MCP ndi UTM angatenge boma?
Wolemba: Precious MSOSA ndi Joseph KAYIRA
Pamene chipani cha Democratic Progressive (DPP) ndi United Democratic Front (UDF) mu mwezi wa Febuluwale chaka chino zinalengeza mgwirizano wawo, nazo zipani za Malawi Congress (MCP) ndi UTM zakambirana zokhazikitsa mgwirizano wawo umene akatswiri pa ndale akuti ukhoza kuthandiza zipani ziwirizi kulowa m’boma chikachitika chisankho cha pa 19 Meyi 2020.
Malinga ndi malipoti zipani za MCP ndi UTM zagwirizana kupanga mgwirizanowo khoti litalamula kuti kuyambira pano, dziko la Malawi lidzigwiritsa ntchito ndo-ndomeko ya 50+1 kapena kuti wopambana azipeza mavoti oposa theka pa chisankho cha pulezidenti. M’mbuyomu pulezidenti amatha kupambana ndi movoti osapyola theka bola angotsogola kuposa enawo ngakhale ndi voti imodzi.
Pa chisankho cha chaka chatha, chipani cha DPP ndicho chidapeza aphungu ambiri komanso mtsogoleri wake ndi amene adapeza mavoti ochuluka. Chipani cha MCP chinali chachiwiri pamene cha UTM kandideti wake anali wachitatu ndipo wa UDF anali wachinayi.
Akatswiri omwe alankhula ndi nyuzipepala ya Mkwaso afotokoza kuti mgwirizano wa zipani pa nyengo ino ndi njira yokhayo imene amene akuimira angapeze theka la mavoti amene aponyedwa chifukwa ndale za m’dziko muno ndi za zigawo komanso mtundu wa munthu.
Poyankhulapo atafunsidwa ngati mgwirizano wa MCP ndi UTM ungathe kubala zipatso kwa Amalawi, a Humphrey Mvula anati ubale wa zipani ziwirizi ndiwokhawo womwe ungathe kubweretsa kusintha komwe anthu ambiri akhala akukuyembeke-zera potengera ndi ma manifesto awo.
Iwo anati zipani ziwirizi zikufanana muzambiri pa zomwe zikufuna kudzachita zikadzalowa m’boma. Apa a Mvula anati zipanizi zinalonjeza kupititsa patsogolo nkhani ya ulimi, kayendetsedwe ka chuma, migodi, maphunziro ndinso kuchepetsa mphamvu za pulezidenti.
“Mutati muwonesetse zipani ziwirizi zili ndi ndondomeko zabwino zodzapititsira patsogolo maphunziro makamaka pothetsa kasankhidwe ka tsankho kopita ku sukulu za ukachenjede (quota system), zilinso ndi zikonzero zabwino ku nkhani ya ulimi poonesetsa kuti pafupifupi aliyense akupindula ndi fetereza wotsika mtengo pofuna kuwonesetsa kuti chakudya chisamasowe.
“Zonse zilinso ndi masomphenya odzachepetsa mphamvu za pulezidenti. Masomphenya awo akufanana mu zambiri kotero kuti atati ayendere limodzi zitha kupindulira kwambiri dziko lino,” anatero a Mvula.
Iwo anafotokoza kuti chipani cha DPP chili kale ndi mantha ndi ubale wa zipani ziwirizi ndichifukwa atsogoleri ake akuyesetsa kuwombanitsa mitu zipani ziwirizi.
Koma katswiriyu anapereka che-njezo loti ndikofunikira kuti atsogoleri a zipani ziwirizi agwirizane mogwira mtima pa momwe angadzayendetsere dziko lino atati adzapambana chisankho chikubwerachi.
“Pa atsogoleri awiriwa, wina ali kale ndi zaka zoposera 60 pomwe wina 40 zomwe zikutanthauza kuti wa 60 ali ndi nthawi yochepa yotengera mgwirizanowo kutsogolo kusiyana ndi wa 40. Choncho zonsezi akuye-nera kuwunikirana bwino kuchitira patsogolo,” iwo anatero.
