NICE ikulimbikitsa ntchito za uchembere wabwino ku Machinga

Gunde: Anthu sakuberekera m’makomo

Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA

Bungwe lophunzitsa anthu pa nkhani zosiyanasiyana la National Initiative for Civic Education (NICE) Trust m’boma la Machinga likulimbikitsa ntchito za umoyo m’zipatala kudzera mu pulojekiti yotchedwa kubadwitsa cha moyo (Deliver Life Project).

Pulojekitiyi ikulimbikitsa anthu akwa Mfumu yayikulu Kawinga kutengapo nawo mbali pa nkhani yokhudza umoyo wawo kuti achepetse imfa zomwe zimabwera kaamba ka uchembere pakati pa abuthu ndi amayı oyembekezera.

Malinga ndi mlangizi wa NICE mdera la mfumu Kawinga, a Jane Gunde cholinga cha pulojekitiyi ndi kufuna kulimbikitsa ntchito za umoyo m’zipatala zazing’onozing’ono mde-rali zomwe bungweli likugwirako ntchito ndi anthu akumudzi.

Pulojekitiyi ikuteteza amayi, abuthu ndi ana omwe sanafike zaka zisanu omwe amachitilidwa nkhanza pa nkhani ya uchembere ndi madyedwe abwino. Ikufikiranso amayi omwe amayenda mtunda wautali kuti akapeze thandizo komanso kuwalimbikitsa kuti ngati chipatala chili kutali azipita mu nthawi yake.

“Mukudziwa inu mzimayi akamafuna kubadwitsa cha moyo ngati pa chipatala palibe madzi zinthu zimakhala zovuta. Pofuna kupewa mavuto omwe amadza amayi aka-mabadwitsa cha moyo pulojekitiyi ikuwonetsetsa kuti zipatala zomwe tikugwirako ntchito pali madzi aukhondo, zipangizo zogwiritsira ntchito ndi zipangizo zina zoyene-rera kuti mayiwo abadwitse cha-moyo pa malo aukhondo,” anatero a Gunde.

A Gunde anati pulojekitiyi ikulimbikitsanso abuthu kudziwa zamaufulu awo kuti asatenge mimba msanga komanso akadzakwatiwa azizapanga chisankho choyenenerera pa banja. Ikuwalimbikitsanso abuthu kuwapatsa mphamvu kuti azikumana ndi adindo ndi kufotokoza za mavuto omwe akukumana nawo okudza madzi, umoyo ndi mmene angathetsere mavutowa.

Pulojekitiyi ikulimbikitsanso ma-komo kuti mzimayi akhala oye-mbekezera azipita ku chipatala nthawi yabwino kupewa imfa zomwe zimadza kaamba ka uchembere komanso azikhala aukhondo pomanga zimbudzi zabwino zomwe azigwiritsa ntchito zomwe sizingabweretse matenda monga kutsekula mimba ndi ena omwe amadza kaamba ka umve.

“Kuno amayı oyembekezera omwe sakupita ku chipatala kukayamba sikelo mu nthawi yake amalipira chindapusa. Omwe achedwa kupita ku chipatala nkubere-kera pakhomo kapena afika ku chipatala mochedwa timawalipiritsa kuti anthu ena atengerepo phunziro ndipo izi zikuthandiza kuchepetsa mchitidwe oberekera ana pakhomo; ambiri akupita ku chipatala,” anatero a Gunde.

Kapitawo: Mng’ono wanga analipira chindapusa cha K3,000 chifukwa chochedwa kupita ku chipatala

Lawrence Major, mkulu wa komiti ya zaumoyo anati pulojekitiyi ya-yamba kuwonetsa zipatso za bwino mderali chifukwa anthu akutenga nawo mbali pa  zochitika zakudera lawo maka pa nkhani ya zaumoyo, kusamalira zipangizo za pachipatala ndi zina.

“Kale anthu samadziwa umwini wa chitukuko chomwe akupatsidwa koma lero pa chipatala cha Kawinga, anthu akusamalira zipangizo zomwe anapatsidwa komanso kuwonetsetsa kuti malowa ali ndi ukhondo nthawi zonse,” anatero a Major.

A Major anati chipatala cha ching’ono cha Kawinga chimathandiza anthu oposa 500 ochokera m’midzi yozungulira chipatalachi. Isanabwere pulojekitiyi panali mavuto adzaoneni monga kusowa kwa madzi, ogwira ntchito zaumoyo amabwera mmene akufunira koma panopa zonsezi ndi mbiri yakale.

