Kwaya ya Mtendere itulutsa chimbale

Kwaya ya Mtendere

Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA

Gulu la kwaya mu mpingo wa CCAP pansi pa sinodi ya Livingstonia ku Likuni m’boma la Lilongwe latulutsa chimbale cha nyimbo za uzimu chomwe achikhazikitse mliri wa Covid-19 ukayamba kuchepako.

Mkulu wa kwayayi mayi Clara Nyoni anati ndikoyamba kwayayi chikhalireni kuyimba mu mpingowu kutulutsa chimbale.

“Nyimbo zomwe timayimba timangodalitsa akhristu a mu mpingo wathu koma pano tinaganiza zotulutsa chimbale kuti anthu ena akamva uthenga azilimbikitsidwa ndi kuphunzitsidwa za chikondi cha Mulungu,”anatero a Nyoni.

Iwo anati nyimbozi zayamba kale  kumveka mnyumba zowulutsira mawu za mdziko muno ndipo chomwe chatsala ndi kuchikhazi-kitsa kuti anthu achidziwe.

“Tinaganiza kufalitsa uthenga wa Mulungu kudzera mmayimbidwe chifukwa anthu ena akakumana ndi mavuto amakhala ndi maganizo olakwika koma akamvera nyimbo zauzimu amakhala ndi chilimbikitso mmoyo wawo,” iwo anatero.

Iwo anati mavuto a zachuma ndi Covid-19 ndi zina zomwe zawabwezeretsa mmbuyo kuti chimbalechi chisawafikire anthu munthawi yake. Koma iwo anati anthu asadandaule kwenikweni chifukwa zithu zikakhala bwino chimbalechi chifika pa msika mwezi wa Sepitembala ndikukhazi-kitsidwa madansi akayambiranso,” anatero a Nyoni.

Chimbalechi chomwe akuchitchula kuti Ulendo wa chikhristu muli nyimbo khumi zomwe zayimbidwa mchichewa komanso chitumbuka. Zina mwa nyimbozi ndi Nikwenelera, Likawa dazi lamwayi, Mungaluwanga, Tumani ine, Dziko la Mtendere, Khira zekeyu ndi zina zomwe akutsitsimuka nazo anthu. 

“Tinaganiza zoyimba ziyankhulo ziwirizi kuti omwe samva chitumbuka nawo akhale ndi mwayi okumva nyimbo zina zo-mwe zili mu chimbalechi,” iwo anatero.

Kwayayi yapempha oyimba nyimbo zauzimu kuti achilimike poyimba nyimbo zachipulumutso, zophunzitsa komanso zokokela anthu kwa Mulungu.

A Nyoni anati kwa omwe akufuna chimbalechi atha kuwapeza pa mpingo wa Likuni CCAP wa pansi pa sinodi ya Livingstonia.