Iwo anawonjezeranso kuti nkhani ina yofunikira ndiyonkhudza kagawanidwe ka mipando chifukwa nthawi zambiri ndizomwe zimayambitsa mamembala ena kugalukira.
Koma iwo anati ndikofunikira kwambiri kuti MCP ndi UTM zibwere pamodzi kaamba koti pazokha palibe chomwe angadzapinduleko pa chi-sankho chikubwerachi.
A Eddy Kalonga, omwe ndi katswiri pa nkhani za ndale ndipo amaphunzitsa ku sukulu ya Malawi Institute of Management (MIM) afotokoza kuti a MCP ndi a UTM awunikira bwino kufunika koye-ndera limodzi chifukwa akudziwa kuti aliyense kuima payekha sidzingayende.
Iwo ati malingana ndi chigamulo cha khotichi, ndi okhawo amene auikira bwino kufunika kwa mgwirizano amene angalowe mboma ndipo zipani ziwirizi zili ndi mwai wonse wopanga boma latsopano.
“Malinga ndi njira ya 50+1 kapena kuti pulezidenti adzipeza mavoti oposa theka kuti apambane, zipani zawona kufunika kogwirizana ndi kuika pa mpando munthu wachikoka ngati akufuna kulowa m’boma,” anatero a Kalonga.
Iwo afotokozanso kuti mgwirizano wa MCP ndi UTM ndi wa mphamvu koma nkofunika kuti atsogoleri aka-mbirane moona mtima pa zogawana maudindo ndi momwe angadzatumikire bwino Amalawi.
Chipani china chomwe chikumakhala nawo ku misonkhano ya MCP ndi cha Peoples (PP), chomwe sichinalengezebe ngati chikhale nawo mu mgwirizanowo.
“Kawirikawiri nkhani yogawana maudindo ikhoza kusokoneza zinthu ngati mbali ziwiri zokhudzidwa sidzikukambirana mwachilungamo. Koma chachikulu sikutsogoza maudindo koma kutumikira Amalawi ndi kutukula dziko lino. Mukaona mgwirizano wa zipanizi ukuonetsa kuti mwai ulipo woti akhoza kulowa m’boma, bola kuchita kampeni ya-mphamvu,” iwo anatero.
A Kalonga achenjeza atsogoleriwa kuti akuyenera kufikiranso owatsatira asanasainirane mgwirizano wawo. Iwo akuti anthunso amakhala ndi zokhumba zawo pa migwirizano yotereyi ndipo kupanda kuwafunsa maganizo awo zithanso kubweretsa mpungwepungwe.
“Zipanizi zili ndi odzitsatira ambiri koma kawirikawiri atsogoleri sala-badira zofunsa maganizo awo pa zomwe akufuna kuchita monga kuchita mgwirizano ndi chipani china. Anthuwanso amafuna mipando ndipo mgwirizano umadzasokonera ngati anthuwa sakuwona phindu la mgwirizano,” anatero a Kalonga.
Mgwirizano wa MCP ndi UTM wadza pomwe zipani za DPP ndi UDF zinalengeza kuti zigwirira ntchito limodzi mpaka pomwe zidzasankhe wodziiimira pa chisankho cha pa 19 Meyi.
Pa 3 Meyi khoti lidagamula kuti chisankho cha pulezidenti chomwe bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidalengeza kuti a Mutharika ndiwo adapambana, chinali ndi zolakwika zambiri. Khotili lidalamula kuti chisankho china chikuyenera kuchitikanso mu masiku 150 kuchokera tsiku la chigamulolo.
A Mutharika ndi MEC anapanga apilo posakhutitsidwa ndi chigamu-locho ndipo nkhaniyi ayamba kuimva ku khoti la Supreme poschedwapa.