IMFA YA LULE: MHRC ikudikirabe apolisi alankhulepo
Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA ndi Bartholomew BOAZ
Bungwe la Malawi Human Rights Commission (MHRC) lati likudikirabe apolisi kuti amange apolisi asanu ndi anayi (9) amene adatchulidwa kuti adatengapo mbali pa imfa ya a Buleya Lule, koma apolisi ati zotsatira za kafukufuku wa nkhaniyi adazitumiza kale ku ofesi ya mkulu woona za milandu.
A Lule adafera m’manja mwa apolisi atangoonekera ku bwalo la milandu ku Lilongwe. Iwo adamangidwa ndi apolisi mu Febuluwale chaka chino powaganizira kuti adali mmodzi mwa anthu amene adasowetsa mnyamata wa chialubino Goodson Fanizo kwa Mfumu Yayikulu Chilikumwendo m’boma la Dedza.
Madotolo atapima thupi la a Lule adapeza kuti mkuluyu adafa chifukwa chootchedwa ndi nyetsi ya magetsi. Koma chodabwitsa chidali choti atamwalira mkuluyu, apolisi sadauze msanga achibale ake ndipo adadikira kuti padutse tsiku limodzi.
Bungwe la MHRC lidachita kafukufuku wa nkhaniyi ndipo mu lipoti lomwe lidatulutsa mu Meyi chaka chino lidapempha mkulu wa apolisi kuti afufuze apolisi amene adamanga a Lule; amene adawasunga ndi kumawafunsa mafunso; ndiponso kuti adali m’manja mwa yani kufikira pomwe adamwalira, kuti adziwe kuti adatengapo mbali yotani.
Ena mwa apolisi amene adatchulidwa mu lipotili adali wogwirizira udindo wa Komishonala a Evalista Chisale – amene ndi mkazi wa mtetezi wa mtsogoleri wa dziko lino a Norman Chisale, mkulu wa chigawo chapakati Insipekitala Ronex Kapesa ndi Insipekitala Mervin Gama.
Bungwe la MHRC lidapereka kuti malire pa 5 Ogasiti chaka chino kuti kafukufukuyu akhale atachitika ndipo apolisiwa amangidwe akapezeka olakwa. Koma ngakhale padutsa miyezi iwiri palibe chimene chachitika.
Mkulu wolankhulira bungwe la MHRC a David Nungu anati kumbali yao ayesetsa koma pakali pano “mpira uli m’manja mwa apolisi kuti aliuze dziko kuti nkhaniyi ili pati.”
“[Apolisi] Akuyenera kutiuza kuti amene adatchulidwawo apanga nawo chiyani? Tikudikira kuti anthu amene adatchulidwa aja amangidwe. Tikufuna kuti chilungamo chiyende ngati madzi chifukwa adaphwanya ufulu wa munthu wokhala ndi moyo,” anatero a Nungu.
Koma mneneri wa apolisi a James Kadzadzera wati kafukufuku wokhudza apolisi amene ada-tchulidwa kuti akukhudzidwa ndi imfa ya a Lule adachitika ndi zotsatira zake zinakaperekedwa kwa mkulu woona za milandu (Director of Public Prosecutions).
“Mkulu woona milandu ndi yemwe ali ndi yankho la mmene nkhaniyi itakhalire ndipo akanena zonse zotsatira mtundu wa Malawi udzauzidwa choona. Iyi ndi nthawi yomwe chilungamo chitadzadziwike. Padakali pano zonse zokhudza nkhaniyi zidatha ndipo nafe tikudikira omwe adalandira mafailo okhudza nkhaniyi kuti apange chiganizo, ” anatero a Kadadzera.
Mkwaso unalephera kulankhula ndi mkulu woona milandu a Mary Kachale chifukwa lamya yao ya m’manja imangoitana.
Koma a Kadadzera apempha Amalawi kuti asatope kudikira chifukwa ati nkhani zofufuza zimatenga nthawi kuti azimalize.