MkwasoUncategorized

Makhoti alowa libolonje

Maloya ku khoti

Wolemba: Precious MSOSA

Nthawi zambiri ambiri mwa ife takhala tikumvapo mau oti ‘ndalama imatha kugula chilungamo.’ Zimakhala zomvetsa chisoni kuwona kuti ku malo komwe anthu akuyembekezera kuwona kapena kulandira chilungamo, pazifukwa zosiyanasiyana zimapezeka kuti chilungamo chakhotetsedwa.

Posapita patali, nkhani ya kachotsedwe ka chisamani chomanga namandwa pa nkhani ya mabizinesi m’dziko muno a Thom Mpinganjira inaimitsa mitu anthu komanso akatswiri pa za malamulo.

A Mpinganjira omwe anamangidwa ndi bungwe lothana ndi katangale komanso ziphuphu la Anti-Corruption Bureau (ACB) pokhala mmodzi mwa oganiziridwa kupereka ziphuphu kwa gulu la oweruza mlandu omwe amayendetsa mlandu wa zachisankho.

Iwo atamangidwa pa 22 Januwale ndi bungwe la ACB ndikukafunsidwa mafunso angapo okhudzana ndi kuganiziridwa kwawo pa mlanduwu, anatengedwa ndi kukatsekeredwa ku polisi ya Blantyre kudikira kuti mawa lake akalowe nawo m’bwalo la milandu.

Koma mphuno salota! Pamene mtundu wa Amalawi kuphatikizapo mkulu wa bungwe la ACB a Reyneck Matemba anali akupha tulo, anthu aku mbali ya a Mpinganjira anali kalikiliki kuwonesetsa kuti namatetule pa bizinesiyu kusamchere mu chitokosi cha apolisi.

Ndipo izi zinathekadi kaamba koti woimira anthu pa milandu a Lusungu Gondwe anakwanitsa kukatenga chiletso chomanga mkuluyu ku khoti la ku Zomba usiku. Choncho zinathekadi; a Mpinganjira  anakamalizira tulo tawo mwa ‘mtendere’ ku nyumba kwawo atatulutsidwa pakati pa usiku. 

Zina kambu zina leku! Ndi katengedwe ka chiletsochi komwe kachititsa anthu kumanena kuti kalipokalipo! Inde, ngakhale mphangala pa zamalamulo nazonso maso adakali chithudzukire kusakhulupirira kuti zinatheka bwanji?

Mwina ena titha kumafunsa kuti cholakwika ndichani pa katengedwe ka chiletsochi? Malingana ndi malamulo, khoti laling’ono lilibe mphamvu lochotsetsa chigamulo choperekedwa ndi bwalo laling’ono linzake. Mu njira ina, ndondomeko yake ndiyakuti bwalo lalikulu (High court) ndi lomwe linali loyenera kupereka chiletsocho.

Malamulowa amavomerezanso kuti khoti lomwe linapereka chisamani chomanga munthu ndilomwe limakhala ndi mphamvu zomasulanso womangidwayo.

Tsono funso lalikulu nkumati; nchifukwa chiyani mbali yoimira a Mpinganjira inasankha zodumpha mabwalo a mu mzinda wa Blantyre ndikupita ku Zomba? Apa tikukamba za anthu oti nawonso malamulo amawatsata bwinobwino. Kodi ku Zombaku anaonako chiyani?

Monga tonse tikudziwa, munthu woweruza mlandu nayenso amakhala kadaulo pa nkhani za malamulo ndipo zimapereka mafunso ambiri ngati munthu woteroyo wakhotetsa mwadala chilungamo. Mafunso monga ‘kodi woweruzayu sanalandire kena kake?’ amayamba kutumphuka pakati pa anthu.

Chomwechonso monga ziliri ndi amene anapereka chiletsochi a Benedicto Chitsakamire – anthu ambiri akumuganizira kuti anadya ‘banzi’ kuti afike popereka chiletso chozizwitsachi. Pakadali pano nthambi ya Judiciary Service Commission a Gondwe ndi a Chitsakamire akuyembekezeka ku-khala nawo pansi.