“Aliyense amasonkha K200 yomwe imathandizira ntchito zina zapa chipatalachi m’malo modikira mabungwe. Moti kudzera mu ndalama yomwe timatolera takwanitsa kumanga malo osungira njinga zomwe zimabedwa chifukwa chosowa oyang’anira.

Pano munthu akabwera ndi njinga amasungitsa ndi kulipira K100, ndalama yomwe imathandiza kumulipira mlonda,” anatero a Major.

Iwo anati zonsezi zikutheka chifukwa cha maphunziro omwe bungwe la NICE limawapatsa ndikuwazindikiritsa anthu kufunika kotengapo mbali pa chitukuko chaku dela.

“Kuno amayi ndi abuthu amayenda mtunda wautali kupita ku chipatala zomwe zimachititsa imfa zodza kaamba ka uchembere kuchuluka. Komanso anthuwa amayenda mtunda wautali kukafuna madzi oti azigwiritsa ntchito pa chipatala. Ngati satunga madzi nthawi imeneyo ndiye kuti achipatala sagwiranso ntchito.

Pulojekitiyi ikutipatsa mwayi otikumbira mijigo m’madera omwe kulibe ndi cholinga choti anthu azi-mwa madzi aukhondo osati m’mitsinje. Pulojekitiyi yalimbikitsa amayi ndi abuthu kutenga nawo mbali pa nkhani ya uchembere wabwino,” anatero a Major.

Mayi Sakina Kapitawo, m’che-mwali wawo anamulipitsa K3,000 chifukwa choberekera mwana mkolido ya kuchipatala cha Ntaja.

“Ng’ono wanga chaka chatha mwezi wa Okotobala anachedwa kupita ku chipatala. Tinanyamuka kupita ku chiptala cha Ntaja ndipo tikungofika mwana kumabadwa. Anamwino anati asanamuthandize alipire kaye K3,000 ngati chindapusa chomwe munthu wina aliyense amapereka posatengera kuti ndi ndani,” anatero a Kapitawo.

Iwo anati izi zinawaphunzitsa kuti kunyalanyaza kupita kuchipatala munthawi yake maka amayi oyembekezera sibwino chifukwa akanatha kufera pakhomo kapena munjira.

Ngakhale pulojetiyi ikulimbikitsa anthu kubadwitsa cha moyo kwa abuthu komanso amayi mdelari ikuyenda bwino palinso zotsamwitsa zina zomwe anthuwa akukumana nazo pogwira ntchitoyi.

A William Yufusu, m’modzi mwa akomiti yoyang’anira za umoyo mu pulojekitiyi mderali anati anthu ena sakumvetsa zomwe pulojekitiyi ikufuna.

Major: Pulojekiti yatitsegula maso maka pa nkhani ya zaumoyo

“Pali anthu ena omwe kumvetsa zinthu zimawavuta; ambiri akumawona ngati ndi nkhanza zomwe tikuchita kuyiwala kuti tikuwaunikira bwino pa umoyo wawo komanso kufuna kuchepetsa kufala kwa matenda otsegula mmimba monga Kolera, omwe amavuta kwambiri kuno maka nyengo ya mvula,” anatero a Yusufu.

Iwo anati ngakhale izi zili chonchi akomiti omwe akugwira ntchitoyi sakutopa koma kuwayendera omwe asakumvetsa kuti pulojekitiyi ikuchita chani khomo ndi khomo ndi kuwazindikiritsa kufunika kotenga nawo mbali pa nkhani yobadwitsa chamoyo ndi ukhondo pa banja pawo.

Bungwe la NICE Trust likugwira ntchitoyi ndi thandizo lochokera m’dziko la Scotland kudzera ku Water Aid komanso Amref, yomwe ikulimbikitsa ntchito zaumoyo kwa mfumu Kawinga zipatala za Nanyumbu, Ntaja, Chikwewo ndi Nyambi – polimbikitsa zipatalazi kukhala za ukhondo ndi zipangizo zokwanira.

Komanso anthu a m’maderawa akutenga nawo mbali pa zochitika za pachipatala kuti akamakabadwitsa chamoyo asakakumane ndi zokhoma. Izi zikuthandiza kuchepetsa imfa za amayi oyembekezera ndi ana.