MkwasoUncategorized

NICE ilalika za mtendere

Chinkhuntha: Tisadzamenyane zotsatira zaku khoti zikadzawulutsidwa

Wolemba: Rose Chipumphula CHALIRA

Bungwe lophunzitsa anthu zinthu zosiyanasiyana la National Initiative and Civic Education (NICE) Trust lapempha anthu m’dziko muno kuti asunge bata ndi mte-ndere pamene akudikira zotsatira za mlandu wa chisankho ndipo kuti zikadzaulu-tsidwa pasadzakhale ziwawa.

Mkulu woona ntchito za bungweli a Enock Chinkuntha amalankhula izi m’boma la Balaka komwe bungweli limazindikiritsa anthu am’derali mmene nthambi za boma zimayenera kugwirira ntchito zake komanso thandizo lomwe anthu amayenera kupeza pa zipatala zomwe zili m’dera lawo.

Iwo anati mmene nkhani ili ku khothi anthu otsatira zipani  zosiyanasiyana apewe ziwawa komanso kuchita chisokonezo mlanduwu ukatha.

“Tikudziwa tonse kuti nkhani yokhudza chisankho ili ku khothi ndipo nkhaniyi akapereka chigamulo ena chidzawakomera [ndipo] ena ayi. Chonde tiyeni tidzapewe mchitidwe womwe udzadzetse ziwawa koma kuvomereza zomwe zabwera posatengera chipani   chomwe tili ndi kuti chitukuko  chipitirire kuyenda bwino m’dziko muno,” anatero a Chinkuntha.

A Chinkuntha anati nkhaniyi ikatha pakuyenera kukhala bata      komanso onse osangalala asadzasa-ngalale mopyola muyezo kuti ena adzamve kuwawa ndi kuyambitsa ziwawa.

“Mudzasangalale mosaphera ena ufulu, ndipo omwe sizidzawakomera asadzawonetse mkwiyo wawo pobwezera ndi ziwawa,” anatero a Chinkuntha.