Chimodzimodzi monga Amalawi komanso ena sakumvetsabe pa zakaperekedwe ka chiletsochi, naye mkulu wa ACB a Matemba akuti anali woima mutu atayimbiridwa foni nthawi ya 12:05 mbandakucha wa pa 23 Januwale kuwuzidwa kuti pali chiletso chomanga a Mpinganjira.

A Matemba anati atamaliza kumva mbali ya a Mpinganjira, anagwirizana ndi wowaimirira kuti mawa lake apita ku khoti kuti akawauze chifukwa chomwe iwo awamangira komanso kuti akapeze mwayi wopemphe belo. Koma kaamba ka chiletso cha pakati pa usikuwo izi sizinatheke mpaka pano pomwe akudikira kuti bwalo lalikulu lichiunikenso chiletsocho.

Iwo anati zomwe zinachitikazi ndizochititsa manyazi ku mbiri ya makhoti m’dziko muno.

Apa iwo anaululanso kuti mpaka pano, adakali ndi mlandu womwe woweruza milandu wina wa bwalo lalikulu anaperekanso chiletso choti bungweli lisafufuze munthu.

“Taganizani khoti lalikulu kupereka chiletso choti tisamufufuze munthu chonsecho malamulo akutilola kutero. Ndikunena pano mlanduwo udakalipo chifukwa tinamang’ala ndipo mpaka pano sitinalandirebe chiweruzo chake,” anatero a Matemba.

Pothirirapo ndemanga pa izi, katswiri wina pa nkhani za malamulo a Garton Kamchedzera anauza wailesi ya MIJ kuti izi zikutanthauza kuti zambiri zomwe anthu timayenera kumadzidalira m’dziko muno ndizowola.

“Ngakhale ku khotiku muli malo ambiri omwe ndiowola. Zimenezi zikutiuzanso kuti amene ali oyenera kumayendetsa malamulowa samawalemekeza. Tili ngati dziko lopanda malamulo kotero kuti zomwe akufuna anthu kuti zichitike ndizomwe zimachitika,” anatero a Kamchedzera, omwenso ndi mphunzitsi wa zamalamulo ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor ku Zomba.

Iwo anauzanso nyuzipepala ya The Nation kuti zomwe zinachitikazi zikuonetseratu kuti ndi chikonzero chapadera  chomwe chinachitika kotero kuti maloya komanso wozenga mlanduyo anali akudziwapo kanthu.

Kaperekedwe ka chinyengo ka chiletsochi kakubwera pomwe lipoti la 2019 la nthambi ya Transparency International (TI) pa kauniuni wa katangale wochedwa Corruption Perception Index (CPI) likuonetsa kuti dziko lino silikuchita bwino pa nkhani za kata-ngale.

Malingana ndi lipotili lomwe linatulutsidwa mwezi wa Januwale, dziko lino labwerera pa nambala 123 kucho-kera pa 120 mu chaka cha 2018. Lipotili limaunika mayiko okwanira 180 ndipo dziko lino liri ndi malikisi okwanira 31 pa 100.

“Ndalama zimagwiritsidwa ntchito kupambana chisankho, kukhala ndi ulamuliro (mphamvu), komanso kupititsa patsogolo zolinga za munthu,” likutero lipotilo mwa zina.

Ngati nkhani zophwanya malamulo monga kupereka mwachinyengo zigamulo m’mabwalo a milandu, kaperekedwe ka makontirakiti ka chinyengo zikupitirira kukula chomwechi nanga atsogoleri athu akamati akufuna kuthana ndi katangaleyu amakhala akunena zoona kapena kumangokhala kumata anthu phula m’maso?

Nthawi yakwana tsopano kuti Amalawi tidzuke ndi kuyamba kumazukuta zomwe atsogoleriwa akumakamba. Tisamangopanga chiganizo chotsatira anthuwa pongotengera ndi ‘nyimbo’ yawo yothana ndi katangale chifukwa zikumaonetsa kuti ndi nkhambakamwa chabe chifukwa mu njira ina nawonso amakhala kuti akusambira nawo momwemo.

One thought on “Makhoti alowa libolonje

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *