Uthenga

Chithandizo chaulele

Ngati njira imodzi yofikira anthu osowa thandizo loyenerera la madotolo pa mavuto omwe anthu osiyanasiyana ali nawo, chipatala cha Pirimiti mu mzinda wa Zomba chakonza m’bindikiro wa chithandizo chaulele kuyambira pa 7 Novembala mpaka pa 17 Novembala. Malingana ndi akuluakulu a chipatalachi, madotolo ochokera m’dziko la Germany ndiamene akuyembekezeka kudzathandiza anthu omwe ali ndi mavuto monga kugawikana kwa milomo monga tikuwonera pa chimodzi mwa zithunzizi, zipsera zobwera kaamba ka kupsa komanso ana omwe ali ndi vuto la mayendedwe (club foot). Kwa omwe akufuna kukalandira thandizoli atha kuyimba foni pa manambala awa kuti alembetse 0887 366 698 ndi 0881 138 644. Wolemba: Precious MSOSA.