Tikulowera kuti ndi Covid-19? …Mliriwu wapha kale nduna ziwiri ndi ena ambiri

Anthu akuyenera kuziteteza ku Covid-19 nthawi zonse mwa zina povala masiki pa gulu

Wolemba: Joseph KAYIRA

Pamene chiwerengero cha anthu amene akupezeka ndi matenda a Covid-19 chikukwera m’dziko muno, Amalawi apempha boma kuti liyambe kuika mfundo zokhwima pa anthu amene akulowa ndi kutuluka m’dziko muno. Pempholi likudza pomwe anthu ochokera mmaiko monga South Africa akhala akulowa m’dziko muno ndikulekereredwa kumapita m’makwawo m’malo mo-wasunga malo amodzi kwa masiku khumi ndi anayi monga m’mene ziyenera kukhalira.

Mwa chitsanzo, chaka chatha Amalawi ochokera m’dziko la South Africa omwe anasungidwa pa bwalo la Kamuzu, anathawa apolisi akuona kumapita m’makwawo. Awa ndi amene akuti ali ndi kuthekera kofalitsa kachirombo koyambitsa matendawawa kwa abale ndi anthu omwe azungulira midzi yawo.

Koma komiti yomwe adakhadzikitsa pulezidenti wa dziko lino yotchedwa Presidential Task Force on Covid-19 yati ilimbikitsa malamulo ndi ndondomeko zoonetsetsa kuti matendawa sakufala mopyola muyezo.

Polankhula pa mso-nkhano wa atolankhani Lachinayi pa 7 Januwale 2020, mu mzinda wa Lilongwe, nduna ya zaumoyo a Khumbize Kandodo Chiponda anati ndiokhumudwa kuti matenda a Covid-19 afika povuta ndipo miyoyo ili pachiopsezo.

Malemu Mia

Iwo anati matendawa achititsa kuti boma liwononge ndalama zambiri maka kumalo amene akhazikitsidwa kuti amene apezeka ndi Covid-19 azisungidwa ndi kulandira thandizo mu zipatala za boma ndi kwina.

“Malamulo alipo kale ndipo adasindikizidwa omwe akunena m’mene tingachitire kuti matendawa asafale. Ndi m’mene zinthu zilili pano sitichitiranso mwina ayi koma kuonetsetsa kuti malamulowa akugwira ntchito,” anatero a Chiponda.

Ndunayi ikuti boma liri ndi zipa-ngizo zokwanira kuyezera anthu kwa pafupifupi miyezi itatu.

Unduna wa zaumoyo ugwira ntchito mogwirizana ndi unduna wa maboma aang’ono ndi woona chitetezo cha m’dziko. Pakali pano   undunawu ukuti uwonetsetsa kuti anthu akutsatira malamulo osamba m’manja komanso kuonetsetsa kuti malo ogulitsira mowa (ma bar) akutsegulidwa pakati pa 2:00 koloko masana nkutseka 8:00 koloko usiku. Anthu sadziloledwa kumwera zomwe agulazo pa malo ogulitsira.

Pakali pano pali anthu oposa 1,000 omwe apezeka ndi Covid-19 koma chiwengero chikumakwera tsiku lirilonse zomwe zachititsa kuti boma liyambe kukhwimitsa malamulo. Pakali pano matendawa akugwira aliyense kuphatikizapo nduna za boma, ogwira ntchito m’boma, abizinesi, aphunzitsi ndi ena ogwira tchito komanso kuchita bizinesi zosiyanasiyana.

Mwa zina, boma lanenetsa kuti likufuna chiwerengero cha anthu omwe amapezeka pa maliro, maukwati ndi miyambo ina yomwe kumakhala anthu ambiri, chichepe ngati njira imodzi yothandiza kuti Covid-19 asafale.

Mlembi mu unduna wa maboma aang’ono, a Charles Kalemba anati ndi cholinga cha undunawu kuti mafumu athandize powuza anthu kuti asamale akakhala mmagulu monga ku maliro.

