MkwasoZa M'dziko

Dalaivala agamulidwa K150,000 poluma wa polisi

Wolemba:

Precious MSOSA

Apolisi apa msewu ngati awa akumakumana ndi nkhanza. (Chithunzi: Internet)

Bwalo lina la milandu mu mzinda wa Blantyre linagamula a Lester Makawa kulipira chindapusa cha K150, 000 chifukwa choluma chala cha wa polisi wa pa msewu zomwe ndikutsutsana ndi gawo 241 (a) la malamulo a buku la milandu.

Malingana ndi wofalitsa nkhani za polisi ya Ndirande a Widson Nhlane, woyimira boma pa milandu a Lyson Chavinda anafotokozera bwalolo kuti a Makawa anapalamula mlanduwu pa usiku wa pa 10 Okutobala chaka chino pomwe amayendetsa galimoto lawo ataledzera. Iwo anati pa nthawiyi apolisiwa anali atapanga malo opangirapo chipikisheni a dzidzidzi pafupi ndi mphambano ya Machinjiri kuchokera mu msewu wa Magalasi.

A Chavinda anafotokozera bwalolo kuti apolisi atayesetsa kukambirana ndi a Makawa, iwo anali mwa uchiwembu ndipo samakambika kotero apolisiwo anammanga ndikupita naye ku…

Subscribe online to Mkwaso newspaper and read the whole story

You can also visit our FaceBook page by simply clicking the link below:

https://web.facebook.com/profile.php?id=100063533438373