General

‘Atsikana ambiri akukumanabe ndi nkhanza’

Wolemba: Rose Chipumphula Chalira

Pa 11 Okotobala chaka chili chonse mayiko amakumbukira tsiku la mwana wa mkazi pa dziko lonse. Kuno ku Malawi mwambo waukulu unachitikira mu mzinda wa Lilongwe pamene boma la Balaka linasankha kuchita mwambowu pa 27 Okotobala pabwalo lamasewero la Kankao kwa Mfumu yayikulu Chanthunya.  

Ngakhale kuti boma ndi mabungwe akuchita chotheka kuti asungwana asamakumane ndi zokhoma pa maphunziro komanso pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku, zikuonetsa kuti ntchito idakalipo kuti nkhanza kwa asungwana zitheretu.

Polankhula pa mwambowu, womwe mutu wake unali ‘Liwu langa, tsogolo langa’, mlangizi woona ntchito yosamalira anthu m’boma la Balaka, a Nelie Kumalele anati ntchitoyi – maka m’dera la Mfumu yayikulu Chanthunya – ikukumana ndi zokhoka zambiri. 

“Mu 2022-2023, atsikana 13 anagwiriridwa m’derali, zomwe zikupereka chiopsezo kwa mwana wa mkazi pa nkhani ya maphunziro komanso chitetezo chake,” anatero a Kumalele.

A Kumalele anati atsikana akukumana ndi mavuto pa sukulu ya pulayimale ya Kankao pomwe palibe zimbudzi zokwanira. Komanso pa sukulu ya sekondale ya Kankao palibe zipinda zogonera za atsikana ndipo iwo sangakwanitse kumakaphunzira sukulu zakutali. 

Iwo anapempha phungu wa derali, a Bertha Ndebele, komanso akuluakulu ena kuti atenge nawo mbali pokonza ena mwa mavutowa kuti mwana wa mkazi aziphunzira ndi kukhala malo abwino. 

A Kumalele ati mavuto azachuma ndi ena mwa omwe akutsamwitsa ntchitoyi kuti iyende bwino. 

M’modzi wa alangizi ku bungwe la Ujama Pamodzi Africa, a Enestina Kamalo anati bungwe lawo likuphunzitsa atsikana njira za m’mene angazitetezere ku nkhanza, powapatsa luso losiyanasiyana komanso kuwulula nkhanza zomwe akukumana nazo. 

“Sitikuphunzitsa atsikana okha; anyamata tikuwaphunzitsanso kutenga nawo mbali poteteza atsikana chifukwa nkhanza zambiri za atsikana zimachokera kwa anthu a amuna,” anatero a Kamalo. 

Phungu wa derali, a Ndebele anachenjeza abambo omwe ali ndi mchitidwe wogonana ndi ana a chichepere kuti asiyiretu zachipongwezi.

“Muloleni mwana wa mkazi aphunzire ngati wina aliyense kuti dera lino, komanso dziko lino lipite patsogolo. Ine makolo anga akanapanda kundipatsa mwayi wa maphunziro sibwenzi ndili phungu otumikira dera lino,” anatero a Ndebele.

A Ndebele anati pa vuto la zimbudzi ndi malo ogona atsikana ayesetsa kuti atheka ndi cholinga choti atsikana asalephere maphunziro awo. 

Mlendo wolemekezeka pa mwambowu, a Hendrina Galafa omwe ndi namwino yemwenso ndi mtsikana amene wakulira mderalo, anati ndizotheka kuti atsikana a mderali achite bwino pa maphunziro awo posaziwonera pansi.

“Ndikupempha makolo kuti adzitumiza ana awo a akazi ku sukulu kuti maphunziro apite patsogolo. Izi zidzathandiza kuti atsikanawa adzakhale  ozidalira pa chuma,” anatero a Galafa. 

Mabungwe a Foundation For Civic Education and Social Empowerment (FOCESE), nthambi ya chitetezo,  Save the Children, ECM ndi nthambi yowona chisamliro cha anthu, anawonetsa ntchito zosiyanasiyana zomwe amagwira zoteteza mwana wa mkazi. 

Pakati pa 2022 ndi 2023, chiwerengeo cha atsikana achichepere omwe anakwatiwa m’derali chinali 56, otenga mimba 88, osiya sukulu 32 ndipo 16 anagwiriridwa.