“Munthu akamwalira ndi Covid-19 thupi liyenera kuikidwa m’manda pasanathe maola 24. Izi zithandiza kuti anthu ambiri asamakhale malo amodzi kwa nthawi yaitali,” iwo anatero.

Mkuluyu walengezanso kuti chakudya chokonzedwa pagulu mo-nga m’mene zimakhalira pa maliro ndizoletsedwa tsopano.

Ena mwa akuluakulu omwe amwalira ndi matendawa ndi monga yemwe anali mlembi mu unduna wofalitsa nkhani, a Ernest Kantchentche, yemwe anali nduna ya zamtengatenga a Sidik Mia ndi nduna ya maboma aang’ono a  Lingson Belekanyama. Loweruka pa 9 Januwale 2021, dziko lino linatayanso Maria Chidzanja Nkhoma yemwe anali mkhalakale pa ntchito yautolankhani. Iyeyu analinso mtolankhani ku wailesi ya Zodiak (ZBS).

Nyuzipepala ya Malawi News ya pa Januwale 9-15 2021, mu nkhani yomwe mutu wake ndi ‘Covid-19 hits LMC Cabinet’, inalengeza kuti nduna zinayi zinapezeka ndi Covid-19. Ndunazi ndi Sam Kandodo, malemu Mia, a Rashid Gaffar ndi malemu Belekanyama. Winanso yemwe nyuzipepalayi idalengeza kuti wapezeka ndi Covid-19 ndi wachiwiri woyamba kwa Sipikala wa Nyumba ya Malamulo a Madalitso Kazombo.

Wapampando wa Presidential Task Force on Covid-19, Dr John Phuka anauza atolankhani mu mzinda wa Blantyre kuti ndi m’mene zinthu zilili pakali pano, kuli bwino kusamala kwambiri ndi kuona ngati aliyense akhoza kukhala ndi kachilomboka.

“Inu amene muziziona ngati muli nako ndi mukuyenera kuziteteza,” anatero Dr Phuka.

Malemu Belekanyama

Pomwe boma lakhwimitsa chite-tezo maka kwa anthu amene akucho-kera m’maiko ena monga ku South Africa, anthu omwe akusungidwa ku sukulu yophunzitsira ogwira ntchito za ndende ku Mapanga ku Blantyre, anaononga katundu ndi kugenda galimoto ati kaamba kokwiya ndi ganizo la boma powalanda ziphaso zawo.

Anthuwa, anagenda komanso anatentha katundu pa malowo ati pokakamiza boma kuti liwalole kuti apite m’makwawo. Boma likufuna anthuwo ayezedwe kuti litsimikize ngati ali ndi Covid-19 kapena ayi.

Apolisi amangapo ena mwa anthu omwe anachita nawo zachisokonezozi.

Kafukufuku waonetsa kuti ambiri mwa anthu omwe amachokera ku South Africa amagwiritsa njira zachidule nkuzemba kuti asayezedwe. Awa ndi omwe akufalitsanso kachiro-mboka nkuika miyoyo ya Amalawi pa chiswe.  

“Boma lisanyengerere anthuwa ayi. Akuyenera kutsatira malamulo monga wina aliyense. Tinaona akulumpha mipanda ku sitediyamu (Kamuzu) ndipo achitetezo ama-ngowayang’anira. Ulendo uno anthuwa asungidwe mpaka atatsatira ndondomeko zonse zokhuza Covid-19,” anatero mayi wina ku Blantyre yemwe anati tisamutchule dzina.

South Africa ndi dziko limene matendawa afika povuta kwambiri muno mu Africa. Pakali pano dzikolo liri ndi mapulani wofuna kuyesera nawo katemera wa Covid-19. Maiko a United States, United Kingdom, India ndi China ndi ena mwa omwe akonza katemera wa Covid-19.

Kuno ku Malawi boma lirinso ndi chidwi chofuna kudzayesera nawo katemerayu.