human Rights Education Assistance and Advice (CHREAA) akuphunzitsa ena mwa akaidi a pa ndendeyi ntchito za luso la manja monga za ukalipentala, kumeta tsitsi ndinso kusoka zovala kudzera mu pologalamu yotchedwa Maphunziro a akaidi mu ndende (Adult Learning and Education (ALE) in Prisons Programme).

Malingana ndi wamkulu wa bungwe la DVV International a David Harrington, iwo anayambitsa pologalamuyi ndicholinga chofuna kuthandiza akaidi kuti akakhale ndi chosamirapo akatuluka ku ndendeku. Iwo akukhulupilira kuti akaidi akakhala ndi luso lomakapanga ntchito za manja, izi zitha kukawathandiza kusakapalamula milandu ina.

“Choncho ndi chikhumbokhumbo chathu kufuna kuwonesetsa kuti akaidiwa akamatuluka ku ndende azikakhala ndi chochita chothandiza kupeza ndalama monga kusoka zovala, kukhoma zinthu zosiyanasiyana ndinso kumeta tsitsi. Ichi ndichifukwa ife mogwirizana ndi a CHREAA tachilimika kuphunzitsa akaidi a pano pa ndende ya Zomba luso la manja,” anatero a Harrington.

Iwo anati ayesetsa kuwonesetsa kuti moyo wa ku ndende usamangokhala wopanda phindu lililonse kwa akaidi. Choncho pamenepa a Harrington anati achita chotheka kuti ma pologalamu ngati amenewa akuchitika mu ndende zambiri mdziko muno.

“Sitikufuna kuti nthawi yomwe akaidi akhala kuno ingopita pachabe. Tikufuna kumadzachitira umboni kuti anthu omwe akutuluka kuno akukhala nsana-mira ya anthu kunjako podzera mu luso lawo. Ngati DVV, tiyesetsa kulumikizana ndi mabu-ngwe ena kuti tiwonesetse kuti akaidi akupindula ndi moyo wa ku ndende,” iwo anatero.

Mmodzi mwa akulu akulu aku nthambi ya ndende a Dezio Makumba anati ndiwothokoza kwambiri kaamba ka chikonzero chomwe bungweli mogwirizana ndi CHREAA anakhazikitsa pa ndendeyi.

Iwo anati achita chotheka kuti pulojekitiyi ikamadzatha, iwo adzapeze njira zoyipitirizira. Mkuluyu anati akukhulupilira kuti akaidi omwe anachita mwayi kuchita nawo pulojekitiyi akayesetsa kugwi-ritsa ntchito mwanzeru luso lomwe anapeza mmaphunziro osiyanasiyana.

“Kunenea zoona iyi ndi pulojekiti yabwino kwambiri ndipo itha kuchepetsa khalidwe la akaidi ena kukhala akabwerebwere. Kwambiri, zomwe zimachititsa mkaidi kukhala kabwerebwere ndikusowa mwayi wa chinthu chomamubweretsera ndalama pa nyumba pake.

“Koma ndi zikonzero ngati zimenezi, tili ndi chikhulupiliro chonse kuti nkhani ya wukabwerebwere wa akaidi itha kukhala mbiri yakale,” anatero a Makumba.
Iwo anafotokoza kuti maphunzirowa omwe amakhala a pafupifupi chaka chimodzi amakhala a akaidi omwe atsala pang’ono kutuluka. Mwachitsanzo iwo anati akaidi omwe nthawi zambiri akhala ndi zaka ziwiri kuti atuluke ndiomwe amasankhidwa kuchita maphunzirowa.

Ndipo wamkulu wa bungwe la CHREAA a Victor Mhango analimbikitsa akaidi omwe adzichita nawo maphunziro a luso la manjawa kuti adzizindikira kuti apatsidwa mbedza yowathandizira kukawedza nsomba akatuluka.

“Kunjaku sikuli bwino. Ndipemphe amene muzisankhidwa kuchita maphunzirowa kuti mudziyikapo mtima kwambiri chifukwa kunjaku ndiokhawo omwe ali ndi luso la manja omwe akukhala bwino,” anatero a Mhango.

