MkwasoNkhani Zina

‘Mu makhonsolo ena muli mavuto’

Wolemba:

Joseph KAYIRA

Nduna ya maboma aang’ono Dr Blessings Chinsinga afotokoza kuti mu makhonsolo ena muli mavuto kaamba ka kuchepekeredwa pa nkhani ya zachuma komanso ngongole zimene makhonsolowa ali nazo. Ndunayi yati boma likuchita chotheka kuti makhonsolawa akhale ozidalira pachuma ngati njira imodzi yothana ndi mavutowa.

Chinsinga: Tigwirane manja

Dr Chinsinga alankhula izi atayendera makhonsolo achigawo chakum’mawa komwe amafuna awone m’mene makhonsolo akuchitira pofuna kusintha zina ndi zina kuti zitukuko ziziyenda bwino m’mabomawa.

“Ndi zoona kuti makhonsolo ena akuvutika pa nkhani ya zachuma. Ena ali ndi ngongole zambiri ndipo akulephera kuti atumikire bwino anthu. Ife ngati boma tikiyesetsa kuti tiwathandize kuti ntchito zawo ziziyenda bwino. Komanso ndi cholinga chathu kuti makhonsolo akhale oziyimira paokha ndikupanga chuma chawo,” anatero Dr Chinsinga.

Iwo afotokoza kuti ngakhale pali mavuto pa ntchito zina zamakhonsolo, ndizosangalatsa kuti makhonsolowa aika kale mapulani omwe atati akwaniritsa kuwapanga azasintha…

Subscribe to mkwaso newspaper and read the whole story

For more information Call: 0886346798 / 0982670335 or

WhatsApp: +265 884 13 57 10

https://web.facebook.com/profile.php?id=100063533438373