General

Nankhumwa ayambitsa chipani chake?

  • Kudzakhala kovuta kuvotera chipani chatsopano – Bamusi 
  • Ndikalankhula dziko lino ligwedezeka – Nankhumwa

Wolemba: Joseph KAYIRA

Pamene chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) chalengeza kuti chachotsa yemwe anali wachiwiri wakale wa pulezidenti wa m’chigawo cha kum’mwera m’chipanichi komanso phungu wa Dera Lapakati m’boma la Mulanje, a Kondwani Nankhumwa, pali manong’onong’o woti mkuluyu akhoza kuyambitsa chipani chake. Koma kufika pano a Nankhumwa sanabenthule ngati ali ndi malingariro oyambitsa chipani chawo.

A Nankhumwa, omwenso ndi mtsogoleri wa zipani zotsutsa ku Nyumba ya Malamulo ati ngakhale awachotsa mu DPP, maganizo awo oti nkhope ndi dzina lawo zidzakhale pa baloti alipobe. Iwo akuti alibe malingaliro olowera ku Malawi Congress Party (MCP) kapena UTM Party monga m’mene anthu ena akunenera.

Nankhumwa: Akufuna kudzapikisana nawo pa mpando wa pulzidenti (Chithunzi: Internet)

Pothirirapo ndemanga pa manong’onong’o amene akumveka a Nankhumwa anati alankhula posachedwapa maganizo awo.

Iwo anauza anthu aku Malabada mu mzinda wa Blantyre, Lamulungu pa 28 Januwale 2024 kuti alankhula posachedwa kumtundu wa Amalawi “ndipo ndikalankhula dziko lino ligwedezeka.”

“Koma zomandiika mawu mkamwa kuti akupita ku Kongeresi [MCP]; akuti akupita ku UTM, akuti akupanga zakuti ayi. Chomwe andichotsera ndichakuti ndimafuna ndikapikisane nawo ku konvenshoni ya DPP kuti chaka cha mawa ndizapikisane nawo pampando wa upulezidenti wa dziko lino.

“Ndiye ndinene chonchi; ndikukusimikizirani abale anga akuno ku Malabada, maloto amene ndinali nawo odzapikisana nawo pampando wa upulezidenti chaka mawa sanafe. Ndipo ndikusimikizireni kuti chaka cha mawa mundiona pa baloti pepala,” anatero a Nankhumwa.

A DPP anasankha a Navicha kukhala mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma (Chithunzi Internet)

Koma akatswiri pa ndale ati ngati a Nankhumwa akana zoti akulowa zipani zomwe zilipo kalezi manong’onong’o oti akufuna kukhazikitsa chipani atha kukhala owona. Pakali pano nkhaniyi yabwereranso ku khoti kutanthauza kuti a Nankhumwa adakali mu DPP momwemo ndipo ku Nyumba ya Malamulo akuwatenga ngati mtsogoleri wa zipani zotsutsa.

A Mary Navicha, omwe ndi phungu wadera la Thyolo Thava, anasankhidwanso mu Nyumbayo ngati mtsogoleri wa zipani zotsutsa lingaliro la DPP losankha a George Chaponda omwe ndi phungu wadera la Kum’mwera cha Kum’mawa kwa boma la Mulanje, kukhala mtsogoleri wa mbali yotsutsa litaomba khoma.

Koma a Mavuto Bamusi, omwe amalankhulapo pankhani zosiyanasiyana, kuphatikizapo za ndale komanso zachuma, ati ngati a Nankhumwa angayambitse chipani chatsopano kudzakhala kovuta kuti anthu ambiri awavotere pa chisankho cha mu 2025 mpaka kutenga upulezidenti wa dziko.

Iwo afotokoza kuti a Nankhumwa ali ndi ufulu woyambitsa chipani chawo chifukwa malamulo a dziko lino akuwalola kutero. Ntchito idzakhala pa kampeni yokopa anthu kuti agwire mfundo zimene a Nankhumwa angabweretse, atero a Bamusi.

