Uncategorized

Mipingo yakana lamulo lochotsa pakati

Wolemba: Joseph KAYIRA

Pamene aphungu a Nyumba ya Malamulo akangalika zokambirana ndi kuti avo-mereze kapena kukana lamulo lochotsa pakati, mipingo yambiri yati siikugwirizana ndi malingaliro okhazikitsa lamuloli.

Izi zikudza pomwe masiku apitawa bungwe lina la mapingo lotchedwa Religious Network for Choice (RNC) lidadzudzula mipingo yomwe ikukana lamuloli.

Nyuzipepala ya The Daily Times ya Lachitatu pa 23 September 2020 idagwira mawu a wapampando wa RNC, m’busa Martin Kalimbe kuti anthu amene akukana lamuloli akuchita izi chifukwa sakumvetsetsa zomwe lamuloli likunena.

“Amene akukana lamulo adatenga nawo mbali pomwe kafukufuku wofuna kupeza maganizo a anthu pa nkhaniyi ndi zina ankachitika koma lero alinso patsogolo kukana ntchito yomwe iwo amene adatengapo mbali,” anatero a Kalimbe.

Iwo anati nkulakwa kumaona anthu amene akufuna kuti lamuloli likhazikitsidwe ngati anthu amene sasamala za moyo wa mwana wosa-badwa.

Mkuluyu anati bungwe la RNC limaganizira kwambiri za mwana wosabadwa ndi mayi ndipo limakhuzidwa kwambiri ndi amayi womwe amamwalira chifukwa cha zomwe zimachitikira akataya pakati mwamseri.

Mipingo ikuti kuchotsa pakati ndi tchimo

Koma mipingo monga wa Katolika pansi pa bungwe la Episcopol Conference of Malawi, Malawi Council of Churches, Evangelical Association of Malawi, Muslim Association of Malawi ndi Quadria Muslim Association of Malawi ndiokhumudwa ndi maganizo a komiti ya zaumoyo ku Nyumba ya Malamulo yomwe ikufuna kuti lamulo likhazikitsidwe kuti amayi azichotsa pakati ngati akufuna kutero.

Mchikalata chomwe chatulutsidwa masiku apitawa, mipingoyi yati ikufuna anthu agwirane manja pokana kukhazikitsidwa kwa lamuloli. Iyo yati imakhulupirira kuti munthu aliyense kuphatikizapo mwana amene sana-badwe, analengedwa mu chifaniziro cha Mulungu.

Mipingoyi yati umoyo wa munthu ndi chinthu chamtengo wapatali ndipo uyenera kutetezedwa nthawi zonse.

“Boma, antchito za makhoti, Nyumba ya Malamulo, mabungwe omwe siaboma komanso ma-bungwe akunja alibe mphamvu yochotsa moyo wa munthu koma Mulungu basi. Kuchotsa pakati nkolakwika ndipo ndi tchimo chifukwa mchitidwewu ukusemphana ndi malamulo a Mulungu,” chatero chikalatacho.

Mipingoyi yapempha aphungu kuti akane bilu yokhazikitsa lamulolo. Iyo yapempha onse okhuzidwa kuti adziwitse anthu zakuipa kochotsa pakati.

Mipingoyi yapempha anthu ndi mafumu kuti atengepo gawo pouza aphungu a Nyumba ya Malamulo m’madera awo kuti “asakhale mbali ya awo amene akufuna kupha ana amene sanabadwe pogwi-ritsa ntchito lamulo lochotsa pakatili.”