Uncategorized

Bungwe la DAPP Malawi lakhazikitsa ntchito zaulimi ku Balaka

By Joseph Kayira

Bungwe la Development Aid from People to People (DAPP) Malawi, lati ndi cholinga chake kuti ligwirane manja ndi boma pofuna kudzamitsa chitukuko m’boma la Balaka — mwa zina pa ntchito zaulimi komanso kuonetsetsa kuti anthu ali ndi chakudya chokwanira ndi chopatsa thanzi.

Polankhula pomwe bungwe la DAPP Malawi limadziwitsa khonsolo ya Balaka za pulojekiti yoonetsetsa kuti anthu ali ndi chakudya chathanzi komanso akutha kukhala ndi ndalama kudzanso kuchepetsa umphawi, a Johnstone Chimatira, omwe adziyang’anira pulojekitiyi anati ndiokondwa kuti pulojekitiyi yalandiridwa m’bomali.

“Pulojekitiyi tiigwira ndi mabanja osiyanasiyana m’madera a Mfumu Phalula ndi Mfumu Chanthunya kwa zaka zinayi. Tigwira ntchitoyi ndi alimi 3,000 — omwe mwa zina — azipanga ulimi wa nthirira — komanso azitha kukongozana ndalama m’magulu omwe akhazikitsidwe kuti achepetse umphawi m’mabanja mwawo,” anatero a Chimatira.

Iwo anati dera la Phalula ndi malo amodzi amene alimi amavutika kukolola mbewu monga chimanga kaamba ka ng’amba ndipo ntchito zaulimi zimasokonekera. Mkuluyu wati ndizotheka kusintha miyoyo ya anthu kudzera mu ulimi wanthirira ndipo bungwe lawo laika padera 595,000 Euros (zomwe ndi pafupifupi K1 biliyoni) zogwirira ntchitoyi.

“China chimene tikufuna kuchita pothandiza alimi amene tidzigwira nawo ntchito ndi kuwalumikidzitsa ndi misika yaphindu kuti akakolola zakumunda asamasowe kogulitsa. Muonanso kuti tikulimbikitsa kugwira ntchito ndi makopaletivu ndipo m’menemu muli amayi, achinyamata komanso abambo ndi aulumali.

“Tikulimbikitsa kwambiri amayi kuti atenge nawo gawo pa pulojekiyi. Chiwerengero cha 50 peresenti ndi amayi; 20 peresenti achinyamata ndipo 10 peresenti ndi aulumali. Sitikusiya wina aliyense m’mbuyo; nkuona amayi, aulumali komanso achinyamata akhale akugwira nawo pulojekitiyi,” anatero a Chimatira.

Khonsolo ya Balaka inalangiza a DAPP Malawi kuti mwa zina, awonjezerenso mbewu zina mu pulojekitiyi monga nandolo, mapira, mtedza ndi khobwe. Komanso pokhala kuti dera la Phalula ndi kwa ng’amba, bungweli alipempha kuti liganizire kuwathandiza mabanja kumeneko ndi ulimi wa ziweto.

Bwanamkubwa wa boma la Balaka, a Tamanya Harawa anapemphanso kuti bungweli lithandize anthu a mderali powakopa kuti achepetse kuotcha makala. Chifukwa chosowa mtengo wogwira anthu ambiri akuwotcha makala ngati njira imodzi yopezera ndalama kuti azipeza zosowa pa moyo wawo.

“Makala akuononga chilengedwe; choncho aliyense ali ndi ntchito yokopa anthuwa kuti apeze njira zina zopezera zosowa pamoyo wawo ndipo ulimi wanthirira ukhoza kuthandiza kuwasintha anthuwa. Mu pulojekiti yanu mutaikamonso mlozo umenewu zikhoza kuthandiza kwambiri kuti titeteze chilengedwe uku tikupulumutsanso anthu ku njala.

“Ndipemphenso onse amene amabwera ndi mapulojekiti a chitukuko kuti azifikiradi anthu amene akusowa thandizo. Zimakhala zodandaulitsa kuona kuti mapulojekiti amatha kubwera ambiri koma funso ndi loti, pakutha pa tsiku akumafikiradi anthu amene akuvutika? Nanga pulojekiti inasintha miyoyo wawo?” anatero a Harawa.

Pulojetiki ya DAPP Malawi itheka ndi thandizo la ndalama lochokera ku Unduna woona za ubale wa dziko la Finland ndi maiko ena.