Demokalase imalimbikitsa kukambirana mwa mtendere
Wolemba: Joseph KAYIRA
Kwa miyezi isanu ndi itatu tsopano, bungwe lomenyera anthu maufulu, la Human Rights Defenders Coalition (HRDC), lakhala likuchititsa zionetsero zosakondwa ndi m’mene bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidayende-tsera chisankho cha mu May chaka chatha. Atsogoleri a HRDC akufuna Pulezidenti Peter Mutharika achotse paudindo wapampando wa bungwe la MEC a Jane Ansah ndi makomi-shona ena onse kuphatikizapo akuluakulu ena aku MEC. Ndi nkhondo imene mpaka pano siinathe.
Kuphatikizapo apa HRDC ikufuna kuti a Mutharika asayinire msanga mabilu amene Nyumba ya Malamulo inagwirizana wokhuza kayendetsedwe ka chisankho. Mabiluwo anapita kwa a Mutharika masiku apitawa ndipo akuyenera kuwasayinira pasanathe masiku 21 kuchokera pomwe adawalandira. Mwa zina mabiluwa akawasayinira adzathandiza kuti dziko lino liyambe kugwiritsa ntchito loti wopambana pa chisankho cha pulezidenti azipeza mavoti oposa theka kapena kuti 50% + 1.
Ngakhale mneneri wa a Mutharika a Mgeme Kalirani ananena kuti mtsogoleri wa dziko linoyu akuunika nkhaniyi, a HRDC akuti a Mutharika akuchedwetsa kusainako ndipo iwo tsopano angoganiza zopita ku nyumba za boma nkukachita mbindikiro. Akuti achita izi pofuna kukakamiza a Mutharika kuti asaine mwamsanga mabiluwo.
Izi zadzetsanso mpungwepungwe wina kaamba koti Pulezidenti Mutharika wanenetsa kuti ngati anthuwa apitirize ganizo loti adzachite mbindikiro ku nyumba za boma adzakumana ndi apolisi ndi asirikali. Pa msonkhano wake waposachedwapa pa bwalo la Njamba mu mzinda wa Blantyre a Mutharika anati atopa ndi zomwe bungwe la HRDC likuchita kaamba koti iloli “silili pa mwamba pa lamulo.
“Kuno ku Malawi kuli boma. Ndikuwauza a HRDC kuti ndatopa ndi zochita zawo ndipo pano sindilekereranso zopusazi. Nthawi yonseyi ndimakhala chete chifukwa sindimafuna kuti zomwe zinachitika pa July 11 zija zichitikenso nthawi imene mchimwene wanga anali pulezidenti.
Zimandikhuza kwambiri. Koma pano sindilolanso kuti anthu ena abweretse chisokonezo,” anatero a Mutharika pa msonkhanowo.
Ubale wa HRDC ndi boma la a Mutharika wakhala uli wa gwede-gwede kaamba koti mbali ziwirizi sizitha kukambirana pa zomwe zikusokonekera. Masiku apitawa apolisi anamanga atsogoleri a HRDC – a Timothy Mtambo, Gift Trapence komanso a MacDonald Sembereka. Izi zinachitika a Mutharika atangonena kuti salekeleranso a HRDC kusokoneza mtendere womwe wuli m’dziko muno.
Atsogoleri a HRDC nawo akuti sangaope aliyense chifukwa iwo zimene akuchita ndi zoloredwa ndi malamulo a dziko lino. Mwa chitsanzo a Timothy Mtambo, omwe ndi wapampando wa bungwe la HRDC anauza wailesi ina m’dziko muno kuti iwo apitiliza kuchita zionetsero kaamba koti akufuna chilungamo chioneke.
“Kupita ku nyumba zaboma kukachita m’bindikiro sikulakwa kaamba koti nyumbazo ndi za Amalawi. Ndi misonkho ya Amalawi. Ngati china chake chinga-tichitikire Amalawi akudziwa anthu amene angawaganizire chifukwa akutiopseza kuti tisachite mbindikiro. A chipani cha DPP [Democratic Progressive] anawalola bwanji kuchita zionetsero?
“Komanso a Mutharika ndi pulezideti wa DPP yokha kapena to-nsefe? Apange zinthu ngati pulezidenti wa dziko osati wa chipani chimodzi. Ife sitisiya kuchita zione-tsero mpaka zomwe tikuona kuti zikulakwika zitakonzedwa,” anatero a Mtambo pa wailesiyo.
Kukhadzulirana Chichewa pakati pa mbali ziwirizi kwaonongetsa za-mbiri. Mwa chitsanzo a HRDC akakhala ndi zionetsero sipalephera wina kulira kuti amuonongera malo ake a bizinesi. Penanso maofesi a boma amene, galimoto za polisi ndi katundu wina wambiri wakhala akutenthedwa kapenso kubedwa kumene.
Pa zionetsero za HRDC masiku apitawo Amalawi anaona m’mene mabanki ndi mabizinesi ena anatchingira malo awo a binzinesi poopa zachipolowe zomwe zimatsatirapo zionetsero zikachitika. Sukulu zina zinafika popereka tchuthi pa tsikuli poopa mkwiyo wa anthu ochita mademo ndi zipolowe.
Tingayende bwanji?
Zaonetseratu kuti kupikisana komwe kukuchitika pakati pa boma ndi a HRDC komanso zipani zotsutsa boma sikukupindulira aliyense. Amene amapindula mwina ndi aupandu amene amatengerapo mwai pa zionetsero nkumaba katundu wa anthu. Pamene mademo kapena kuti zionetsero ndi zololedwa ndi Malamulo oyendetsera dziko, umbanda umene ukuchitika pa nthawi ya zionetsero ndi upandu – ndipo uku nkuphwanya malamulo.
Ambiri tikunena pano akulira chifukwa bizinesi zawo zinathera pomwe anthu ena aupandu anaswa malo awo abizinesi nkuba katundu yense. Ena galimoto ndi nyumba zawo zinatenthedwa pomwe anthu ena aupandu, mu dzina la mademo anawachita chipongwe.
A HRDC sangaletsedwe kuchita zionetsero chifukwa uwu ndi ufulu wawo. A DPP nawo sangaletsedwe kuchita zionetsero chifukwa nawonso ngati a HRDC – nawonso ali ndi ufulu wochita zomwe akufuna mogwirizana ndi malamulo a dziko lino. Chomwe chikuvuta ndi kuthana ndi aupandu amene amalowerera zionetsero zikamachitika nkumabera ena.
Nthawi yakwana tsopano yoti ambali ya boma ndi a HRDC akhale pansi ndi kukonza Malawi. Kuopsezana, kukulirana mtima kukungosokoneza mapulani a chitukuko amene alipo kale. Atsogoleri akutaya nthawi yokumana ndi anthu ndi kumva zosowa zawo ndipo ali mkati mopikisana nkumakhadzulirana Chichewa.
Mipingo, kudzera mu bungwe lawo la Public Affairs Committee (PAC) likuyenera kupitiriza ntchito yake yoludzanitsa mbali ziwirizi zomwe tsopano zikuye-nera kukumana maso ndi maso. Mwina mbali ziwirizi zitakumana maso ndi maso kudzakhala kosavuta kuuzana chilungamo. M’mene zikukhalira pano, palibe chomwe Amalawi apindulirepo pa mkanganowu.
Ndi mkangano wosathandiza komanso wowonongetsa zinthu. Pajatu amati njovu ziwiri zikamamenyana ndi udzu umene umavutika – Amalawi ndi amene akuvutikatu apa.