MkwasoZa M'dziko Muno

BOMA LA TONSE LABALALIKA

 Katundu akukwera mtengo pafupipafupi
 Ulendo wa ku Kenani siufera m’giya?

Wolemba:

Precious MSOSA

ndi Wingstone PHIRI

Pamene Amalawi ambiri akupitilirabe kuloza zala utsogoleri wa boma la mgwirizano wa Tonse kaamba kosawonetsa chidwi chokwaniritsa pa zomwe linalonjeza ndinso kupeza njira zowatetezera kumbali ya kukwera mtengo wa katundu, pulezidenti Lazarus Chakwera wati iye wangokhala dalaivala chabe.

Pomwe boma la Tonse tsopano likuthamangira kukwanitsa zaka ziwiri, anthu ambiri ayamba kuwonetsa kukhumudwa ndi bomali pomanena kuti likulephera kukwaniritsa zomwe linalonjeza Amalawi. Mwazina, anthu ambiri akunena nkhani monga kuchedwa kwa kuyamba kwa zitukuko zosiyanasiyana monga misewu.

Kuwonjezera apo, ambiri mwa anthuwa awonetsa nkhawa zawo ndi momwe katundu akumakwerera mtengo pafupifupi tsiku ndi tsiku. Mwachitsanzo, katundu monga mafuta ophikira tsopano botolo la ma lita awiri likugulidwa pa mtengo wa K4,500 pomwe enanso ali pa K4,700 kuchoka pa K2,500.

Kukwera kachiwiri kwa mtengo wa mafuta ophikirawa kukubwera pamene panali kale mkwiyo wochokera ku mabungwe omenyerera ufulu wa anthu omwe amakakamiza makampani opanga mafutawa kuti atsitse mtengo.

Mwachitsanzo, pamene masiku apitawa anthu anangozizimuka za mtengo watsopano wa mafuta ophikirawa, wamkulu wa bungwe la Consumers Association of Malawi (CAMA) a John Kapito anauza wailesi ya kanema ya Times Television kuti boma likuyenera kupeza njira yowonesetsa kuti mafuta ophikira akugulitsidwa pa mtengo wabwino.

“Sikale pomwe anthu amachita zionetsero ndikukwera kwa mtengo wa mafuta ophikirawa, pano tizimvanso kuti akweranso. Pali njira zambirimbiri zomwe boma litha kuchita poteteza Amalawi kumitengo yokwerayi,” anatero a Kapito.

Koma poyankhula posachedwapa ku mtundu wa Amalawi pa mwambo wokhazikitsa nthambi yatsopano yoonetsetsa kuti ntchito zachitukuko za mtsogoleri zikukwaniritsidwa ya Presidential Delivery Unit (PDU), a Chakwera anati kukanika kwa zitukuko zina ndi mavuto a adindo ena omwe akulephera kuchita zomwe zikufunikira.

Pamenepa iwo anayerekeza boma kukhala galimoto lonyamulira katundu ndipo iye nkukhala woyendetsa, wachiwiri wake kukhala mekaniko pomwe akuluakulu ogwira ntchito m’boma ngati makondakitala omwe ntchito yawo ndi kuonetsetsa kuti katundu aliyense wafika malo oyenerera.

“Nkotheka kukhala ndi dalayivala wabwino, mekaniko wabwino ndi galimoto lonyamula katundu labwino komabe ndikulephera kuperekera katundu yemwe Amalawi tidawalonjeza chifukwa cha makondakitala amene akulephera komanso kuyiwala kuyika katundu malo oyenera mu galimotoli.

“Kapenanso makondakitala kulephera kumuteteza bwino katunduyo kuti asaonongeke ndinso kuti mbava zisamufikire,” anatero a Chakwera.

Poyankhapo pa mau a Chakwera, mmodzi mwa anthu otsatira bwino nkhani za ndale, a Humphreys Mvula anati zomwe akunena a Chakwera ndizoona kaamba koti iwowo ntchito yawo ndiyongolamula zofunikira kuchita koma okwaniritsa ndi adindo ochokera ku nthambi zosiyanasiyana ndi m’maofesi a boma omwe anayerekezedwa ngati makondakitala.

“Pulezidenti kapena wachiwiri wake samatha kulowa kukagwira ntchito m’maofesi a nthambi za boma ndipo ogwira ntchitozi amakhala iwo amene ayikidwa m’maofesimo ndiye nthawi zina olephera amakhala omwe atumidwa kuti agwire ntchito yomwe mtsogoleri walamula kuti agwire,” anatero a Mvula.

Koma ngakhale izi zili chomwechi, a Mvula anatinso mtsogoleri wa dziko ayembekezerebe kulozedwa zala zinthu zikamalakwika pozindikira kuti maso a nzikazi amayang’ana kwa mtsogoleri.

Iwo anati izi zimakhala chomwechi chifukwa iye ndiyemwe adamusankha ndikumukhulupirira pomwe ogwira ntchito mu nthambi zabomazi adasankhidwa ndi mphamvu za mtsogoleriyu.

Malingana ndi a Chakwera, kukhazikitsidwa kwa nthambi yatsopanoyi ndi njira imodzi yomwe ithandizire kukweza ntchito yokwaniritsa zitukuko zonse zomwe iwo analonjeza ngati boma la mgwirizano wa Tonse.

Kupatula mafuta ophikira, ena mwa mavuto omwe anthu ambiri akudikira a Chakwera kuchitapo kanthu ndi monga kukwera kwa mtengo wa fetereza ndi katundu wina.