Iwo anati akuzindikira bwino mavuto omwe ali mu ndende za mdziko muno koma iwo ayesetsa kuwamenyera nkhondo kuti zinthu ziyambe kuyenda bwino mu ndendezi.

Pamenepa iwo anati ayesetsa kupempha boma kuti liwonjezere ndalama zomwe limapereka ku nthambi yoyang’anira ndende. A Mhango anati kuchepa kwa ndalamazi kukumapangitsa oyang’anira ndendezi kumagula chakudya chochepa.

“Mu ndende zina akaidi sakumadya mokwanira zomwe ndikuphwanya ufulu wawo. Tichita chotheka kumenya nkhondo kuti ndalama zomwe zimapita ku nthambi ya za ndende zitawunikiridwanso,” anatero a Mhango.

Poyankhulaponso pa katundu yemwe akaidiwa amapanga, a Mhango anati ndizomvetsa chisoni kuti ndalama zomwe zimapezeka akagulitsa katundu yemwe amapanga sizimawapindulira eni ake (akaidi). Iwo anawulula kuti ndalama zomwe zimapezeka akagulitsa katunduyu zimapita ku thumba la boma (Account Number One).

“Izi sizikumayenera kukhala choncho chifukwa akaidiwa akumayenera kumapindula ndi thukhuta lawo. Tinayamba kale kukambirana ndi a komiti yoona za malamulo ya ku Nyumba ya Malamulo ndipo anatitsimikizira kuti izi aziwunika bwino,” iwo anatero.

A Mhango anati boma silikuyikapo kale chidwi pa miyoyo ya akaidi choncho likanawasiyira ndalama zomwe akumapeza akagulitsa katunduyu kuti adziwonera zosowa zawo.

Mmodzi mwa akaidi omwe anamaliza maphunzirowo a Malipiro Chisoni wochokera mmudzi wa Gwaza mfumu yayikulu Kachindamoto anati akuyembekeza kuti moyo wawo ukasinthika kwambiri kaamba koti adzitha kumakachita zomwe aphunzira.

Koma a Chisoni omwe ali ndi ana asanu ndi mmodzi ndipo anaphunzira luso la ukalipentala anati vuto lomwe angakakhale nalo ndikusowa kwa zipangizo zoyambira ntchitoyo.

“Ndikadakonda pulojekitiyi ikanakhalanso ndikuthekera koma-perekanso zida kwa omwe aphunzira luso losiyanasiyana kuti adzikatha kuyambirapo. Kaya utha mgwirizano wapadera kuti zipangizozo zizibwezedwanso pakadutsa miyezi ingapo zitha kukhalabe zothandiza,” anatero a Chisoni.

Ndipo anapitiriza: “Taganizani tikatuluka tikakhala kuti tilibe kalikonse. Kuwonjezera apo anthu ambiri samakhulupilira kweni kweni munthu woti watuluka ku ndende choncho zitha kumakakhala zovuta kupeza mwayi wobwereka ndalama zogulira zida zogwirira ntchito ya luso taphunzira.”

Bungwe la DVV ndi CHREAA linakhazikitsa pulogalamuyi mchaka cha 2020 ndipo kwakukulu ikungowona pa gawo la ntchito za luso la manja. Mabungwe awiriwa anakhazikitsa pulogalamuyi pozindikira kuchepa kwa mwayi wa maphunziro a mtunduwu mu ndende zambiri za mdziko muno.

Pa zaka ziwiri zomwe mabungwewa akhala akuyendetsa pulogalamuyi, bungwe la DVV International lakonza malo ophunzirira pa ndende yayikulu ya Zomba, kugula zipangizo zophunzitsira komanso kuphunzirira mwazina. Ilo linagwira ntchitoyi ndi thandizo lochokera ku unduna woona za mgwirizano wa za chuma wa mdziko la Germany (Ministry for Economic Cooperation and Development- BMZ) komanso CHREAA.