Uncategorized

‘Tisasale anyamata potukula maphunziro’

Wolemba Precious Msosa

Pamene mabungwe osiyanasiyana akangalika kutukula maphunziro a atsikana mdziko muno, bwanamkubwa wa boma la Balaka a Tamanya Harawa apempha mabungwewa kuti azikumbukiranso anyamata mu mapulojekiti awo.

Poyankhula pa mbindikiro wa atsikana (Girls Summer Camp) ku sekondale ya Balaka lero, a Harawa anati ndizomvetsa chisoni kuti anyamata sakulabadiridwa mu mapulojekiti ambiri othandiza kupititsa patsogolo maphunziro awo.

“Ngati dziko tamuyiwala mnyamata. Iyeyu ndiamene amakavutitsa mtsikana choncho tikuyenera kumuganiziranso ndicholinga choti akamamuona mtsikana, adziona ngati mchemwali wake woti sangamupange zosayenera,” anatero a Harawa.

Phungu wa dera la Kuzambwe kwa Balaka a Bertha Ndebele anagwirizana ndi a Harawa ponena kuti anyamata akapitiriza kusalidwa, atsikanawa adzasowa owakwatira patsogolo chifukwa azidzawopedwa kufunsiridwa kaamba ka maphunziro awo.

Wachiwiri kwa nduna ya za maphunziro a Nancy Chaola Mdooko yemwe anali mlendo wolemekezeka anapempha atsikanawo kuti agwiritse ntchito mwayi womwe mabungwe a Oxfam ndi Centre for Alternatives for Victimized Women and Children (CAVWOC) awapatsa ndicholinga choti adzakwaniritse maloto awo.

Iwo anati boma likuyesetsa kumbali yake yothandiza atsikana kuti azimaliza maphunziro awo mopanda zopsinja zambiri. Pamenepa anatchula kumangidwa kwa malo ogonera mu sukulu zina komanso kulipiliridwa sukulu ndi mabungwe osiyanasiyana (scholarships).

Mbindikirowu womwe unali wa masiku atatu unakonzedwa ndi bungwe la Oxfam komanso CAVWOC ndicholinga chofuna kuwalimbikitsa pa maphunziro awo komanso pa moyo wawo.

#Montfortmedia