A Bamusi akuti m’mbuyomu atsogoleri ena anayambitsapo zipani zawo atasemphana maganizo ndi atsogoleri a mzipani zomwe anali koma pa chisankho sizinawayendere monga m’mene iwo amaganizira.

A Chaponda (kumanzere) atasankhidwa kukhala mtsogoleri wa mbali yotsutsa zawo sizinayende (Chithunzi: Internet)

“Ndikupatsani chitsanzo cha a Brown Mpinganjira amene anayambitsa chipani cha National Democratic Alliance (NDA) ndipo anatchuka ndi chipani chawochi kwambiri. Koma pa chisankho zinthu zinasokonekera. Enanso ndi a Saulos Chilima omwe anatsogolera UTM Party. Nawonso paokha sizinayende. Amalawi amakakamira zipani zawo zomwe akhala nazo ndipo akudzidziwa bwino,” anatero a Bamusi.

Mkuluyu anati kutakhala kuti a Nankhumwa achita chiganizo chozaima paokha ngati kandideti woima paokha pa chisankho cha pulezidenti, kudzakhalabe kovuta kuti anthu awatsatire kaamba koti ndale za ku Malawi kufikira lero ndi zoyendetsedwa kwambiri ndi zipani.

“Mukakumbuka bwino muona kuti a [Justine] Malewezi anayeserapo kuima paokha koma sizinaphule kanthu. Mpaka pano ndale za ku Malawi ndizoyendetsedwa ndi zipani. Komanso ndi kubwera kwa lamulo la 50+1, muzaona kuti ndi zipani za ndale zomwe zingachite bwino zikagwirizana – maka pakakhala chisankho chachibwereza,” anatero a Bamusi.

Mkuluyu anati a Nankhumwa akuyenera kubwera ndi mfundo zozama ndi kukhwima pa ndale komanso pa chitukuko kuti anthu adzawavotere kaamba koti Amalawi ali pamoto ndipo akufuna mtsogoleri yemwe angawaphule pa mavuto omwe akumana nawo mu ulamuliro ulipowu.

“Amalawi pano atseguka maso ndipo akufuna mtsogoleri amene ali ndi kuthekera kowasintha kuchoka mu umphawi kufika mu ulemero. Kodi a Nankhumwa adzachita chani pachuma? Nanga pa maphunziro abwera ndi mfundo zanji? Nanga pa zaumoyo abweretsa zachilendo zotani? Kodi adzaimira Amalawi ngakhale mu nyengo zovuta?” anatero a Bamusi.

Bamusi: A Nankhumwa adekhe (Chithunzi: Internet)

Iwo ati njira ina yabwino kwa a Nankhumwa inali yodekha ndikukhalabe mu DPP kuti adzatenge utsogoleri wake m’tsogolo muno pa nthawi yoikika.

“Ndipo akanapanga izi nthawi imene zinthu zinali zisanafike poipa. Koma chinavuta kwambiri ndi kutengerana ku khoti pa nkhani ina iliyonse. Nkhani zina zija akanatha kukambirana levulo ya chipani. Zimatheka kudzudzulana nkhani nkutha chipani nkumayendanso bwinobwino. Koma zinafika poti makhoti ndi amene amayendetsa chipani zomwe ndizolakwika. Panalibe kulolerana; m’chipani mumafunika kusunga mwambo kuti zinthu zilongosoke,” anatero a Bamusi.

Masiku apitawa a Shadric Namalomba omwe m’neneri wa pulezidenti wa DPP a Peter Mutharika anati chipanichi chiyamba kupeza anthu owaika m’maudindo a anthu omwe anachotsedwa kuphatikizapo a Nankhumwa. Ena ndi phungu wadera la Zomba Chisi, a Mark Botomani, a Grezelder Jeffrey omwe anali mlembi wamkulu wa chipanichi, a Nicholas Dausi omwe anali mneneri wa chipanichi, a Cecelia Chazama omwe anali mlembi wa amayi, a Joe Nyirongo ndi a Ken Msonda.