Kuli ziii…a Escom sadzabwera
Uku ndi ku dera la Phimbi m’boma la Balaka komwe msewu wolowera ku Nkaya komwe kuli ma ofesi komanso depoti ya sitima ya pa mtunda ya kampani ya CEAR watsekedwa ndi mawaya a magetsi a kampani ya Escom.
Malingana ndi anthuwa, chichitikireni ngoziyi dzulo, a Escom sanabwerebe kudzakonza vutoli lomwe lazimitsa magetsi ku derali lomwenso kuli chipatala chaching’ono cha Phimbi.
Iwo ati ngoziyi yachitika kaamba koti anthu ena amadula mtengo pa sukulu ya pulaimale ya Thundu womwe unagwera pa nthambo za magetsizi ndikugwetsa mapolo pafupifupi atatu.
Pakadali pano, anthu komanso magalimoto olowera ku Nkaya akuvutika kudutsa pa malowa. Izi kuperekanso chiopsezo kwa ana omwe atha kuyamba kusewera pa malowa.