Hangover ikufuna mendulo za FISD
Victor SINGANO Junior, Mtolankhani Wapadera
Akatswiri omwe awonetsa msana wa njira timu ya Be Forward Wanderers mu FISD Challenge Cup a Hangover United anenetsa kuti maloto awo ndiwofunisitsakuvala mendulo pa mapeto pampikisanowu.
Hangover yomwe ikuphunzi-tsidwa ndi katswiri yemwe anase-werapo mu timu Ya dziko lino komanso Wanderers ndi Nyasa Big Bullets MacDonald Yobe yapanga mbiri yokhala timu yokhayo yose-wera mu ligi yaying’ono kufika mu ndime ya semifayinolo chiyambire mpikisanowu mchaka cha 2016.
Koma iyo ikuyenera kuvala zili-mbe chifukwa ikudzakumana ndi timu ya Kamuzu Barracks omwe amatha kusewera mpira wa ‘nkhanza’ ndicholinga chobalalitsa timu yinayo.
Kaputeni wa timuyi Innocent Indwa wauza Mkwaso kuti palibe chinthu china chilichose chomwe akuchifunisitsa choposa kumenya nkhondo yofuna kuvala mendulo.
Malinga ndi Indwa, iye wati akudziwa bwino lomwe kuti atsala ndi mtunda wina kuti afikire malotowa komabe iye watsindika kuti ayesetsa kuyika mtima monga akhala akuchitira mmasewero awo a m’mbuyomu.
“Ntchito yomwe tayamba kuyi-gwira mu chikho cha FISD ingakhale yopweteka ngati tingatulukire panjira, choncho tikufuna kupanga zothekera kuti ulendowu ukhale wokathera mu ndime yomaliza ya mafayinolo,” anatero Indwa.
Hangover yomwe ili panambala yachinayi mu ligi yakumwera ya ThumbsUp Southern Region Football League yakwanitsa kugonjetsa matimu a Airborne Rangers, Mighty Tigers komanso Wanderers.
Pakadalipano, mkulu woona za malonda kukampani ya Rab Processors yomwe imathandidza ligi ya ThumbsUp Anthony Kafuwa anati ndiwosangalala kuti timu yosewera mu ligiyi yakwanitsa kufika pa ndimeyi zomwe anati ndizokondwe-retsa komanso zopereka chilimbikitso.
“Izi ndi zinthu takhala tikufuna kuti zizichitika ndipo ngati kampanitikhala pansi kuti tiwone momwe tingayili-mbikitsire timuyi mmasewero ake amene atsala ndicholinga choti adzathe kutenga chikho chimenechi,” anatero Kafuwa.
Mu ndime ya ma semifayinolo muli ma timu a Silver Strikers yomwe inapha Nyasa Big Bullets kudzera mmapenote, Kamuzu Barracks yomwe inagonjetsa Savenda Chitipa United 3-0 komanso Blue Eagles imene inakwapula Moyale Barracks.
Masewero a ndime ya masemifayinolo akuyembekezeka kumenyedwa pa 23 ndi 24 Novembala, katswiri wa chikhochi akudzatenga K20 miliyoni.