MkwasoUncategorizedZa M'dziko Muno

ZAKA 13 AKUDIKIRA KULONGEDWA UFUMU

  • Bingu anandikweza koma ndikuponderezedwa – Gulupu Sosola
  • Palibe kalata yowonetsa kuti anakwezedwa – Unduna

Wolemba:

Rose Chipumphula CHALIRA 

A Gulupu Sosola a m’boma la   Balaka ati ndi wodabwa kuti mpaka pano Unduna wa Maboma Aang’ono ulibe chidwi chowakweza kukhala Sub Traditional Authority (STA) patatha zaka khumi ndi zitatu (13) mtsogoleri wakale wa dziko lino, malemu Bingu wa Mutharika ata-lengeza kuti akwezedwa.

Mfumuyi yati ndiyodandaula kuti anakwezedwa kukhala mfumu yaying’ono mpaka pano sanavekedwe mkanjo wosonyeze kuti anakwezedwa. Iyo yati inauzidwa za kukwezedwa kwawo kudzera kwa nduna yakale ya Maboma Aang’ono m’boma la Democratic Progressive (DPP), a George Chaponda. 

Nyuzipepala ya Mkwaso yapeza kuti m’chaka cha 2008, nthawi yomwe Mfumu Kawinga ya m’boma la Machinga amaikweza kukhala mfumu yaikulu (Paramount Chief) a Chaponda ndi akuluakulu aku Unduna wa Maboma Aang’ono, anayitanitsa Mfumu Sosola, kudzera kwa bwanamkubwa wa boma la Balaka nthawi imeneyo, a James Manyetera ndikuwawuza zakukwezedwa kwa ufumu wawo.

“Ndinapita ku ofesi ya khonsolo ya Balaka nditayitanidwa ndipo kunabweradi a George Chaponda omwe anali nduna nthawi imeneyo komanso mlembi opuma ku Undunawu a LawrenceMakonokaya. Anthuwa anane akuti chawakomera a pulezidenti Bingu wa Muntharika kundikweza ine kuchoka pa gulupu kufika pa mfumu yaying’ono —STA — potengera mbiri ya ufumu wa Sosola komanso kagwiridwe ka ntchito yanga,” anatero a Sosola. 

Mwanza: Sitimagwiritsa ntchito ndale pa nkhani za ufumu

A Sosola anati analonjezedwa kuti zonse zikatheka ku Undunawu kudzakhala mwambo wapadera owapatsa mkanjo ndi zina ngati mfumu yayi-ng’ono yomwe ili pansi pa Mfumu Yayikulu Nsamala m’bomali. Iwo ati umu munali mu mwezi wa Okotobala mu chaka cha 2008.

“Nthawi yonseyi maso anga anali kunjira kudikirira. Mu chaka 2009 kutachitika chisankho Unduna wa Maboma Aang’ono unasintha kupita kwa Goodall Gondwe ndipo bwanamkubwa wa boma la Balaka pa nthawiyo anali a Fred Movete omwe anasinthana ndi a Manyetera. Atawafotokozera za nkhani yanga anandiuza kuti anduna [Goodall Gondwe] akubwera kudzayendera ntchito za chitukuko kwa Mfumu Chanthunya ndipo ndikapezeke kumeneko ndi kufotokoza za nkhani yanga,” anatero a Sosola. 

Atapita kumwambowo ndikukumana ndi a Gondwe ndikuwafotokozera nkhani yawo iwo akuti anawona kuwala atauzidwa kuti “mubwere ku ofesi yanga ku Capital Hill  ku Lilongwe kuti nkhaniyi tidzayilongosole bwinobwino.” 

“Mwezi wa Meyi 2010 ndinatengana ndi abale anga awiri kupita ku ofesi ya andunawa ku Lilongwe. Kumeneko ndinakumana ndi zikhomo kuti ndisaonane nawo anduna chifukwa sindinali pa m’ndandana wa anthu okumana nawo pa tsikulo. Ndinapanga makani mpaka a Makonokaya atandiona anadilandira kutsatira ndondomeko zonse mpaka tinakakumana ndi anduna.

“Kumbali yawo anali anthu atatu a Gondwe, mlembi wa ku undunawu komanso mkulu woyang’anira mafumu ku undunawu. Ndipo tinakambirana za nkhani yanga ndipo atayimva onse anavomereza ndikutsimikiza kuti zichitika chaka chimenecho. Kuphatikiza pamenepo anati phungu wa dera la kuzambwe kwa Balaka, a Nasline Pillane, nawo akhala akukambitsana za nkhani yangayi,” anatero a Sosola. 

Kutsatira mkumano wa ku Lilongwewu a Gulupu a Sosola akhala akuyang’anira kudikirira tsiku lomwe azalongedwe ufumu koma mpaka maulamuliro angapo atasintha chochitika sichikuwoneka. M’chaka cha 2019 mfumuyi inaganizanso zochita kalondolondo wa nkhaniyi powona m’mene mafumu ena m’bomali akhala akuwakwezera. 

“Pa 11 Novembala 2019 ndinalembanso chikalata china cha madando chofotokoza nkhani yanga ku undunuwu koma sizinaphule kanthu mpaka lero. Kutabwera bwanamkubwa wina ku Balaka, a Emmanuel Bambe nawo anayesetsa koma sizinaphulenso kanthu,” anatero a Sosola. 

Zikalata zomwe nyuzipepala ya    Mkwaso yapeza zikutsimikiza za zomwe iwo akhala akulemba kufunsa za nkhani yawo kuti ili pati. Chikalata china chinalembedwa pa 11 Juni 2021 ndi Bwanamkubwa wopuma a Macloud Kadam’manja  kupititsa ku undunawu chofotokoza mbiri ya mfumu Sosola. 

Mfumuyi yati sikukakamira kukwezedwa koma ikufuna chilungamo pa nkhani yawo chiwoneke chifukwa anachita kuwuzidwa ndi anduna kuti a-kwezedwa udindo kukhala Mfumu yaying’ono. “Ndikunena pano anthu ena amawona ngati ndine mfumu yaying’ono pomwe ndikanalibe Gulupu kuyambira m’chaka cha 1996 pomwe ndinatenga ufumuwu mpaka pano,” anatero a Sosola. …

Subscribe Mkwaso newspaper and read the whole story