Uncategorized

UDF ikuti siikutekeseka ndi zochitika mu DPP

A Muluzi ndi a Mutharika tsiku losainirana mgwirizano wawo

Wolemba: Precious MSOSA

Chipani cha United Democratic Front (UDF) chati icho sichigwedezeka ndi zomwe zikuchitika mchipani chakale cholamula cha Democratic Progressive (DPP) chomwe anali nacho pa mgwirizano pokonzekera chisankho cha pulezidenti pa 23 Juni.

Zikuoneka kuti madzi ayamba kuchita katondo mchipani cha DPP pomwe atsogoleri ayamba kulozana dzala komanso ena kutula pansi maudindo. Posachedwapa, mtsogoleri wa chipanichi a Peter Mutharika anachotsa a Grezelder Jeffrey pa mpando wawo wa mlembi wamkulu chifukwa chonena kuti a Mutharika achitapo mbali yawo kotero mso-nkhano wawukulu umafunika.

Nawo a Ben Phiri omwe anali wamkulu woona za zisankho analengeza kuti atula pansi udindo wako kaamba koti anthu ena mchipanichi akuwanena kuti anagulitsa chisankho cha pa 23 Juni, mwazina.

Koma poyankhapo pa zochitikazi mchipanichi, wogwirizira udindo wa mneneri wa chipani cha UDF a Yusuf Mwawa anati iwo sakhudzika kwenikweni kaamba koti ubale wa zipani ziwirizi unali wa chisankho chapitachi.

“Mgwirizano womwe ulipo pakati pa ife ndi a DPP ndiwoti tonsefe tili ku mbali yotsutsa boma mu nyumba ya Malamulo. Kupatula apa palibenso ubale wina wuliwonse. Choncho zomwe zikuchitika ku DPP ndi za ku DPP komweko,” anatero a Mwawa po-wuza wailesi ya MIJ.

Koma iwo anati chipanichi chili ndi malingaliro woyitanitsa mkumano wa mamembala ake a komiti yayikulu kuti awunikirane za chisankho chapitachi ndikuwona mmene angapitire chitsogolo.