MkwasoZa M'dziko Muno

UTSI UFUKA PA CHIPATALA CHA BALAKA

  • K40 miliyoni imatha masabata awiri opanda cholozeka’
  • ‘Ambulansi sizikuyenda kupita kutali’
  • Ogwira ntchito zaumoyo akudandaula ndi utsogoleri omwe ulipo

Wolemba:
Rose Chipumphula CHALIRA

Ogwira ntchito pa chipatala cha Balaka awopseza kuti achita zionetsero zosakhutira ndi momwe akuluakulu apachipatalachi akuyendetsera zinthu, mwa zina akulu akuluwa atalengeza kuti madotolo sazitengedwanso m’makomo mwawo akamakagwira ntchito madzulo kapena akaitanidwa mwadzidzidzi kuti akatumikire. 

Madotolowa ati ndiokhumudwanso ndi m’mene nkhani zoyendetsa ndalama pa chipatalachi zikuyendera. Odandaulawa alembera akulu akulu a khonsolo ya Balaka chikalata momwe muli nkhawa zawo.

Chikalatachi chapitanso kwa mkulu woyang’anira ntchito zaumoyo kuti afotokoze m’mene ndalama zamafuta ndi zina zimayendera pa chipatalachi. Izi zadza kaamba ka zomwe akulu akulu apachipatalachi anawuza madotolo mu mwezi wa Malichi chaka chino kuti makilinishani [clinicians] omwe azigwira ntchito madzulo sadzikatengedwa m’makomo mwawo kupita ku ntchito komanso ngati pali zochitika zadzidzidzi ku chipatala azipeza mayendedwe awo chifukwa cha vuto lamafuta ndi zina. 

Izi sizinawakondweretse ogwira ntchitowa chifukwa ambiri amakhala kutali komanso zimakhala zovuta kuti akafike mu nthawi yake kukakhala matenda adzidzidzi popanda galimoto. 

Ena mwa ogwira ntchitowa omwe ati tisawatchule maina awo, ndipo anasayinira chikalata chomwe anaka-siya kwa ogwirizira udindo wa bwanamkubwa wa bomali ndi ena ati, pachipatalapa pali mavuto ambiri ndipo imfa zomwe zikuchitika pa chipatalachi ndi zopeweka koma chifukwa cha utsogoleri ndi mkana zinthu sizikuyenda. 

“Mabwana akuti pano dongosolo loti galimoto idzidzatitenga latha tikamagwira ntchito usiku. Chonsecho magalimoto omwe iwo amayendera amakhala ali pa mseu ndi malo azisangalalo tsiku ndi tsiku. Kuti apange dongosolo loti tikagwire ntchito mu nthawi yake akuti mafuta palibe,” anatero m’modzi wa anthu omwe asayinira nawo chikalatachi.

Mkuluyu anati ndalama zomwe akulu akuluwa amasakaza pochita zinthu zachinyengo zitha kuthandizira kukonza mavuto ena omwe ali pachipatalachi monga kugula makina a X-ray omwe anawonongeka. 

“Odwala amakajambulitsa ku Comfort Clinic ku Andiamo kapena mu zipatala zina za boma zomwe tayandikana nazo chifukwa makinawa anawonongeka ndipo ndalama zake ndi zosachepera K2 miliyoni. Koma mpaka pano makina ena sanagulidwe ati kaamba koti makinawa anapsa chifukwa cha mphamvu ya magetsi yomwe inachitika nthawi yomwe magetsiwa, omwe anali atazima, ankayaka. Ndipo akulu akulu oyendetsa chipatalachi atafotokozeredwa anati akapereke chikalata chogulira makinawa ku bungwe loona mphamvu ya magetsi [ESCOM] m’dziko muno chifukwa ndi lomwe linachititsa kuti makinawa apse,” anatero mkuluyu. 

Anthuwo akuti pakuoneka kuti pali chinyengo chomwe chimachitika ndi malo omwetsera mafuta galimoto komwe m’malo mothira mafuta kumatengedwa ndalama. Akuti zikatero ambulansi amangoilemba nambala kuti athira mafuta ndalama atathyolera pathumba.

“Tangoganizani, ndi ambulansi yakuti yomwe angathire mafuta a K200,000 kapena K400,000 pa tsiku? Ngakhale galimoto za kwa pulezidenti samathira mafuta ochuluka chonchi pa tsiku galimoto imodzi ayi. Mabwanawa amakangotenga ndalamazi kumagwiritsa zofuna zawo kuyiwala odwala ndi ogwira ntchito zaumoyo. 

“Kunena zoona umbava pa chipatalachi wakula ndipo thandizo kuchokera ku boma komanso kwa anthu akufuna kwabwino limabwera koma zimathera m’matumba mwa akulu akulu omwe sakutha kuyendetsa ntchito zaumoyo,” anatero mkuluyu. 

Pothirira ndemanga pa nkhanizi mkulu winanso anati sinkhani ya ndalama yokha yomwe yavuta pachipatalachi kaamba kotinso odwala sakudya zakudya zabwino, kusowa kwa mankhwala ndi zipangizo zina zogwirira ntchito. 

“Zafika poti polemba umachita kung’amba pena pake kusowa mapepela; ngakhale mayunitsi olumikizalana kuti ogwira ntchito adziwe zinthu zofunika pa chipatalachi sakumapezeka,” anatero mkuluyu. 

Iwo anenetsa kuti ngati khonsolo ya Balaka siwamvera madandaulo awo achita ziwonetsero zokwiya kuti mkulu woona ntchito zaumoyo ndi ena achoke pa chipatalachi kuti kubwere ena omwe angakwanitse kulimbikitsa ntchito zaumoyo osati ozikundikira zinthu

Subscribe Mkwaso news paper online and read the whole story.