MkwasoZa M'dziko Muno

Matenda a Kolera akukodola ku Chingale

Wolemba:

Taona MKANDAWIRE

Mtolankhani Wapadera

Mphepo: Tiyesesa kuti anthu amwe madzi aukhondo. (Chithunzi:Taona Mkandawire)

Pali nkhawa zochuluka kuti anthu ambiri a mdera la Chingale m’boma la Zomba atha kukhudzidwa kwambiri ndi matenda a kolera kaamba kakusowa kwa madzi abwino ku derali.

Izi zadziwika m’masiku apitawa pa msonkhano womwe bungwe la Centre for Social Concern (CfSC) linachititsa m’bomali womwe unabweretsanso pamodzi nzika zokhudzidwa zochokera ku Chingale.

Poyankhula pa msonkhanowo, mkulu wa gulu la Chingale Network, a Francis Gondwa anati derali likukumana ndi mavuto ambiri okhudza madzi kaamba koti mijigo yambiri yauma. Iwo anati izi zikupangitsa anthu a ku derali kutunga madzi ochokera mu zitsime zosasamalidwa bwino zomwe anatinso…

Subscribe online to Mkwaso newspaper and read the whole story