MkwasoUncategorized

Flames ikumana ndi Burkina Faso patatha zaka 11

Wiolemba: Bartholomew BOAZ

Timu ya Flames ikhala ikupita ku Burkina Faso komwe ikasewere ndi timu ya dzikolo mu mpikisano wa 2021 Africa Cup of Nations (AFCON) womwe uchitike pa 23 Malichi. Aka kakhala koyamba matimuwa kukumana chikumanireni m’chaka cha 2009 m’masewero olimbirana malo mu chikho chadziko lonse lapansi.

Mu gulu lomwe Flames ili, muli matimu a Uganda, Burkina Faso ndi South Sudan. Matimu onsewa asewera masewero awiriawiri ndipo Uganda ndi Burkina Faso akutsogola ndi mapointi anayi, pomwe Malawi ndi yachitatu ndi mapointi atatu. South Sudan ili kumapeto opanda pointi.

Flames ili ndi mtunda waukulu woti ikakwere ku Burkina Faso potengera kuti ikukumana ndi imodzi mwa matimu aakulu mumo mu Africa yomwenso ili ndi ose-wera ambiri abwino.

Potengera mbiri, Flames siinagonjetsepo Burkina Faso. Mukukumana kanayi kwa matimu awiriwa mu mpikisano wolimbirana chikho cha dziko lonse, Flames siinapambanepo, mmalo mwake idagonja katatu ndi kufanana mphamvu kamodzi.

M’chaka cha 2000 Flames idafanana mphamvu ndi Burkina Faso pakhomo atagoletsana chigoli chimodzichimodzi. M’chaka chotsatira idagonja 4-2 ku Burkina Faso. Ndipo m’chaka cha 2009 idagonja kawiri motsatizana ndi chigoli chimodzi kwa duu m’masewero onse awiri.

M’masewero asanu ndi atatu amene timu ya Flames yasewera chaka chathachi yapambanapo masewero awiri kugonja atatu ndipo kufanana mphamvu atatu. Masewero asanu ndi amodzi anali a mu mpikisano wa AFCON pomwe awiri anali a World Cup.

Mati a Malawi ndi Burkina Faso ndi osiyana kwambiri mu zinthu zambiri. Burkina Faso ili pa nambala 76 mu mndandanda wa matimu padziko lonse lapansi pomwe Malawi ili pa nambala 123.

Mphunzitsi wa Flames Meck Mwase adalira kwambiri anyamata monga Gabadinho Mhango amene wayaka moto ku timu ya Orlando Pirates ku South Africa. Ena mwa osewera omwe masapota a Flames anga-ikepo chiyembekezo chao ndi Limbikani Mzava (Highlands Park, South Africa), Frank Banda (Songo, Mozambique), Gerald Phiri Junior komanso Richard Mbulu (Baroka FC, South Africa) ndi Robin      Ngalande (Zira FC, Azerbaijan) mwa osewera ena.

Burkina Faso ikuyenera kudalira osewera monga Charles Kabore amene akusewera ku timu ya FC Dynamo Moscow (Russia), Bertrand Traore (Lyon, France), Babayoure Sawadogo (Saudi Arabia), Edmond Tapsoba (Bayern Leverkusen, Germany), Issa Kabore (Belgium), Zakaria Sanogo  (Armenia), Aristide Bance (Guinea) ndi Lassina Traore (AFC Ajax, Denmark).

Kutengera mbiri za matimuwa, zotsatira zabwino kwambiri zimene ochemerera timu ya Flames angayembekezere ndi kugonja ndi zigoli zitatu kwa chimodzi. Matimu awiriwa adzakumananso pa 31 Malichi pomwe Burkina Faso idzabwere m’dziko muno.